Ziwanda Zimapha
Satana ndi ziwanda ndi ankhanza ndiponso oopsa. M’mbuyomu, Satana anapha ziweto komanso antchito a Yobu. Kenako anayambitsa “chimphepo” chimene chinagwetsa nyumba n’kupha ana 10 a Yobu. Pomaliza anamudwalitsa “zilonda zopweteka, kuyambira kuphazi mpaka kumutu.”—Yobu 1:7-19; 2:7.
M’nthawi ya Yesu ziwanda zinkachititsa anthu kuti akhale akhungu komanso osalankhula. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Zinazunzanso munthu wina moti ankadzitematema ndi miyala. (Maliko 5:5) Zinachititsanso mnyamata wina kugwa pansi n’kumachita ngati akuphupha.—Luka 9:42.
Masiku anonso Satana ndi ziwanda zake amapha anthu.
Kuyambira pamene anagwetsedwa kuchokera kumwamba, akuzunza kwambiri anthu ndipo umboni wake ulipo padziko lonse. Mwachitsanzo, ziwanda zimadwalitsa anthu, kuwalepheretsa kugona chifukwa cha mantha, kuwalotetsa zoopsa ndipo ena zimawagwirira. Anthu ena zimawachititsa misala pomwe ena zimawachititsa kudzipha kapena kupha anthu ena.Mayi wina wa ku Suriname dzina lake Lintina, ananena kuti chiwanda chinapha abale ake okwana 16 ndipo chinamuzunza kwa zaka 18. Iye anazindikira kuti ziwanda zimasangalala zikamazunza anthu mpaka kufika powapha.
Koma Yehova ndi wokonzeka kuteteza atumiki ake.—Miyambo 18:10.