Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 12

Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”

Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”

“Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.”​—AEFESO 4:29.

1-3. (a) Kodi Yehova anatipatsa mphatso iti, nanga ndi zinthu ziti zomwe zingasonyeze kuti sitikuigwiritsa ntchito bwino? (b) Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphatso yolankhula?

TIYEREKEZE kuti bambo wagulira mwana wake njinga. Bamboyo akusangalala kuti wam’patsa mwana wakeyo mphatso yapadera. Koma kodi angamve bwanji ngati mwanayo atamayendetsa njingayo mosasamala, moti tsiku lina wagunda munthu mpaka munthuyo kuvulala?

2 Yehova amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yakobo 1:17) Imodzi mwa mphatsozi ndi mphatso ya kulankhula. Mphatso imeneyi imatithandiza kuti tizifotokozera ena maganizo athu komanso mmene tikumvera. Timathanso kulankhula zinthu zimene zingathandize ndiponso kusangalatsa ena. Koma zolankhula zathu zikhozanso kubweretsa mavuto kwa ena kapena kuwakhumudwitsa.

3 Mawu amene timalankhula amakhala ndi mphamvu. N’chifukwa chake Yehova amatiphunzitsa mmene tingagwiritsire ntchito bwino mphatso yolankhula. Amatiuza kuti: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikire, kuti asangalatse owamva.” (Aefeso 4:29) Tiyeni tione mmene tingagwiritsire ntchito bwino mphatso imeneyi kuti tizisangalatsa Yehova komanso tizilimbikitsa ena.

MUZISAMALA NDI ZIMENE MUMALANKHULA

4, 5. Kodi tingaphunzire chiyani m’buku la Miyambo pa nkhani ya zolankhula zathu?

4 Monga taona kale, mawu amakhala ndi mphamvu. Choncho tiyenera kusamala ndi zomwe timalankhula komanso mmene timalankhulira. Lemba la Miyambo 15:4 limati: “Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo, koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.” Monga zilili kuti mtengo wokongola umasangalatsa, mawu abwino amalimbikitsa munthu. Koma mawu opweteka amakhumudwitsa munthu ndipo amam’pangitsa kudziona ngati wosafunika.​—Miyambo 18:21.

Mawu abwino amalimbikitsa kwambiri munthu amene tikulankhula naye

5 Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga.” Munthu wolankhula mosaganizira angakhumudwitse kwambiri ena komanso angachititse kuti anthu adane. Mwina mukukumbukira nthawi imene wina analankhula mawu amene anakukhumudwitsani kwambiri. Koma lembali limapitiriza kuti: “Lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Mawu osonyeza kuganizira ena angathandize kuti munthu amene anakhumudwa ayambirenso kusangalala komanso kuti anthu amene anakhumudwitsana ayambirenso kugwirizana. (Werengani Miyambo 16:24.) Tikamakumbukira kuti zolankhula zathu zingakhumudwitse ena kapena kuwalimbikitsa, tidzayesetsa kulankhula mosamala.

6. N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta kuti tizilankhula bwino?

6 Tiyeneranso kusamala ndi zomwe timalankhula chifukwa tonsefe si ife angwiro. Baibulo limanena kuti, “maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.” Nthawi zambiri zolankhula zathu zimasonyeza zomwe zili mumtima mwathu. (Genesis 8:21; Luka 6:45) Ndipo nthawi zina zimakhala zovuta kwambiri kuti tizilankhula bwino. (Werengani Yakobo 3:2-4.) Komabe tiyenera kuyesetsa kuti tizilankhula bwino.

7, 8. Kodi zolankhula zathu zingakhudze bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

7 Tiyeneranso kusamala ndi zolankhula zathu chifukwa timakhala ndi mlandu kwa Yehova pa zimene timalankhula komanso mmene timalankhulira. Lemba la Yakobo 1:26 limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” Mawu amene anawamasulira kuti “n’kopanda pake,” angatanthauzenso kuti “n’kopanda ntchito.” (1 Akorinto 15:17) Choncho, ngati sitisamala polankhula tingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.​—Yakobo 3:8-10.

8 Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula komanso mmene timalankhulira. Koma kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphatso yolankhula, tiyenera kudziwa malankhulidwe oyenera kuwapewa.

MAWU OKHUMUDWITSA

9, 10. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano amakonda kulankhula motani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kutukwana?

9 Anthu ambiri masiku ano amakonda kutukwana kapena kulankhula mawu osayenera. Ambiri amaganiza kuti ayenera kutukwana kapena kulankhula mawu onyoza kuti anthu amvetse zimene akunena. Ochita zisudzo amakonda kugwiritsa ntchito mawu komanso nthabwala zotukwana n’cholinga choti aseketse anthu. Koma mtumwi Paulo ananena kuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Ananenanso kuti: “Nthabwala zotukwana” ‘zisamatchulidwe n’komwe pakati’ pa Akhristu.​—Aefeso 5:3, 4.

10 Yehova komanso anthu amene amamukonda amadana kwambiri ndi kutukwana. Mawu otukwana, ndi zinthu zodetsa. Baibulo limati “zinthu zodetsa” zili m’gulu la “ntchito za thupi.” (Agalatiya 5:19-21) “Zinthu zodetsa” zingaphatikizepo machimo osiyanasiyana ndipo khalidwe lililonse lodetsa lingachititse kuti munthu achitenso khalidwe lina lodetsa. Ngati munthu ali ndi chizolowezi cholankhula mawu oipa kwambiri komanso olaula ndipo akukana kusiya, angachotsedwe mumpingo.​—2 Akorinto 12:21; Aefeso 4:19; onani Mawu Akumapeto 23.

11, 12. (a) Kodi miseche n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kulankhula zabodza zokhudza anthu ena?

11 Tiyeneranso kupewa miseche. Mwachibadwa anthufe timachita chidwi ndi anthu ena ndipo timakonda kufotokozera ena zokhudza anzathu kapena achibale athu. Zoterezi zinkachitikanso mu nthawi ya atumwi. Akhristu ankafuna kudziwa mmene abale ndi alongo awo alili komanso mmene angawathandizire. (Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:8, 9) Koma titapanda kusamala, nkhani zokhudza anthu ena zikhoza kusintha n’kukhala miseche. Tikayamba kufotokozera ena nkhani za miseche zimene ena anatiuza, tingapezeke kuti tikulankhula nkhani zabodza komanso zimene zimayenera kukhala zachinsinsi. Kenako tingapezeke kuti tayamba kumunena munthu pa zinthu zoti zilibe umboni. Zimenezi ndi zomwe Afarisi ankachita. Ankamunena Yesu pa zinthu zoti alibe umboni wake. (Mateyu 9:32-34; 12:22-24) Nkhani zabodza zimaipitsa mbiri ya munthu, zimayambitsa mikangano, zimakhumudwitsa wonamiziridwayo komanso zimadanitsa anthu.​—Miyambo 26:20.

12 Yehova amafuna kuti tizilankhula zinthu zothandiza komanso zolimbikitsa, osati zodanitsa anthu. Iye amadana ndi “aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.” (Miyambo 6:16-19) Woyambirira kunena bodza anali Satana ndipo ananamizira Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 10) Masiku ano anthu ambiri amakonda kulankhula zabodza zokhudza anthu ena. Koma Akhristu sayenera kuchita zimenezi. (Agalatiya 5:19-21) Choncho tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula komanso tiziyamba taganiza kaye tisanalankhule. Tisanauze ena nkhani yokhudza munthu wina yomwe tamva, tizidzifunsa kaye kuti: ‘Kodi zomwe ndikufuna kunenazi ndi zoona, nanga zisonyeza kuti ndine wachikondi? Kodi n’zothandiza? Kodi munthu ndikumunenayo atamva zingakhale bwanji? Kodi ndingamve bwanji munthu wina atandinenera ineyo zimenezi?’​—Werengani 1 Atesalonika 4:11.

13, 14. (a) Kodi mawu achipongwe ndi oopsa bwanji? (b) Kodi kulalata n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kupewa kulalatira ena?

13 Tonsefe nthawi zina timalankhula zinthu zomwe pambuyo pake tinganong’oneze nazo bondo. Koma si bwino kukhala ndi chizolowezi cholankhula zonyoza ena kapena kuwalankhula mawu osakhala bwino. Akhristufe tiyenera kupewa kulankhula mawu achipongwe. Paulo ananena kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aefeso 4:31) Mabaibulo ena anamasulira mawu akuti “mawu achipongwe” kuti “mawu oipa,” “mawu opweteka,” ndiponso “mawu onyoza.” Mawu achipongwe amamuchotsera munthu ulemu komanso amamupangitsa kuti azidziona kuti ndi wosafunika. Ana sachedwa kukhumudwa, choncho tiyenera kusamala kwambiri tikamalankhula ndi ana.​—Akolose 3:21.

14 Baibulo limatichenjezanso kuti tiyenera kusamala kwambiri ndi mawu ena achipongwe, omwe ndi kulalata. Kulalata kumatanthauza kumulankhula munthu mawu onyoza kwambiri n’cholinga choti akhumudwe. Zingakhale zokhumudwitsa kwambiri ngati munthu atamachitira zimenezi mkazi kapena mwamuna wake kapenanso ana ake. Ndipotu munthu amene amakana kusiya khalidwe lolalata angathe kuchotsedwa mumpingo. (1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10) Monga taonera, ngati titamatukwana kapena kulankhula zabodza, tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova komanso ndi anthu ena.

MAWU OLIMBIKITSA

15. Kodi ndi mawu otani amene amathandiza kuti anthu azigwirizana?

15 Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mphatso ya kulankhula m’njira imene Yehova amafuna? Ngakhale kuti Baibulo silitiuza mawu enieni oyenera kulankhula ndi osayenera kulankhula, limatiuza kuti tiyenera kulankhula mawu “olimbikitsa” okha. (Aefeso 4:29) Mawu olimbikitsa amakhala oyera, osonyeza kukoma mtima komanso oona. Yehova amafuna kuti tizilankhula mawu olimbikitsa komanso othandiza. Koma zimenezi sizophweka. Pamafunika khama kuti tilankhule mawu abwino kusiyana ndi kulankhula mosaganiza. (Tito 2:8) Tiyeni tikambirane zinthu zina zomwe tingalankhule kuti tilimbikitse ena.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumayamikira ena? (b) Kodi ndi ndani amene tingawayamikire?

16 Yehova ndi Yesu saumira kuyamikira ena akachita zabwino ndipo tiyenera kuwatsanzira. (Mateyu 3:17; 25:19-23; Yohane 1:47) Koma kuti tithe kuyamikira munthu m’njira yoti timulimbikitse, tiyenera kumachita chidwi ndi munthuyo komanso kuyamba taganizira kaye tisanalankhule. Lemba la Miyambo 15:23 limati: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.” Timalimbikitsidwa kwambiri munthu wina akatiyamikira mochokera pansi pa mtima chifukwa choti tagwira ntchito mwakhama kapena tachita zinthu zinazake zabwino.​—Werengani Mateyu 7:12; onani Mawu Akumapeto 27.

17 Ngati mutakhala ndi chizolowezi chomaona zabwino mwa ena, zingakhale zosavuta kuti muziwayamikira. Mwachitsanzo, mwina mungaone kuti munthu wina amakonzekera bwino nkhani kapena amayesetsa kuyankha pa misonkhano. Mwinanso pangakhale wachinyamata wina amene amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo akakhala kusukulu kapena wachikulire amene nthawi zonse amalowa mu utumiki. Kuwayamikira anthu oterewa kungawalimbikitse kwambiri. N’zofunikanso kwambiri kuti amuna aziuza akazi awo kuti amawakonda komanso amayamikira zimene amachita. (Miyambo 31:10, 28) Monga zilili kuti zomera zimafuna kuwala komanso madzi, nawonso anthu amasangalala akamayamikiridwa pa zabwino zimene amachita. Ana makamaka ndi amene amafunika kuwayamikira. Choncho yesetsani kuti muziwayamikira chifukwa cha makhalidwe awo abwino komanso khama lawo. Kuwayamikira kungapangitse kuti azichita zinthu molimba mtima, asamadzikayikire komanso aziyesetsa kuchita zabwino.

Tingathe kulimbikitsa ena pa zimene timalankhula komanso mmene timalankhulira

18, 19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbikitsa ena, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

18 Tikamalimbikitsa ena komanso kuwatonthoza timakhala kuti tikutsanzira Yehova. Yehova amadera nkhawa anthu “onyozeka” ndiponso “opsinjika.” (Yesaya 57:15) Iye amafuna kuti ‘tizilimbikitsana’ komanso ‘tizilankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni.’ (1 Atesalonika 5:11, 14) Tikamachita zimenezi Yehova amaona ndipo amayamikira khama lathu.

19 Mwina mungazindikire kuti munthu wina wa mumpingo wakhumudwa ndi zinazake kapena akuda nkhawa kwambiri. Kodi mungalankhule zotani kuti mumulimbikitse? Mwina simungathe kuthetsa vuto lakelo. Komabe mukhoza kuchita zinthu zimene zingathandize munthuyo kudziwa kuti mumamuganizira. Mwachitsanzo, mungapeze nthawi yocheza naye kuti mumulimbikitse. Mwinanso mungawerenge naye lemba lolimbikitsa kapenanso kumupempha kuti mupemphere naye. (Salimo 34:18; Mateyu 10:29-31) Mutsimikizireni kuti abale ndi alongo amamukonda kwambiri. (1 Akorinto 12:12-26; Yakobo 5:14, 15) Muzilankhula mosonyeza kuti zimene mukunenazo ndi zoona ndipo mumazikhulupirira.​—Werengani Miyambo 12:25.

20, 21. N’chiyani chingathandize kuti munthu asavutike kulandira malangizo omwe wapatsidwa?

20 Tingathenso kulimbikitsa ena powapatsa malangizo abwino. Popeza anthufe si angwiro, nthawi zambiri timafunika malangizo. Lemba la Miyambo 19:20 limati: “Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo.” Si akulu okha amene ayenera kupereka malangizo. Makolonso ayenera kupereka malangizo kwa ana awo. (Aefeso 6:4) Komanso alongo angathe kupatsana malangizo abwino. (Tito 2:3-5) Popeza timakonda abale ndi alongo athu, tiyenera kupereka malangizo m’njira yoti tisawakhumudwitse. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

21 Mwina mukukumbukira nthawi imene munthu wina anakupatsani malangizo abwino m’njira yoti simunavutike kuwatsatira. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti muone kuti malangizowo ndi othandiza? Muyenera kuti munazindikira kuti munthuyo amakuganizirani. Apo ayi, anapereka malangizowo mokoma mtima komanso mwachikondi. (Akolose 4:6) Malangizowo ayeneranso kuti anali ochokera m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Malangizo alionse amene tikupereka, ayenera kukhala ochokera m’Malemba, kaya titchula lemba ndendende m’mene lilili kapena tingotchula mfundo yake. Sitiyenera kukakamiza anthu kuti azitsatira maganizo athu komanso sitiyenera kupotoza malemba n’cholinga choti agwirizane ndi maganizo athuwo. Kukumbukira mmene munthu wina anakupatsirani malangizo komanso mmene munamvera, kungakuthandizeni mukamapereka malangizo.

22. Kodi inuyo mukufuna kuti muzigwiritsa ntchito bwanji mphatso yanu ya kulankhula?

22 Monga taonera, kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Popeza timakonda Mulungu tiyenera kuyesetsa kuti tiziigwiritsa ntchito bwino mphatsoyi. Choncho tiyeni tizichita chilichonse chimene tingathe kuti tizilankhula mawu olimbikitsa kwa ena.