Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziwanda Zimanama Kuti Akufa Ali Moyo

Ziwanda Zimanama Kuti Akufa Ali Moyo

Baibulo limanena kuti Satana “akusocheretsa dziko lonse lapansi.” (Chivumbulutso 12:9) Iye ndi ziwanda zake safuna kuti tizikhulupirira Baibulo. Amayesetsa kunamiza anthu kuti akufa ali moyo kwinakwake. Tiyeni tione mmene amachitira zimenezi.

Zipembedzo Zonyenga

Anthu, nyama, nsomba ndiponso mbalame zili m’gulu la zamoyo

Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu aliyense ali ndi mzimu ndipo thupi likafa mzimuwo umapita kudziko lamizimu.

Koma izi ndi zosiyana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo silinena kuti munthu amakhala ndi chinachake m’kati mwake chimene chimapita kudziko lamizimu. Mwachitsanzo, pofotokoza zimene Mulungu anachita polenga Adamu, Baibulo limati: ‘Kenako, Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi, ndipo anauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala wamoyo.’​—Genesis 2:7.

Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani yokhudza moyo:

  • “Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.”​—Ezekieli 18:4.

  • “Kodi malamulo amalola kuchita chiti pa sabata? Chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”​—Maliko 3:4.

Tikawerenga Baibulo kuyambira kumayambiriro mpaka kumapeto sitingapeze pamene analemba kuti moyo suufa. Amene amaphunzitsa nkhani zimenezi ndi Satana ndi ziwanda zake ndipo Yehova amadana ndi mabodza amenewa omwe zipembedzo zambiri zimaphunzitsa.​—Miyambo 6:16-19; 1 Timoteyo 4:1, 2.

Anthu Olankhula ndi Mizimu

Ziwanda zimayerekezera kukhala mizimu ya anthu amene anamwalira

Satana amagwiritsanso ntchito anthu olankhula ndi mizimu. Anthu amenewa amanena kuti amalandira mauthenga ochokera kwa mizimu ya akufa ndipo anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Koma malinga ndi zimene taona m’Baibulo, zimenezi si zoona.​—Mlaliki 9:5, 6, 10.

Ndiyeno, kodi mauthenga amene amalandirawo amachokera kuti? Ziwanda zimaonetsetsa munthu pa nthawi imene ali moyo n’kudziwa maonekedwe ake, kalankhulidwe kake, zimene akuchita komanso zimene akudziwa. Ndiyeno munthuyo akamwalira, zimayerekezera zimene ankachita komanso mmene ankalankhulira n’kumapereka mauthenga kwa anthu.​—1 Samueli 28:3-19.

Nkhani Zabodza

Satana amafalitsanso nkhani zabodza zokhudza anthu akufa. Nkhanizi zimachititsa anthu kuti asamakhulupirire mfundo zoona za m’Baibulo.​—2 Timoteyo 4:4.

Anthu ena amaganiza kuti aona anthu amene anamwalira alinso ndi moyo

Mu Africa muli nkhani zambirimbiri zofotokoza za anthu amene anaonekanso pambuyo poti amwalira. Anthuwo amakapezeka kutali ndi kumene ankakhala ali moyo. Koma funso n’kumati: ‘Kodi zimenezi zikanakhala zoona, munthu woukayo akanapita dala kutali kopanda achibale ake komanso anzake?’

N’kutheka kuti anthu amangoona munthu wofanana ndi amene anamwalirayo. Mwachitsanzo, m’dziko lina bambo wina wachikulire ankangolondola Akhristu awiri amene ankalalikira. Bamboyo atafunsidwa, ananena kuti ankaganiza kuti m’modzi mwa Akhristuwo ndi mchimwene wake amene anamwalira zaka zingapo m’mbuyomo. Bamboyo anakakamira kwambiri m’baleyo n’kumanena kuti ndi mchimwene wake basi. Ndiye kodi mukuganiza kuti bamboyo atafika kwawo anakanena zotani kwa anzake?

Zinthu Zimene Anthu Amaona, Kulota Kapena Kumva

Ziwanda zimachititsa anthu kuona, kulota kapena kumva mawu a munthu wina

Mwina inu munamvapo anthu ena akunena kuti anaona, kumva kapena kulota zinthu zachilendo ndipo amachita mantha. Chitsanzo ndi mayi wina wa ku West Africa, dzina lake Marein. Nthawi zambiri ankamva mawu a agogo ake omwe anamwalira akumuitana usiku. Chifukwa cha mantha, iye ankafuula kwambiri mpaka kudzutsa anthu onse m’nyumba. Patapita nthawi anachita misala.

Koma kodi akufa akanakhala kuti ali ndi moyo kwinakwake, bwenzi akungokhalira kuopseza achibale awo chonchi? Ayi. Ziwanda n’zimene zimachita zonsezi.

Nanga bwanji za mauthenga amene amaoneka ngati othandiza kapena olimbikitsa? Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Gbassay wa ku Sierra Leone atadwala, analota bambo ake amene anamwalira. Iwo anamuuza kuti akathyole masamba a mtengo winawake, asakanize ndi madzi n’kumwa ndipo achite zimenezi asanalankhule ndi aliyense. Atapanga izi anachiradi.

Mayi wina ananena kuti patangopita tsiku limodzi mwamuna wake atamwalira, anadzamuonanso. Mwamunayo ankaoneka bwino komanso anali atatchena.

Mauthenga komanso maloto ngati amenewa amaoneka ngati olimbikitsa ndiponso othandiza. Koma kodi ndi ochokeradi kwa Mulungu? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova ndi “Mulungu wachoonadi.” (Salimo 31:5) Iye sangatinamize kapena kutipusitsa koma ziwanda ndi zomwe zimachita zimenezi.

Nanga kodi pali ziwanda zabwino? Ayi. Ngakhale kuti nthawi zina zingaoneke ngati n’zothandiza, ziwanda zonse ndi zoipa. Pamene Satana ankalankhula ndi Hava ankaoneka ngati wabwino. (Genesis 3:1) Koma Hava atamumvera anafa.

Satana anauza Hava kuti sadzafa. Hava anamvera zimenezi koma patapita nthawi anafa

Nthawi zambiri munthu woipa akafuna kunamiza komanso kupusitsa ena, amaoneka ngati wabwino. Izi zikugwirizana ndi mwambi uja wakuti, “Chikomekome cha nkhuyu mkati muli nyerere.” Baibulo limati: “Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.”​—2 Akorinto 11:14.

Masiku ano Mulungu salankhulanso ndi anthu kudzera m’maloto kapena masomphenya. Iye amatitsogolera ndiponso kutilangiza kudzera m’Baibulo ndipo limathandiza munthu kukhala “wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 Timoteyo 3:17.

Yehova amatikonda ndipo amatichenjeza za kuopsa kwa misampha ya Mdyerekezi. Iye amadziwa kuti ziwanda ndi zoopsa.