Yehova Analenga Angelo Ambirimbiri
Baibulo limanena kuti Yehova ndi mzimu. Iye analenganso angelo ambirimbiri omwe ali ndi matupi auzimu.—Yohane 4:24; 2 Akorinto 3:17, 18.
Poyambirira, Yehova analipo yekha. Kenako anayamba kulenga angelo omwe ndi amphamvu komanso anzeru kuposa anthufe. Angelowa alipo ambirimbiri ndipo Danieli anaona m’masomphenya angelo okwana 100 miliyoni.—Danieli 7:10; Aheberi 1:7.
Angelowa analengedwa dziko lapansili lisanalengedwe. (Yobu 38:4-7) Iwowa si anthu amene anamwalira padzikoli n’kupita kumwamba.
Yehova analenga angelo ambirimbiri