Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

Dzikoli Lidzakhala Paradaiso

Yehova adzathetsa mavuto onse amene Satana anayambitsa ndipo anasankha Yesu kuti akhale Mfumu ya dziko lonse. Yesu akadzayamba kulamulira dzikoli, lidzakhala paradaiso.​—Danieli 7:13, 14; Luka 23:43.

Yehova anatilonjeza zinthu zotsatirazi:

  • PADZAKHALA CHAKUDYA CHAMBIRI: “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.” “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 67:6; 72:16.

  • SIPADZAKHALANSO NKHONDO: “Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova, onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi. Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Salimo 46:8, 9.

  • SIPADZAKHALANSO ANTHU OIPA: “Pakuti ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi. Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.”​—Salimo 37:9, 10.

  • SIPADZAKHALANSO MATENDA, KUVUTIKA KOMANSO IMFA: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”​—Yesaya 35:5, 6.

    “Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova amanena zoona zokhazokha koma Satana ndi ziwanda ndi abodza. Yehova amachita chilichonse chimene walonjeza. (Luka 1:36, 37) Iye amakukondani ndipo akufuna kuti mudzakhale m’Paradaiso. A Mboni za Yehova angakuthandizeni kudziwa zinthu zabwino zimene zili m’Mawu a Mulungu. Mukamatsatira mfundo za m’Baibulo simudzanamizidwa, simudzaopa mizimu ndipo mudzakhala ozindikira. M’tsogolomu, tonse sitidzakhalanso akapolo a uchimo ndi imfa. Paja Yesu ananena kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.