Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 4

Kodi Zamoyo Zonse Zinachokera ku Chinthu Chimodzi?

Kodi Zamoyo Zonse Zinachokera ku Chinthu Chimodzi?

Darwin ankaganiza kuti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chimodzi. Iye anayerekezera mbiri ya zamoyo padziko lapansi ndi chimtengo chachikulu. Kenako, anthu ena anayamba kukhulupirira kuti mtengowu unayamba ndi thunthu limodzi lomwe likuimira maselo oyambirira. Kenako mitundu yatsopano ya zinyama komanso zomera inayamba kuphukira kuchokera ku thunthuli. Ndiyeno amati mitundu yosiyanasiyana ya zamoyo zimene zilipo masiku ano zinayamba mwa njira imeneyi. Kodi zimenezi ndi zimene zinachitikadi?

Kodi asayansi ambiri amanena zotani? Asayansi ambiri amanena kuti zinthu zakufa zakale zimene zinafukulidwa m’nthaka zimasonyezadi kuti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chimodzi. Iwo amanenanso kuti zimenezi ndi zoona chifukwa choti zamoyo zonse zimakhala ndi DNA.

Kodi Baibulo limanena zotani? Buku la Genesis limasonyeza kuti zomera, zamoyo zonse za m’madzi, nyama zapamtunda ndiponso mbalame zinalengedwa “monga mwa mtundu wake.” (Gen. 1:12, 20-25) Mawu akuti “mtundu” angaphatikize zamoyo zooneka mosiyanasiyana koma amasonyeza kuti zamoyo za mtundu wina sizingasinthiretu n’kukhala za mtundu wina. Zimene Baibulo limafotokoza pa nkhani yolenga zinthu zimasonyeza kuti mitundu yatsopano ya nyama inayamba kupezeka pa nthawi imodzi popanda kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Kodi umboni umasonyeza zotani? Kodi umboni womwe wapezeka umasonyeza kuti zoona ndi ziti, zimene Baibulo limanena kapena zomwe Darwin ananena? Kodi zimene anthu apeza pa zaka 150 zapitazi zikusonyeza chiyani?

ANTHU ANAZINDIKIRA KUTI ZIMENEDARWIN ANANENA SI ZOONA

M’zaka zaposachedwapa, asayansi apeza njira yoyerekezera malangizo a mu DNA ya zamoyo zosiyanasiyana. Iwo ankaganiza kuti kuchita zimenezi kungathandize kutsimikizira zimene Darwin ananena zoti zamoyo zinachokera ku chinthu chimodzi. Koma zimene apeza si zimenezo.

Kodi anapeza zotani atapanga kafukufuku? M’chaka cha 1999, katswiri wina wa zamoyo dzina lake Malcolm S. Gordon analemba kuti: “Zikuoneka kuti zamoyo sizinachokere ku chinthu chimodzi. Ndipo palibe umboni woti zamoyo zonse zinakhala ngati zaphuka kuchokera ku tsinde limodzi la mtengo.” Kodi pali umboni wosonyeza kuti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chimodzi ngati mmene Darwin ankakhulupirira? Gordon anapitiriza kuti: “Zimene anthu amakhulupirira zoti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chimodzi si zomveka tikaona mmene mitundu ikuluikulu ya zamoyo ilili. Mwina mfundo imeneyi singagwirenso ntchito tikaganizira za mitundu ing’onoing’ono ya zamoyo.””29 *

Zimene asayansi apeza posachedwapa n’zosiyananso kwambiri ndi mfundo imene Darwin ananena. Mwachitsanzo, mu 2009, m’magazini ina munali mawu a wasayansi wina dzina lake Eric Bapteste akuti: “Sitinapeze umboni uliwonse wotsimikizira kuti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chimodzi.””30 M’magazini yomweyo munalinso mawu a wasayansi wina dzina lake Michael Rose yemwe anati: “Pang’ono ndi pang’ono tikuzindikira kuti zimene Darwin ankaphunzitsa si zoona. Chatsala n’kungovomereza kuti tiyenera kusintha maganizo athu pa nkhani ya mmene moyo unayambira.”31 *​—New Scientist.

KODI ZINTHU ZAKALE ZIMENE ASAYANSI APEZA ZIMASONYEZA CHIYANI?

Asayansi ambiri amanena kuti zinthu zakufa zimene asayansi apeza zimatsimikizira kuti zamoyo zinachokera ku chinthu chimodzi. Mwachitsanzo, amanena kuti zinthu zimene apezazo zimasonyeza kuti nsomba zinasintha kukhala zinyama za m’gulu la achule ndipo zinyama za m’gulu la njoka ndi buluzi zinasintha n’kukhala nyama zoyamwitsa. Koma kodi zimenezi n’zoona?

Wasayansi wina dzina lake David M. Raup ananena kuti: “Asayansi a nthawi ya Darwin ndiponso amasiku ano sanapeze umboni wakuti zamoyo zinkasintha mwapang’onopang’ono n’kukhala zamoyo zina. Zinthu zakufa zimene apeza zikungosonyeza kuti mitundu ya zamoyo inangoyamba kukhalapo pa nthawi ina ndipo sinasinthe pa nthawi yonse imene inalipo, kenako ina inangosowa.””32

Zinthu zambiri zakale zimasonyeza kuti mitundu ya zinyama inakhalapo osasintha kwa nthawi yaitali. Sizisonyeza kuti zamoyo zinkasintha n’kukhala za mtundu wina. Zimasonyezanso kuti mitundu yatsopano ya zinyama inangoyamba kukhalapo nthawi imodzi. Mwachitsanzo, mileme yokhala ndi luso lozindikira zinthu popanda kuziona inangoyamba kukhalapo ndipo palibe umboni wakuti inachokera ku zamoyo zina zimene zinalibe luso limeneli.

Ndipo zikuoneka kuti hafu ya mitundu ikuluikulu ya zinyama inayamba kukhalapo pa nthawi yochepa. Asayansi amatchula nyengo imene zamoyozi zinayamba kupezeka pa nthawi imodzi kuti Cambrian. Ndiye kodi nyengo imeneyi inayamba liti?

Ngati zimene asayansiwa amanena ndi zoona, ndiye kuti nthawi yonse imene dzikoli lakhalapo tingaiyerekezere ndi mzere wautali ngati bwalo la mpira wa miyendo (1). Ngati mutayamba kuyenda pabwaloli, kuti mufike pamene pali nyengo ya Cambrian muyenera kufika chakumapeto kwa bwalolo (2). Zinthu zakufa zimene azipeza zimasonyeza kuti mitundu ikuluikulu ya zinyama inayamba kupezeka pa nthawi yochepa m’nyengoyi. Kodi inayamba kupezeka munthawi yochepa bwanji? Mukamayenda chakumapeto kwa bwalo la mpiralo, mitundu yonse ya zinyamazo zinayamba kupezeka musanamalize kuyenda ngakhale sitepe imodzi yokha.

Popeza kuti mitundu yambiri ya zinyama inayamba kupezeka pa nthawi yochepa chabe, asayansi ena ayamba kukayikira zimene Darwin ananena. Mwachitsanzo, mu 2008 wasayansi wina dzina lake Stuart Newman ananena kuti pakufunika kupeza njira yatsopano yofotokozera zimene zinachitika kuti zamoyo zisinthe. Njirayo iyenera kugwirizana ndi mfundo yakuti mitundu yambiri ya zinyama inayamba kupezeka nthawi imodzi. Iye anati: “Ndikukhulupirira kuti anthu ambiri adzayamba kuona kuti zimene Darwin ananena zija zikhala ngati mfundo ina chabe yotithandiza kumvetsa zimene zinachitika kuti nyama zisinthe n’kukhala za mitundu ina, koma osati mfundo yofunika kwambiri.”33

UMBONI WAKE SI WODALIRIKA

N’chifukwa chiyani m’mabuku ena amasintha kakulidwe ka nyama zina zakufa?

Kumanzere m’mwamba: mmene amajambulira m’mabuku ena

Kumanja m’mwamba: mmene nyamazo zilili

Nanga bwanji zinthu zakufa zimene amazigwiritsa ntchito posonyeza kuti nsomba zinasintha n’kukhala m’gulu la achule ndipo nyama zoikira zinasintha n’kukhala zoyamwitsa? Kodi zimaperekadi umboni wakuti zamoyo zinachita kusintha? Kafukufuku akusonyeza kuti umboni wake si wodalirika.

Choyamba, nyama zakufa zimene zimajambulidwa m’mabuku posonyeza kuti nyama zoikira zinkasintha mwapang’onopang’ono mpaka kukhala zoyamwitsa, nthawi zina amazijambula mosiyana kwambiri ndi mmene zilili. Zina amazikulitsa kwambiri pomwe zina amazichepetsa.

Chachiwiri n’chakuti palibe umboni wotsimikizira kuti nyamazo zinasintha kuchokera ku nyama imodzi. Asayansiwo amanena kuti nyama zina zimene zimajambulidwazo zinakhalapo zaka mamiliyoni ambiri zina zisanakhalepo. Ponena za zaka zimene asayansiwa amanena, wasayansi wina dzina lake Henry Gee ananena kuti: “Pali kusiyana kwambiri pa nthawi imene nyamazi zinakhalapo moti n’zovuta kutsimikizira kuti zinachokera ku nyama imodzi.”34 *

Pa nkhani ya zinthu zakufa zosonyeza kuti nsomba zinasintha n’kukhala nyama za m’gulu la achule, Malcolm S. Gordon ananena kuti zinthu zakufa zimene zapezekazo ndi zochepa ndipo “mwina sizingasonyeze kwenikweni kuchuluka kwa mitundu ya nsomba komanso nyama za m’gulu la achule zomwe zinalipo pa nthawizo.” Iye anapitiriza kuti: “N’zosatheka kudziwa ngati nyama zakufa zimene mbali zake zapezeka zinasintha n’kukhala za mitundu ina kapena ngati zikuchokera ku nyama imodzi.”35 *

KODI MBALI ZA FILIMU ZIKUSONYEZA CHIYANI?

Nkhani ya m’magazini ina inayerekezera zinthu zakufa zimene asayansi azipeza ndi filimu yosonyeza kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina. Inanena kuti: “Pa mbali 1,000 zilizonse za filimuyo, mbali 999 zasowa.”36 (National Geographic) Kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?

Ngati “mbali 95” za zinthu zakufa zimasonyeza kuti nyama sizinasinthe n’kukhala nyama zina, n’chifukwa chiyani asayansi amasanja “mbali 5” zotsalazo pofuna kusonyeza kuti nyama zinasinthadi?

Tiyerekeze kuti mwapeza mbali 100 za filimu imene poyamba inali ndi mbali 100,000. Kodi mungadziwe kuti filimuyo inali yonena za chiyani? Mwina mungakhale ndi chithunzi cha filimuyo. Koma nanga zitachitika kuti mbali 5 zokha n’zimene zikugwirizana ndi chithunzi chimene mukuganiza, pomwe 95 zikusiyana ndi zimene mukuganizazo. Kodi mungakakamire maganizo anuwo chifukwa cha mbali 5 zokhazo? Mwina n’kutheka kuti mwasanja dala mbali 5 zimenezo m’njira yoti zigwirizane ndi maganizo amene muli nawo kale. Koma kodi si chanzeru kulola kuti mbali 95 zinazo zikuthandizeni kudziwa zoona zake za filimuyo?

Ndiye kodi chitsanzo chimenechi chikugwirizana bwanji ndi nkhani imene tikukambiranayi? Kwa zaka zambiri, asayansi sanavomereze kuti zinthu zakufa zambiri zimene zapezeka, zomwe zili ngati mbali 95 za filimu, zimasonyeza kuti nyama sizinasinthe kwenikweni ngakhale patapita nthawi yaitali. Koma n’chifukwa chiyani sanavomereze zimenezi? Wolemba mabuku wina dzina lake Richard Morris ananena kuti: “Zikuoneka kuti asayansi sankafuna kusiya kukhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha mwapang’onopang’ono kuchokera ku zinthu zina ngakhale pamene anapeza umboni wotsutsa mfundoyi. Iwo ankayesetsa kufotokoza zinthu zakufa zimene anapeza m’njira yoti zizigwirizana ndi zimene ankakhulupirirazo.”37

“Kutenga zinthu zakufa zimene zapezeka n’kuzisanja pofuna kusonyeza mmene zinyama zinasinthira kuchokera ku nyama zinzake n’kosagwirizana ndi sayansi chifukwa palibe umboni wake. Kungafanane ndi kuuza mwana nthano kuti agone. Zikhoza kukhala zosangalatsa kapena zophunzitsa mwanayo zinazake koma sizigwirizana ndi sayansi.”​—In Search of Deep Time​—Beyond the Fossil Record to a New History of Life, lolembedwa ndi Henry Gee, tsa. 116-117

Nanga bwanji za asayansi amasiku ano amene amakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha? Kodi mwina nawonso amasanja zinthu zakufa m’njira yoti zizigwirizana ndi zimene ambiri amakhulupirira, osati mogwirizana ndi umboni umene wapezeka? *

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Malinga ndi umboni umene wapezeka, kodi zoona zake pa nkhaniyi ndi ziti? Tiyeni tionenso mfundo zimene takambirana.

  • Palibe chamoyo chimene chinali chosadabwitsa, ngakhale choyambirira.

  • Umboni ukusonyeza kuti n’zovuta kapenanso zosatheka kuti ngakhale selo limodzi lingokhalako lokha.

  • DNA yomwe imakhala ndi malangizo amene amayendetsa zinthu muselo ndi yodabwitsa kwambiri moti palibiretu kompyuta kapena chipangizo chilichonse chimene anthu apanga chomwe chingafanane nayo.

  • Kafukufuku wokhudza majini amasonyeza kuti zamoyo sizinachokere ku chinthu chimodzi. Komanso zinthu zakufa zimene zapezeka zimasonyeza kuti mitundu ikuluikulu ya zinyama inayamba kukhalapo pa nthawi imodzi.

Malinga ndi mfundo zimenezi, kodi simungavomereze kuti umboni umene wapezeka umagwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mmene zamoyo zinayambira? Koma anthu ambiri amanena kuti sayansi imatsutsana ndi mfundo zambiri zimene Baibulo limanena pa nkhani yolenga zinthu. Koma kodi zimenezi n’zoona? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

^ ndime 9 Asayansi amaika zamoyo m’magulu kapena mitundu yosiyanasiyana malinga ndi kufanana kapena kusiyana kwake. Amazigawa m’mitundu ikuluikulu ndipo kenako amazigawanso m’mitundu ing’onoing’ono.

^ ndime 10 Tiyenera kudziwa kuti magaziniyi, Bapteste komanso Rose sankatsutsa zoti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Mfundo yawo yaikulu inali yakuti zimene Darwin ananena zoti zamoyo zinachokera ku chinthu chimodzi n’zopanda umboni. Koma asayansi ngati amenewa akufufuzabe njira zina zofotokozera kuti zimene amakhulupirira, zoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina, ndi zoona.

^ ndime 21 Sikuti Henry Gee amatsutsa zoti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina. Anangonena izi pofuna kusonyeza kuti zinthu zakufa zimene anthu apeza sizingathandize kwambiri kudziwa zoona zake pa nkhaniyi.

^ ndime 22 Malcolm S. Gordon amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

^ ndime 50 Dziwani kuti: Asayansi onse amene apereka ndemanga zawo m’bokosili sakhulupirira zimene Baibulo limanena pa nkhani yolenga zinthu. Onse amakhulupirira kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina.