Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kwa anthu amene amakonda Yehova Mulungu ndiponso Baibulo:

Yesu ananena kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Takumbukirani mmene munamvera mutangophunzira kumene choonadi kuchokera m’Baibulo. Munasangalala kudziwa kuti n’zotheka kuphunzira choonadi ngakhale kuti tikukhala m’dziko lodzadza ndi bodza.​—2 Timoteyo 3:1.

Yehova Mulungu amafuna kuti tidziwe choonadi. Ndipo timafuna kuuza ena za choonadichi chifukwa chakuti timawakonda. Koma pali zambiri zimene tiyenera kuchita potumikira Mulungu. Tiyenera kuyesetsa kumakhala monga Akhristu chifukwa choti timalemekeza kwambiri mfundo za Yehova. Yesu anafotokoza njira imodzi yofunika yomwe tingamusonyezere Mulungu kuti timamukonda. Iye ananena kuti: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’chikondi changa, monga mmene ine ndasungira malamulo a Atate ndi kukhalabe m’chikondi chake.”​—Yohane 15:10.

Yesu amakonda kwambiri Atate ake ndipo amachita chilichonse chimene amamuuza kuti achite. Ngati titamatsanzira Yesu pa moyo wathu, Yehova adzatikonda ndipo tidzakhala wosangalala. Ndipotu paja Yesu ananena kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziwa, ndinu odala mukamazichita.”​—Yohane 13:17.

Tikukhulupirira kuti bukuli likuthandizani kuti muzikhala mogwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo ndiponso kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova. Pemphero lathu ndi lakuti mupitirize kukulitsa chikondi chanu pa Yehova komanso kupitiriza kuchita zimene zingachititse Mulungu kukukondani kuti ‘mudzalandire moyo wosatha.’​—Yuda 21.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova