Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 20

Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?

Kodi Mpingo wa Chikhristu Umayendetsedwa bwanji?

Yehova ndi Mulungu wadongosolo. (1 Akorinto 14:33) Choncho anthu akenso ayenera kumachita zinthu mwadongosolo. Ndiye kodi mpingo wa Chikhristu umayendetsedwa bwanji? Nanga tingathandize bwanji kuti mpingo uziyenda bwino?

1. Kodi ndi ndani amene amatsogolera mpingo wa Chikhristu?

‘Khristu ndi mutu wa mpingo.’ (Aefeso 5:23) Yesu ali kumwamba koma amatsogolera ntchito imene anthu a Yehova amachita padziko lonse lapansi. Monga mutu wa mpingo iye wasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kapoloyu ndi kagulu kakang’ono ka akulu omwe amadziwikanso kuti Bungwe Lolamulira. (Werengani Mateyu 24:45-47.) Mofanana ndi atumwi komanso akulu a ku Yerusalemu, Bungwe Lolamulira limapereka malangizo kumipingo ya padziko lonse lapansi. (Machitidwe 15:2) Koma anthu amenewa si atsogoleri a gulu lathu. Tikutero chifukwa iwo amadalira Yehova ndi Mawu ake kuti aziwatsogolera ndiponso amagonjera Yesu monga mutu wawo.

2. Kodi akulu amagwira ntchito yanji mumpingo?

Akulu ndi abale olimba mwauzimu omwe amaphunzitsa Malemba ndi kusamalira anthu a Yehova powathandiza ndi kuwalimbikitsa. Iwo salandira malipiro akamagwira ntchito yawoyi. M’malomwake amatumikira ‘mofunitsitsa, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake koma ndi mtima wonse.’ (1 Petulo 5:1, 2) Akulu amathandizidwa ndi atumiki othandiza, omwe n’kupita kwa nthawi nawonso amadzayenerera kukhala akulu.

Bungwe Lolamulira limasankha akulu ena kuti akhale oyang’anira madera. Abale amenewa amayendera mipingo yosiyanasiyana kuti alimbikitse abale ndi alongo komanso kuwapatsa malangizo othandiza. Oyang’anira maderawa amaika pa udindo akulu komanso atumiki othandiza amene akwaniritsa mfundo za Malemba.​—1 Timoteyo 3:1-10, 12; Tito 1:5-9.

3. Kodi wa Mboni aliyense ali ndi udindo wotani?

Aliyense mumpingo ‘amatamanda dzina la Yehova’ pochita nawo zinthu zosiyanasiyana pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake.​—Werengani Salimo 148:12, 13.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti mudziwe kuti Yesu ndi mtsogoleri wotani, zimene akulu amachita potengera chitsanzo chake, komanso zimene ifeyo tingachite kuti tizimvera Yesu ndi akulu.

4. Yesu ndi mtsogoleri wachifundo

Yesu akutipempha mwachikondi kuti akhale mtsogoleri wathu. Werengani Mateyu 11:28-30, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Yesu ndi mtsogoleri wotani, nanga iye amafuna kuti tizimva bwanji akamatitsogolera?

Kodi akulu amatengera bwanji chitsanzo cha Yesu? Onerani VIDIYO.

Baibulo limanena momveka bwino zimene akulu ayenera kuchita pogwira ntchito yawo.

Werengani Yesaya 32:2 ndi 1 Petulo 5:1-3, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti akulu amayesetsa kulimbikitsa ena ngati mmene Yesu ankachitira?

  • Kodi akulu amatsanzira Yesu m’njira zinanso ziti?

5. Akulu amaphunzitsa ena pogwiritsa ntchito chitsanzo chawo chabwino

Kodi Yesu amafuna kuti akulu aziuona bwanji udindo wawo? Onerani VIDIYO.

Yesu ndi chitsanzo chabwino kwa abale amene amatsogolera mumpingo. Werengani Mateyu 23:8-12, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chiyani chimakuchititsani chidwi mukaganizira kusiyana kwa zimene Baibulo limanena kuti akulu azichita ndi zomwe mwakhala mukuona atsogoleri azipembedzo akuchita?

  1. Akulu amayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo amathandizanso mabanja awo kuchita zomwezo

  2. Akulu amasamalira anthu onse mumpingo

  3. Akulu amalalikira nthawi zonse

  4. Akulu amaphunzitsa mumpingo. Amagwiranso ntchito zina monga kukonza pa Nyumba ya Ufumu

6. Tizimvera akulu

Baibulo limatiuza chifukwa chomveka chimene tiyenera kumamvera akulu. Werengani Aheberi 13:17, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani Baibulo limatilimbikitsa kuti tizimvera komanso kugonjera amene akutsogolera? N’chifukwa chiyani mukutero?

Werengani Luka 16:10, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumamvera akulu ngakhale pa nkhani zooneka ngati zing’onozing’ono?

ZIMENE ENA AMANENA: “Si zofunikira kwenikweni kukhala m’chipembedzo chinachake.”

  • Kodi inuyo mukuganiza kuti munthu angapindule bwanji akamalambira Mulungu limodzi ndi mpingo?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yesu ndi mutu wampingo. Timasangalala kumvera akulu omwe amamvera Yesu chifukwa amatilimbikitsa komanso amatiphunzitsa pogwiritsa ntchito chitsanzo chawo chabwino.

Kubwereza

  • Kodi mutu wampingo ndi ndani?

  • Kodi akulu amathandiza bwanji mpingo?

  • Kodi wa Mboni aliyense ali ndi udindo wotani?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani umboni wakuti Bungwe Lolamulira ndi akulu amaganizira kwambiri Akhristu masiku ano.

Kulimbikitsa Abale Ntchito Yathu Ikaletsedwa 4:22

Onani ntchito imene oyang’anira dera amagwira.

Moyo wa Woyang’anira Dera Amene Amatumikira Madera a ku Midzi 4:51

Onani zimene akulu amachita kuti alimbikitse abale ndi alongo awo.

“Akulu Achikhristu Ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe” (Nsanja ya Olonda, January 15, 2013)