Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziwanda Zimafuna Kuti Tisamamvere Mulungu

Ziwanda Zimafuna Kuti Tisamamvere Mulungu

Miyambo ina imachokera pa bodza lakuti akufa amationa

Satana ndi ziwanda zake amayesetsa kutisocheretsa kuti nafenso tisamamvere Mulungu. Amafuna kuti tiziwalambira, tizikhulupirira mabodza awo komanso tizichita zimene Mulungu amadana nazo. Zinthu zina zimene amafuna kuti tizichita n’zokhudza akufa.

Munthu amene timamukonda akamwalira, zimatipweteka ndipo timamva chisoni. Yesu atamva kuti Lazaro wamwalira “anagwetsa misozi.”​—Yohane 11:35.

Anthu ambiri padzikoli amakhulupirira miyambo yosiyanasiyana yokhudza akufa. Miyambo ina siitsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, koma pali ina imene anthu amachita chifukwa chokhulupirira kuti akufa amakhalabe ndi moyo ndipo amationa. Mwachitsanzo, ena amachezera pamaliro, amalira mopanda chiyembekezo komanso amachita mwambo wa maliro wapamwamba chifukwa choopa kukhumudwitsa mizimu ya akufa. Koma popeza kuti akufa “sadziwa chilichonse,” ndiye kuti amene amakhulupirira zimenezi amatsatira mabodza a Satana.​—Mlaliki 9:5.

Miyambo ina imachokera pa bodza lakuti tingathe kuthandiza anthu amene anamwalira

Anthu amachitanso zinthu zina chifukwa chokhulupirira kuti akufa amafuna thandizo la anthu amoyo ndipo ngati sawathandiza akhoza kuwachitira zoipa. M’mayiko ena amapanga phwando komanso kupereka nsembe pakatha masiku 40 kapena chaka kuchokera pamene munthu wamwalira. Amachita zimenezi kuti athandize wakufayo kupita kudziko la mizimu. Anthu ena amapereka chakudya kwa akufa.

Zikhulupiriro zonsezi n’zolakwika chifukwa zimathandizira kufalitsa mabodza a Satana. Koma kodi Yehova angavomereze kuti tizikhulupirira zimene ziwanda zimaphunzitsa? Ayi.​—2 Akorinto 6:14-18.

Atumiki a Yehova sachita nawo miyambo imene imathandiza kufalitsa mabodza a Satana. Koma amayesetsa kuthandiza ndiponso kulimbikitsa amene ali moyo. Amadziwa kuti munthu akamwalira ndi Yehova yekha amene akhoza kumuukitsa.​—Yobu 14:14, 15.

Mulungu Amadana ndi Kuchita Zamizimu

Anthu ena amalankhulana ndi ziwanda paokha kapena kudzera kwa asing’anga. Zinthu monga ufiti, matsenga, kulosera za mtsogolo komanso kufunsira kwa akufa zimasonyeza kukhulupirira mizimu.

Mulungu amadana ndi zinthu zimenezi. Amafuna kuti tizilambira iye yekha basi.—Ekisodo 20:5

Baibulo limaletsa zinthu zimenezi ndipo limati: “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.”​—Deuteronomo 18:10-12.

N’chifukwa chiyani Yehova amatiletsa kukhulupirira mizimu?

Yehova amatiletsa zimenezi chifukwa amatikonda. Iye amatidera nkhawa ndipo amadziwa kuti anthu amene amakhulupirira ziwanda amazunzika.

Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Brazil dzina lake Nilda, ankalankhulana ndi ziwanda ndipo zinkamuzunza kwambiri. Iye anati: “Mizimu inandigwira ndipo inkandilamulira. Nthawi zambiri ndinkakomoka ndipo ndinkadwala matenda a maganizo. Ziwandazi zinkandizunza kwambiri mpaka zinachititsa kuti ndizidwaladwala. Kwa zaka zingapo ndinayamba kumwa mankhwala ogonetsa, kusuta komanso kuledzera pafupipafupi kuti ndizipeza mtendere.”

Nthawi zambiri anthu amene amakhulupirira zamizimu amakumana ndi mavuto. Akhoza kutaya nyumba yawo, ufulu wawo komanso ngakhale moyo wawo kumene

Patapita nthawi, Nilda anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova omwe anamuthandiza kuti asiye kulankhulana ndi ziwanda ndipo panopa amakhala mosangalala. Iye ananena kuti: “Ndimalimbikitsa anthu kuti asayerekeze n’komwe kulankhulana kapena kugwirizana ndi ziwanda.”