Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 3

Kodi Malangizo Anachokera Kuti?

Kodi Malangizo Anachokera Kuti?

N’chifukwa chiyani mumaoneka mmene mumaonekeramo? N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikhala ndi mtundu winawake wa maso, tsitsi ndi khungu? Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu akhale aatali, aafupi, onenepa kapena ochepa thupi? Nanga n’chiyani chimachititsa kuti muzifanana ndi makolo anu? Kodi n’chifukwa chiyani zala za anthu onse zimakhala ndi zikhadabo mbali imodzi koma mbali inayo minofu?

Mu nthawi ya Charles Darwin, asayansi sankadziwa mayankho a mafunso amenewa. Darwin ankachita chidwi kwambiri ndi zoti ana amatengera makolo awo, koma sankadziwa kwenikweni kuti chimachititsa n’chiyani. Kwa zaka zambiri asayansi akhala akuphunzira zomwe zimachititsa kuti tizitengera makolo athu komanso malangizo amene amakhala mu DNA. Koma funso lofunika n’lakuti, Kodi malangizowo anachokera kuti?

Kodi asayansi ambiri amanena zotani? Asayansi ambiri amaganiza kuti DNA komanso malangizo ake zinakhalako mwangozi chifukwa cha zinthu zimene zinkangochitika zokha kwa zaka mamiliyoni ambiri. Iwo amanena kuti DNA, malangizo ake komanso mmene imagwirira ntchito sizisonyeza kuti zinachita kupangidwa ndi winawake.17

Kodi Baibulo limanena zotani? Baibulo limasonyeza kuti pali chinthu chofanana ndi buku chimene Mulungu anapanga, chomwe muli malangizo okhudza kapangidwe ka ziwalo za thupi lathu komanso nthawi imene zinapangidwa. Mfumu Davide anafotokoza zimenezi m’Baibulo. Iye ananena za Mulungu kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.”​—Sal. 139:16.

Kodi umboni umasonyeza chiyani? Ngati n’zoona kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi, pakufunikanso zifukwa zomveka zosonyeza kuti DNA ikhoza kukhalako mwangozi. Koma ngati Baibulo ndi loona, mmene DNA ilili ziyenera kupereka umboni wosonyeza kuti inapangidwa ndi winawake wanzeru komanso wadongosolo.

Nkhani ya DNA imakhala yochititsa chidwi kwambiri ikafotokozedwa m’njira yosavuta kumva. Choncho tiyeni tilowenso muselo koma ulendo uno tilowe muselo la munthu. Tiyerekeze kuti mukupita kumalo oonetsera zinthu zochititsa chidwi kuti mukaone mmene selo limagwirira ntchito. Malo onsewa apangidwa ngati selo limene lakulitsidwa maulendo pafupifupi 13,000,000 kuti muthe kuliona bwinobwino. Malowa ndi aakulu ngati sitediyamu yokwana anthu pafupifupi 70,000.

Ndiyeno mukulowa m’malo amenewa n’kudabwa kwambiri ndi zinthu zosiyanasiyana zochititsa chidwi zomwe zilimo. Pafupi ndi pakati pa seloli pali nyukiliyasi yomwe ndi yozungulira ngati dzira ndipo ndi yaitali mofanana ndi nyumba ya nsanjika 20. Ndiye mukupita kumeneko.

Zinapangidwa “mwaukatswiri kwambiri”—Kukulungizidwa kwa DNA: DNA imakulungizidwa munyukiliyasi mwaukatswiri kwambiri moti zili ngati kutenga ulusi wautali makilomita 40 n’kuuika m’kampira kosewerera tenesi

Mukulowa pakhomo la khungu la nyukiliyasiyi n’kuyamba kumwazamwaza maso. Mkati mwake muli zinthu zotchedwa makoromosomu zokwana 46. Makoromosomuwa ndi awiriawiri koma peyala iliyonse ndi yosiyana kutalika kwake ndi inzake. Peyala imene ili pafupi ndi inuyo ndi yaitali pafupifupi ngati nyumba ya nsanjika 12 (1). Koromosomu iliyonse ndi yoning’a pakati koma yonenepa ngati tsinde la mtengo waukulu. Ndiyeno mukuona zingwe zosiyanasiyana zomwe zazungulira makoromosomuwa. Mukayandikira mukuona kuti chingwe chilichonse ndi chamizeremizere ndipo pakati pa mizereyo pali mizere ina yaifupi moti zikuoneka ngati timashelufu tokhala ndi mabuku (2). Koma kodi timizereti ndi mabukudi? Ayi. Ndi zingwe zinazake zomwe zakulungizidwa mothinana kwambiri. Kenako mukukoka chingwe chimodzi ndipo chikumasuka. Mukudabwa kuona kuti chingwechi chapangidwa ndi zingwe zina zing’onozing’ono (3), zomwe zakulungizidwanso kwambiri. Mkati mwa zingwe zing’onozing’onozi mukuoneka ngati muli chingwe chinanso chachitali kwambiri. Kodi chingwechi n’chiyani?

MOLEKYU YOGOMETSA KWAMBIRI

Chinthu chooneka ngati chingwechi ndi chonenepa pafupifupi masentimita atatu. Chakulungizidwa mothinana pa zinthu zinazake zooneka ngati zosungirapo ulusi (4). Ndiye pali zinthu zinazake zokhala ngati timitengo zomwe zimathandiza kuti chingwechi chisamasunthe. M’malo oonetsera selowa muli chikwangwani chonena kuti chingwechi chakulungizidwa mothinana komanso mwaluso kwambiri. Mutati muchotse chingwe chomwe chili mukoromosomu iliyonse n’kuchilumikiza ndi zinzake, zingwe zonsezo pamodzi zikhoza kuzungulira hafu ya dziko lapansi. *

Buku lina la sayansi limanena kuti zingwezi zimakulungizidwa munyukiliyasi “mwaukatswiri kwambiri.”18 Ndiye kodi zimene asayansi amanena zoti panalibe amene anachita zimenezi n’zomveka? Tiyerekeze kuti m’malo oonetserawa muli shopu yogulitsiramo zinthu mamiliyoni ambiri ndipo zonse zasanjidwa mwadongosolo kwambiri moti mungapeze mosavuta chilichonse chimene mukufuna. Kodi mungaganize kuti palibe munthu amene anasanja zinthuzo? Ayi. Koma kusanja zinthu chonchi mushopu ndi ntchito yophweka kwambiri poyerekezera ndi mmene zinthu zilili muselo.

Tiyerekeze kuti m’malo oonetserawa muli chikwangwani china chokuuzani kuti mutenge chingwechi kuti muchione bwinobwino (5). Ndiyeno mukachigwira mukuona kuti si chingwe wamba. Koma ndi zingwe ziwiri zimene zapotedwa ndipo pakati pa zingwezi pali zinazake zooneka ngati masitepe. Choncho chingwechi chimaoneka ngati makwerero opotoka (6). Kenako mukuzindikira kuti chingwe chimene mwagwiracho ndi molekyu yodabwitsa kwambiri ya DNA.

Molekyu ya DNA imodzi yokulungizidwa limodzi ndi mbali zake zonse imapanga koromosomu imodzi. Masitepewo amakhala awiriawiri (7). Koma kodi amagwira ntchito yotani? Chikwangwani china cha m’malo oonetserawo chikufotokoza mosavuta ntchito yake.

NJIRA YODABWITSA YOSUNGIRA MALANGIZO

Chikwangwanicho chikunena kuti chinsinsi chomvetsa DNA chimakhala m’masitepewo, amene amalumikiza mbali ziwiri za makwererowo. Koma tayerekezerani kuti makwererowo agawika pakati moti mbali iliyonse ya makwererowo ili ndi mbali imodzi ya masitepewo. Masitepewo alipo a mitundu 4 basi ndipo asayansi amatchula mitunduyo kuti A, T, G ndi C. Asayansiwo anadabwa kutulukira kuti kasanjidwe ka zilembozo n’kamene kamapangitsa kuti zizipereka malangizo.

Mwina mumadziwa za mauthenga otchedwa Morse omwe anatulukiridwa m’ma 1800 ndipo ankatumizidwa pogwiritsa ntchito telegalafu. Potumiza mauthengawo ankangogwiritsa ntchito zizindikiro ziwiri zokha, zomwe zinali timadontho ndi timizere. Komabe pongogwiritsa ntchito zizindikiro ziwirizo, ankatha kutumiza mauthenga okhala ndi mawu ambiri. Koma DNA ili ndi zilembo 4 ndipo kasanjidwe ka zilembozo kamapanga zinthu zokhala ngati mawu. Ndiyeno mawuwo amasanjidwa kuti akhale ngati ndime zimene zimatchedwa majini. Jini iliyonse imakhala ndi zilembo pafupifupi 27,000. Majiniwa ndiponso malo amene amakhala pakati pa majiniwa amasanjidwanso n’kukhala ngati machaputala, omwe amapanga makoromosomu. Makoromosomu okwana 23 amapanga jenomu imodzi, yomwe ili ngati buku lathunthu. Jenomu imeneyi imakhala ndi malangizo onse ofunika kuti chinthu chamoyo chipangike. *

Jenomu ili ngati chibuku chachikulu kwambiri. Kodi mujenomu mungakhale malangizo ochuluka bwanji? Jenomu ya munthu imakhala ndi masitepe pafupifupi 3 biliyoni pamakwerero a DNA.19 Mujenomu imodzi mumakhala malangizo ambiri moti akhoza kudzaza mabuku okwana 428 amasamba oposa 1,000. Choncho majenomu awiri amene ali muselo angadzaze mabuku okwana 856. Mutati mulembe malangizo onse amene amapezeka mujenomu imodzi, zingakutengereni pafupifupi zaka 80 mukulemba maola 8 pa tsiku kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu mlungu uliwonse.

Komatu malangizo amene mungalembewo sangakhale othandiza m’thupi lanu. Tikutero chifukwa malangizowo angagwire ntchito yake pokhapokha ataikidwa mwadongosolo m’maselo onse 100 thiriliyoni a m’thupilo, zomwe ndi zosatheka. Palibe munthu amene angakwanitse kuchita zimenezi.

Pulofesa wa mamolekyu komanso sayansi ya makompyuta ananena kuti: “DNA yokwana galamu imodzi ingasunge malangizo okwana mumadisiki 1 thiriliyoni.”20 Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Paja mu DNA mumakhala majini, omwe ndi malangizo opangira thupi la munthu. Selo lililonse limakhala ndi malangizo onsewa. Ndiye mu DNA mumakhala malangizo ambiri moti DNA yokwana musipuni yaing’ono imodzi ingakhale ndi malangizo okwana kupangira anthu pafupifupi 2.5 thiriliyoni. Ndipotu DNA imene ingafunike kupangira anthu 7 biliyoni omwe ali padzikoli panopa, itati ikhale pasipuni yaing’ono mwina singaoneke n’komwe.21

KODI PANGAKHALE BUKU LOPANDA WOLILEMBA?

DNA yolemera galamu imodzi ingakhale ndi malangizo ofanana ndi amene angakwane mu ma CD okwana 1 thiriliyoni

Masiku ano luso lopanga zinthu lapita patsogolo kwambiri. Komatu palibe munthu amene angapange chipangizo chosunga zinthu zochuluka ngati zimene DNA ingasunge. Disiki ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Timachita chidwi ndi mmene imaonekera, kunyezimira kwake komanso kapangidwe kake. Sitikayikiranso zoti pali anthu anzeru amene anaipanga. Koma tiyerekezere kuti m’disikimo mwaikidwa malangizo opangira mashini ogometsa kwambiri komanso malangizo okonzera mashiniwo akawonongeka. Malangizo ofunika onsewo akwana bwinobwino mudisikiyo popanda kuikulitsa. Kodi malangizo amene ali mudisikiwo sangakupangitseni kukhulupirira kuti pali anthu ena anzeru zogometsa amene anawaikamo? Kodi pangakhale malangizo olembedwa popanda wowalemba?

N’zomveka kuyerekezera DNA ndi disiki kapena buku. Buku lina lonena za majenomu limati: “Sikulakwitsa kunena kuti jenomu ili ngati buku. Ndipotu ndi bukudi chifukwa mofanana ndi buku, . . . mujenomu mumakhala malangizo amene angawerengedwe. Koma jenomu ndi buku logometsa chifukwa imatha kudzikopera yokha komanso kudziwerenga.””22 Imeneyi ndi mbali ina yogometsa ya DNA.

MASHINI OMWE SASIYA KUGWIRA NTCHITO

Tiyerekeze kuti mwaima penapake m’malo oonetsera zinthu zochititsa chidwi muja ndiye mukudzifunsa ngati zinthu m’nyukiliyasi ya selo zimangokhala osagwira ntchito. Kenako mukuona chikwangwani chomwe chili pafupi ndi DNA yongoyerekezera ndipo alembapo kuti: “Dinani apa kuti muone mmene DNA imagwirira ntchito.” Mutadina batani lija mukumva munthu akufotokoza kuti: “DNA imagwira ntchito zikuluzikulu ziwiri. Ntchito yoyamba ndi kukopera. DNA imafunika kudzikopera n’cholinga choti selo latsopano lililonse likhale ndi malangizo ofanana ndi maselo ena. Imanibe pomwepo kuti muonere.”

Ndiyeno pakubwera mashini ochititsa chidwi kwambiri omwe apangidwa ndi maloboti. Mashiniwa akuyamba kuyenda pa DNA yongoyerekezera ija ngati mmene sitima imayendera panjanji. Akuyenda mofulumira kwambiri moti zikukuvutani kuona zimene mashiniwo akuchita. Koma mukuona kuti kumbuyo kwake tsopano kuli zingwe ziwiri za DNA osati chimodzi.

Wofotokoza uja akunena kuti: “Apa tangokusonyezani mwachidule zimene zimachitika DNA ikamadzikopera. Mamolekyu otchedwa maenzayimu amayenda pa DNA ndipo choyamba amagawa DNA kuti ikhale ndi mbali ziwiri, kenako amagwiritsa ntchito mbali iliyonse n’kupanga mbali zinanso zofanana nazo ndendende. Mashiniwa ali ndi mbali zosiyanasiyana zimene zimagwira ntchito koma sitingakuonetseni zonse. Mwachitsanzo, pali kambali kena kakang’ono komwe kamathamanga patsogolo pa maenzayimu ndipo kamadula mbali imodzi ya DNA n’cholinga choti izizungulira bwinobwino popanda kumangana kwambiri. Sitingakwanitsenso kukusonyezani zimene DNA imachita maulendo ambirimbiri potsimikizira kuti palibe zolakwika komanso pokonza zolakwika zimene yapeza.”​—Onani chithunzi chomwe chili  patsamba 16 ndi 17.

Wofotokoza uja akupitiriza kuti: “Zimene tingakwanitse kukusonyezani ndi mmene zinthuzi zimagwirira ntchito mofulumira kwambiri. Kodi mwaona kuti mashiniwa akuyenda mofulumira? Komatu maenzayimu amayenda pa DNA mofulumira kwambiri moti amadutsa masitepe a DNA aja pafupifupi 100 pa sekondi iliyonse.23 Zimenezi tingaziyerekezere ndi sitima imene ikuthamanga pa liwiro la makilomita 80 pa ola limodzi. Koma maenzayimu amubakiteriya amagwira ntchitoyi pa liwiro limeneli kuwirikiza ka 10. M’maselo a thupi la munthu, magulu mahandiredi ambiri a maenzayimu amagwira ntchito m’malo osiyanasiyana a DNA pa nthawi imodzi. Ndipo amatha kukopera malangizo onse a mujenomu kwa maola 8 okha.””24 (Onani bokosi lakuti “ Molekyu Imene Ingathe Kuwerengedwa Komanso Kukoperedwa,” patsamba 20.)

KUWERENGA DNA

Panopa maenzayimu aja amaliza kukopera DNA ndipo akuchoka. Kenako mashini ena akubwera omwenso ndi maenzayimu. Nawonso akuyenda pa DNA koma osati mwamsanga kwambiri ngati maenzayimu oyamba aja. Chingwe cha DNA chija chikulowa mumashiniwa ndipo chikutulukira mbali ina koma sichinasinthe. Ndiye pali chingwe chinanso chimene chikutulukira mbali ina ya mashiniwo ndipo chikuoneka ngati mchira. Kodi n’chiyani chikuchitika?

Wofotokoza uja akunena kuti: “Ntchito yachiwiri ya DNA ndi kuwerenga malangizo ake. DNA sichoka m’malo otetezeka a munyukiliyasi. Koma malangizo a m’majini ake opangira mapulotini a thupi la munthu ayenera kuwerengedwa ndiponso kutsatiridwa. Choncho maenzayimu omwe amagwira ntchito ngati mashini amapeza jini ya DNA imene pafika uthenga wochokera panja pa nyukiliyasiyo ndipo amagwiritsa ntchito molekyu yotchedwa RNA kuti akopere jiniyo. RNA imaoneka mofanana ndi DNA koma ndi yosiyana ndipo ntchito yake ndi kuwerenga malangizo amene amakhala m’majini. RNA imawerenga malangizowo pa nthawi imene ili ndi maenzayimu aja, kenako imatuluka munyukiliyasi n’kukapereka malangizowo kumaribosomu kumene amagwiritsidwa ntchito kuti apange mapulotini.”

Mukudabwa kwambiri mukamaona zinthuzi zikuchitika. Mukuona kuti anthu amene anapanga malo oonetsera zinthuwa komanso mashini ake ali ndi luso kwambiri. Koma tangoganizirani mmene zingakhalire zikanatheka kuti malowa ndiponso mashini ake achite zinthu zonse zimene zimachitika muselo la thupi la munthu pa nthawi imodzi. N’zosachita kufunsa kuti zikanakhala zogometsa kwambiri.

Kenako mukuzindikira kuti zinthu zonse zimene mashiniwa akuchita n’zimene zikuchitika panopa m’maselo okwana 100 thiriliyoni omwe ali m’thupi lanu. Malangizo a mu DNA opangira mapulotini masauzande ambiri a maenzayimu, minofu kapena ziwalo za m’thupi lanu akuwerengedwa n’kumatsatiridwa. DNA yanu ikukoperedwanso komanso kutsimikiziridwa pofuna kuona ngati yakopedwa bwino n’cholinga choti selo latsopano lililonse likhale ndi malangizowo.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA MFUNDO ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Ndiye tiyenera kudzifunsanso kuti, ‘Kodi malangizo onsewa anachokera kuti?’ Baibulo limasonyeza kuti malangizowa analembedwa ndi winawake wapamwamba kwambiri kuposa anthu. Kodi tinganenedi kuti mfundo imeneyi ndi yachikale kapena yotsutsana ndi sayansi?

Taganizirani mfundo iyi: Kodi n’zothekadi kuti anthu amange malo oonetsera zinthu amene tafotokoza aja? Kunena zoona sangakwanitse. Pali zambiri zokhudza jenomu ya m’thupi la munthu zomwe anthufe sitikuzimvetsa mpaka pano. Asayansi akuyesetsa kudziwa malo onse amene majini amapezeka komanso ntchito zake. Koma majini ndi mbali yaing’ono chabe ya DNA. Nanga bwanji za malo ena onse a mu DNA amene palibe majini? Asayansi ananenapo kuti malo amenewa ndi opanda ntchito, koma posachedwapa asintha maganizo amenewa. Panopa amanena kuti mwina malowa ndi amene amapereka malangizo okhudza kagwiritsidwe ntchito ka majini. Ngati zikanatheka kuti asayansi apange DNA ndiponso mashini okopera DNA ndi kutsimikizira kuti yakopedwa bwino, kodi zikanathekadi kuti DNA imeneyo izigwira ntchito mofanana ndi DNA yeniyeni?

Wasayansi wotchuka kwambiri dzina lake Richard Feynman analemba pabolodi mfundo inayake atatsala pang’ono kumwalira. Iye analemba kuti: “Chinthu chimene sindingathe kuchipanga, sindingachimvetse.””25 N’zosangalatsa kuona kuti iye anavomereza mfundo imeneyi modzichepetsa ndipo pa nkhani ya DNA tinganene kuti mfundoyi ndi yoonadi. Tikutero chifukwa chakuti asayansi sangathe kupanga DNA limodzi ndi mashini ake onse komanso sangaimvetse bwino. Ngakhale zili choncho, ena amanenabe kuti amadziwa zoti DNA inangokhalapo mwangozi. Mukaganizira zimene takambiranazi, kodi mungavomereze zimene anthu ena amanenazi?

Anthu ena ophunzira amaona kuti umboni umene wapezeka susonyeza kuti DNA inakhalapo mwangozi. Mwachitsanzo, Francis Crick yemwe anatulukira zinthu zina zokhudza DNA ananena kuti molekyu ya DNA ndi yogometsa kwambiri moti n’zosatheka kuti inangokhalapo mwangozi. Koma iye ananena kuti mwina enaake anzeru amene amakhala mlengamlenga ndi amene anatumiza DNA padzikoli n’cholinga choti zamoyo ziyambe kupangika.26

Posachedwapa, katswiri wina dzina lake Antony Flew anasinthiratu maganizo ake. Kwa zaka 50, iye ankalimbikitsa anthu kuti asamakhulupirire kuti kuli Mulungu. Koma atakwanitsa zaka 81 anayamba kukhulupirira kuti kuli winawake wanzeru yemwe anachititsa kuti zamoyo zipangike. Iye anasintha maganizo ake chifukwa chophunzira mmene DNA ilili. Flew atafunsidwa mmene angamvere ngati asayansi ena sangasangalale ndi zimene wayamba kukhulupirira, anati: “Zimenezo ndi zawo. Ine pa moyo wanga wonse ndimayendera mfundo yakuti . . . tizikhulupirira zinthu mogwirizana ndi umboni umene wapezeka.””27

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi umboni umasonyeza chiyani? Tayerekezerani kuti mufakitale inayake mwapeza chipinda chokhala ndi kompyuta. Ndiyeno mwaona kuti kompyutayo ili ndi pulogalamu imene imayendetsa mashini onse a mufakitaleyo. Imatumizanso malangizo opangira ndiponso okonzera mashini onsewo ndipo pa nthawi yomweyo kompyutayo ikudzikopera komanso kutsimikizira kuti yakopedwa bwino. Kodi mungaganize kuti kompyutayo komanso pulogalamu yake zinangokhalako zokha kapena anthu anzeru ndi amene anazipanga? Kunena zoona yankho la funsoli ndi lodziwikiratu.

^ ndime 12 Buku lina lokhudza sayansi limafotokoza zimenezi m’njira ina. Limanena kuti kukulungiza zingwe zonsezi m’njira yoti zikwane munyukiliyasi ya selo kungafanane ndi kutenga ulusi wautali makilomita 40 n’kuuika m’kampira kosewerera tenesi, koma n’kuchita zimenezi mwaluso kwambiri moti mbali iliyonse ya ulusiwu ingapezeke mosavuta.​—Molecular Biology of the Cell.

^ ndime 18 Selo lililonse limakhala ndi majenomu awiri kapena kuti makoromosomu okwana 46.