Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzitumikira Yehova Osati Satana

Muzitumikira Yehova Osati Satana

Aliyense ali ndi ufulu wosankha yekha kuti azitumikira Yehova kapena Satana ndi ziwanda zake. Koma sitingatumikire onsewa nthawi imodzi, choncho ndi bwino kuyesetsa kuti tizitumikira Yehova.

Yehova Ndi Wabwino

Monga taona kale, ziwanda zimasangalala zikamazunza komanso kunamiza anthu. Koma Yehova amatikonda ngati mmene bambo amakondera ana ake. Iye amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yakobo 1:17) Mulungu amalolera kutipatsa zilizonse zabwino ngakhale zitaoneka ngati zovuta kwambiri.​—Aefeso 2:4-7.

Yesu Khristu, yemwe anali mwana wa Mulungu anasonyeza kuti ankakonda anthu pochiritsa odwala

Taganizirani zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Iye anathandiza anthu osalankhula kuti azilankhula ndiponso osaona kuti aziona. Anachiritsa matenda amtundu uliwonse komanso anatulutsa ziwanda. Yesu anaukitsa anthu akufa. Anachita zonsezi ndi mphamvu ya Mulungu.​—Mateyu 9:32-35; 15:30, 31; Luka 7:11-15.

Mulungu amatiuza zoona zokhazokha. Iye satiuza zinthu zabodza n’cholinga choti atisocheretse.—Numeri 23:19.

Pewani Zizolowezi Zoipa

Anthu ambiri sachedwa kukhulupirira zinthu zabodza komanso zamatsenga. Iwo amaopa anthu akufa ndiponso ziwanda. Amakhulupirira zinthu monga matsenga, malodza ndiponso zithumwa. Apa tingati amakhala ndi mantha chifukwa cha mabodza a Satana Mdyerekezi. Koma atumiki a Yehova saopa zimenezi.

Yehova ndi wamphamvu kuposa Satana ndipo amateteza anthu ake kuti asavulazidwe ndi ziwanda komanso asalodzedwe. (Yakobo 4:7) Mwachitsanzo, asing’anga atatu ku Nigeria anaopseza kuti alodza wa Mboni wina ngati sachoka m’tauni imene ankakhala. Atalephera kumulodza, sing’anga wina anaopa kwambiri ndipo anapita kwa wa Mboniyo kukapempha kuti amukhululukire.

Anthu a ku Efeso anawotcha mabuku awo a zamatsenga

Ziwanda zikamakuvutitsani muyenera kuitana Yehova ndipo adzakutetezani. (Miyambo 18:10) Koma kuti Yehovayo akutetezeni, muyenera kusiyiratu kuchita chilichonse chokhudzana ndi ziwanda. Izi n’zimene atumiki a Yehova a ku Efeso anachita. Iwo anatolera mabuku onse a zamatsenga n’kuwaotcha. (Machitidwe 19:19, 20) Choncho atumiki a Yehova masiku ano ayenera kutayanso zinthu monga zithumwa, mphinjiri, mabuku a zamatsenga komanso chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.

Muzilambira Mulungu Woona

Komabe kusiya kukhulupirira zinthu zabodza komanso kuchita zoipa si kokwanira. Kuti musangalatse Mulungu, muyenera kuyesetsa kuti muzimulambira m’njira yoyenera. Baibulo limasonyeza mmene tingachitire zimenezi.

Kusonkhana.—Aheberi 10:24, 25

Kuphunzira Baibulo.—Yohane 17:3

Kulalikira.—Mateyu 24:14

Kupemphera kwa Yehova.—Afilipi 4:6, 7

Kubatizidwa.—Machitidwe 2:41

Muzisonkhana ndi a Mboni za Yehova

Satana ndi ziwanda zake ali ndi anthu amene amaphunzitsa zabodza komanso kuchita zinthu zoipa. Nayenso Yehova ali ndi gulu lake lomwe ndi la Mboni za Yehova limene limaphunzitsa zoona. (Yesaya 43:10) Padziko lonse pali a Mboni ambirimbiri ndipo amayesetsa kuchita zabwino komanso kuphunzitsa anthu zinthu zoona. M’mayiko ambiri, amasonkhana ku Nyumba za Ufumu ndipo akakulandirani bwino.

Iwo amagwira ntchito yothandiza anthu kuti azitumikira Mulungu. Inunso adzakuthandizani kuti muziphunzira Baibulo kunyumba kwanu komanso kuti muzilambira Yehova m’njira yoyenera. Sadzakulipiritsani chilichonse. Iwo amakonda anthu ndipo amasangalala kuphunzitsa anthu mfundo zoona n’cholinga choti nawonso azikonda Yehova Mulungu.

A Mboni za Yehova angakuthandizeni kuti muzitumikira Mulungu