Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 29

N’chiyani Chimachitikira Munthu Amene Wamwalira?

N’chiyani Chimachitikira Munthu Amene Wamwalira?

Kodi munaferedwapo? Anthu ena akaferedwa amadzifunsa kuti, ‘N’chiyani chimachitikira munthu amene wamwalira? Kodi n’zotheka kudzaonananso ndi okondedwa athu amene anamwalira? M’phunziroli komanso lotsatira, tipeza mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa.

1. N’chiyani chimachitikira munthu amene wamwalira?

Yesu anayerekezera imfa ndi tulo tofa nato. Ndiye kodi imfa imafanana bwanji ndi tulo? Munthu amene wagona tulo tofa nato, sadziwa chilichonse chimene chikuchitika. Munthu akamwalira samva kupweteka kulikonse ndiponso savutika mwa njira ina iliyonse. Baibulo limati: “Akufa sadziwa chilichonse.”​—Werengani Mlaliki 9:5.

2. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?

Anthu ambiri amachita mantha ndi imfa ngakhalenso ndi anthu amene anamwalira. Koma mukaphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza imfa mulimbikitsidwa kwambiri. Yesu anati: “Choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira. Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Choncho munthu akamwalira savutika kapena kumva kupweteka. Komanso akufa sangativulaze chifukwa sadziwa chilichonse. Choncho, sitiyenera kuchita chilichonse chosonyeza kuti tikulambira kapena kulemekeza akufa poopa kuti angativulaze.

Anthu ena amanena kuti angathe kulankhula ndi amene anamwalira. Koma zimenezi sizingatheke. Monga mmene taphunzirira, anthu amene anamwalira, “sadziwa chilichonse.” Amene amaganiza kuti akulankhulana ndi achibale awo amene anamwalira, amakhala akulankhulana ndi ziwanda zimene zimayerekezera kukhala munthu womwalirayo. Choncho kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira, kumatiteteza kuti tisamavutitsidwe ndi ziwanda. Yehova amatichenjeza kuti tisayese kulankhulana ndi anthu amene anamwalira chifukwa amadziwa kuti kulankhulana ndi ziwanda kungatibweretsere mavuto aakulu.​—Werengani Deuteronomo 18:​10-12.

FUFUZANI MOZAMA

Dziwani zambiri zokhudza zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Zimenezi zikuthandizani kuti muzikhulupirira kwambiri Mulungu wachikondi yemwe sazunza anthu amene amwalira.

3. N’chiyani chimene chimachitikira munthu amene wamwalira?

Padziko lonse lapansi anthu amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitikira munthu amene wamwalira. Koma zambiri mwa zimene amakhulupirirazi, si zoona.

  • Kodi anthu ambiri m’dera lanu amakhulupirira zotani zokhudza zimene zimachitikira munthu amene wamwalira?

Kuti mudziwe zimene Baibulo limaphunzitsa, onerani VIDIYO.

Werengani Mlaliki 3:20, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Mogwirizana ndi lembali, n’chiyani chimene chimachitikira munthu amene wamwalira?

  • Kodi pali chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo munthu akamwalira?

Baibulo limatiuza zokhudza imfa ya Lazaro, yemwe anali mnzake wapamtima wa Yesu. Mukamawerenga Yohane 11:11-14, onani zimene Yesu ananena zokhudza zimene zinachitikira Lazaro atamwalira. Kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi Yesu anayerekezera imfa ndi chiyani?

  • Kodi zimene Yesu ananenazi zingatithandize bwanji kudziwa zimene zimachitikira munthu amene wamwalira?

  • Kodi inuyo mukuona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi ndi zomveka?

4. Kudziwa zenizeni zimene zimachitikira munthu amene wamwalira n’kothandiza

Tikadziwa zoona zenizeni zokhudza imfa, sitimaopa anthu amene anamwalira. Werengani Mlaliki 9:10, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi anthu amene anamwalira angatichitire zinthu zinazake zoopsa?

Kudziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya imfa kungatithandize kuti tisamakhulupirire bodza lakuti anthu amene anamwalira amafunika kuwalambira, kuwalemekeza kapenanso kuwachitira zinazake kuti asatipweteke. Werengani Yesaya 8:19 ndi Chivumbulutso 4:11, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji akaona munthu akulambira kapena kupempha chithandizo kwa munthu amene anamwalira?

Kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kumatithandiza kuti tisamachite nawo miyambo imene Yehova sasangalala nayo

5. Kudziwa zenizeni zokhudza imfa kumatitonthoza

Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti akadzamwalira adzalangidwa chifukwa cha zoipa zimene ankachita ali moyo. Koma n’zolimbikitsa kudziwa kuti palibe amene amazunzidwa akamwalira, ngakhalenso munthu amene anachita zinthu zoipa kwambiri. Werengani Aroma 6:7, kenako mukambirane funso ili:

  • Monga mmene tawerengera m’Baibulo, munthu amene wamwalira amakhala kuti wamasuka ku uchimo. Ndiye kodi mukuganiza kuti anthu amene anamwalira amazunzika chifukwa cha zinthu zoipa zimene anachita ali moyo?

Tikamudziwa bwino Yehova, m’pamene timazindikira kuti iye sangazunze anthu amene anamwalira. Werengani Deuteronomo 32:4 ndi 1 Yohane 4:8, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi mukuganiza kuti Mulungu amene ali ndi makhalidwe amene tawawerenga m’mavesiwa, angasangalale kuzunza anthu amene anamwalira?

  • Kodi mukuona kuti kudziwa zoona zokhudza anthu amene anamwalira n’kotonthoza? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZIMENE ENA AMANENA: “Ndimaona kuti ndikadzamwalira ndidzalangidwa.”

  • Kodi munthu wotereyu mungamuwerengere mavesi ati a m’Baibulo?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Munthu akamwalira sadziwa chilichonse. Anthu amene anamwalira sakhala akuzunzika kwinakwake ndiponso sangatichitire zinthu zoipa.

Kubwereza

  • Kodi n’chiyani chimene chimachitikira munthu amene wamwalira?

  • Kodi kudziwa zenizeni zokhudza imfa kumatithandiza bwanji?

  • Kodi kudziwa zenizeni zokhudza imfa kumatitonthoza bwanji?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene mawu akuti “nzimu” amatanthauza m’Baibulo.

“Kodi Munthu Akamwalira Mzimu Wake Umapitirizabe Kukhala Ndi Moyo?” (Nkhani yapawebusaiti)

Onerani vidiyo kuti muone ngati Mulungu amaotcha anthu ndi moto.

Kodi Mulungu Amaotcha Anthu Kumoto? 3:06

Kodi tiyenera kuopa akufa?

Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi? (kabuku)

Onani mmene kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kunathandizira munthu wina.

“Ndinapeza Mayankho Ogwira Mtima a Mafunso Anga” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2015)