Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Akafa Amapita Kudziko la Mizimu?

Kodi Anthu Akafa Amapita Kudziko la Mizimu?

Anthu ambiri amaganiza kuti munthu akamwalira amapita kumwamba kapena kumidima, koma zimenezi si zoona. Tikutero chifukwa cha zimene Baibulo limanena. Yehova Mulungu ndi amene analenga anthu ndipo amadziwa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira.​—Salimo 83:18; 2 Timoteyo 3:16.

Adamu anapangidwa kuchokera ku fumbi, ndipo atafa anabwereranso ku fumbi

Baibulo limanena kuti Mulungu analenga Adamu “kuchokera kufumbi” n’kumuika m’munda wa Edeni. (Genesis 2:7) Ngati Adamu akanamvera lamulo limene Yehova anamupatsa, sakanafa. Koma sanamvere ndipo Mulungu anati: ‘Udzabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.’​—Genesis 3:19.

Kodi Adamu asanalengedwe kuchokera kufumbi, anali kuti? Iye kunalibeko komanso sanali mzimu kumwamba. Choncho pamene Yehova ankamuuza kuti “udzabwerera kunthaka,” ankatanthauza kuti adzafa. Iye atafa sanapite kudziko la mizimu ndipo sanakhalenso ndi moyo kwinakwake.

Kodi anthu ena amene anamwalira, nawonso kulibe? Baibulo limayankha kuti:

  • “Zonse [anthu komanso nyama] zimapita kumalo amodzi. Zonse zinachokera kufumbi ndipo zonse zimabwerera kufumbi.”​—Mlaliki 3:20.

  • “Akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlaliki 9:5.

  • “Chikondi chawo, chidani chawo ndiponso nsanje yawo zatha kale.”​—Mlaliki 9:6.

  • “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”​—Mlaliki 9:10.

  • “Iye amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.”​—Salimo 146:4.

Amoyo ndi amene angagwire ntchito izi

Kuti mumvetse bwino malembawa, taganizirani izi: M’mabanja ambiri bambo ndi amene amapeza ndalama kuti asamalire banja lake ndipo akamwalira banjalo limavutika kwambiri. Nthawi zina mkazi ndi ana ake amasowa chakudya. Mwinanso amazunzidwa ndi adani a bamboyo. Ndiyeno tingafunse kuti: ‘Ngati bamboyo ali ndi moyo kudziko la mizimu, n’chifukwa chiyani sapitiriza kusamalira banja lake? N’chifukwa chiyani sateteza banja lake kwa adani ake?’ Zonsezi ndi umboni wakuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. Bamboyo salinso moyo ndipo sangachite chilichonse.​—Salimo 115:17.

Akufa sangatipatse chakudya kapena kutiteteza

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu amene anamwalira sadzakhalanso ndi moyo? Ayi. M’mutu wina kutsogoloku tidzakambirana zoti akufa adzauka. Koma panopa anthu akufa sadziwa chilichonse. Iwo sangathe kutiona, kutimva kapena kutiyankhula. Sitiyenera kuwadalira kapena kuwaopa.​—Mlaliki 9:4; Yesaya 26:14.