Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

ADAUDA omwe amakhala ku Sierra Leone, anati: “Ndinakulira m’mudzi wina kumpoto kwa dziko la Sierra Leone. Ndili mnyamata, banja lathu linkalimbirana munda ndi banja lina. Pofuna kuthetsa nkhaniyi, anaitana sing’anga. Sing’angayo atabwera, anapatsa bambo wina galasi ndipo kenako anamufunditsa kumutu nsalu yoyera. Pasanapite nthawi, bambo uja anayamba kunjenjemera komanso kutuluka thukuta. Atayang’anitsitsa pagalasi lija anati: ‘Ndikuona munthu wamwamuna wokalamba, akubwera. Wavala zovala zoyera, ndi wamtali, ali ndi imvi ndipo akuyenda chowerama.’”

A Dauda anapitiriza kuti: “Zimene bamboyo ananena, zinali zogwirizana ndi mmene agogo anga ankaonekera. Kenako anafuula mwamantha kuti: ‘Ngati simukukhulupirira zomwe ndikunenazi, bwerani mudzaone nokha.’ Koma palibe amene analimba mtima kuti akaone pagalasipo. Kenako sing’anga uja anawaza bamboyo mankhwala omwe anali munsupa pofuna kumukhazika mtima pansi.”

A Dauda anatinso: “Kenako munthu amene ankaoneka pagalasi uja ananena kuti mundawo ndi wa banja lathu. Ananena kuti agogo aakazi azilima mundawo ndipo asade nkhawa ndi chilichonse. Banja lina lija silinachitenso makani, linangovomereza zomwe agogowo ananena ndipo mkanganowo unathera pomwepo.”

Zinthu ngati zimenezi zimachitika m’mayiko ambiri padziko lonse. Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umapita kumwamba kapena kumidima. Amakhulupiriranso kuti mzimuwo umaona zonse zomwe zikuchitika komanso ukhoza kuthandiza kapena kuchitira zoipa anthu. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Kodi anthu amene anamwalira amakhalanso ndi moyo kwinakwake? Ngati yankho ndi loti ayi, nanga ndani amene amayerekezera kuti ndi mizimu ya anthu omwe anamwalira? Kudziwa mayankho olondola a mafunsowa, kungatithandize kuti tidzapeze moyo kapena ayi.