Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 60

Pitirizani Kulimbitsa Ubwenzi Wanu Ndi Yehova

Pitirizani Kulimbitsa Ubwenzi Wanu Ndi Yehova

Pa nthawi yonse yomwe mwakhala mukuphunzira Baibulo, mwadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova. Zimene mwaphunzira zakuthandizani kuti muzimukonda kwambiri mpaka munasankha kudzipereka kwa iye ndiponso kubatizidwa. Koma ngati simunabatizidwe, mwina mukuganiza zoti mubatizidwe posachedwapa. Komabe ngakhale mutabatizidwa, mudzafunika kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Mukhoza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mpaka kalekale. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

1. N’chifukwa chiyani muyenera kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova?

Tonsefe tiyenera kumachita khama kuti tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Tiyenera kuchita zimenezi “kuti tisatengeke pang’onopang’ono” n’kusiya kumukhulupirira. (Aheberi 2:1) Ndiye n’chiyani chimene chingatithandize kuti tipitirize kutumikira Yehova mokhulupirika? Tingachite zimenezi poyesetsa kugwira ntchito yolalikira mwakhama ndi kupeza njira zina zowonjezera utumiki wathu. (Werengani Afilipi 3:16.) Palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kutumikira Yehova.​—Salimo 84:10.

2. Kodi muyeneranso kupitiriza kuchita chiyani?

Ngakhale kuti mwamaliza kuphunzira bukuli, koma pali zinthu zambiri zimene muyenera kupitiriza kuchita monga Mkhristu. Baibulo limanena kuti tiyenera “kuvala umunthu watsopano.” (Aefeso 4:23, 24) Mudzadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova ndi makhalidwe ake mukamapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupezeka pamisonkhano yampingo. Muziyesetsa kutsanzira makhalidwe a Yehova komanso kusintha moyo wanu n’cholinga choti musangalatse Yehova.

3. Kodi Yehova adzakuthandizani bwanji kuti mupitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba?

Baibulo limati: “Mulungu, . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.” (1 Petulo 5:10) Tonsefe timayesedwa kuti tichite zinthu zoipa. Koma Yehova amatipatsa zinthu zonse zofunikira kuti tisagonje pa mayesero. (Salimo 139:23, 24) Iye amalonjeza kuti adzakupatsani mphamvu komanso mtima wofunitsitsa kuti mupitirize kumutumikira mokhulupirika.​—Werengani Afilipi 2:13.

FUFUZANI MOZAMA

Onani zimene mungachite kuti mupitirize kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso mmene Yehova angakudalitsireni.

4. Musasiye kulankhulana ndi Yehova

Pofika pano, Yehova ndi mnzanu wapamtima chifukwa mwakhala mukupemphera ndi kuphunzira Baibulo. Kodi kupitiriza kuchita zimenezi kungakuthandizeni bwanji kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova?

Werengani Salimo 62:8, kenako mukambirane funso ili:

  • Kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova, kodi pali zinthu zimene mukuona kuti mungafunikire kusintha mukaganizira zimene mumamuuza m’pemphero?

Werengani Salimo 1:2, kenako mukambirane funso ili:

  • Kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova, kodi mungachite chiyani kuti kuwerenga Baibulo kuzikuthandizani kwambiri?

Kodi mungachite chiyani kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo? Kuti muone zimene zingakuthandizeni, onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

  • Pa mfundo zimene zatchulidwa muvidiyoyi, kodi ndi mfundo ziti zomwe mungakonde kuzigwiritsa ntchito?

  • Ndi nkhani ziti zomwe mungakonde kuphunzira?

5. Muzikhala ndi zolinga zowonjezera zomwe mumachita potumikira Yehova

Mungapitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mukamakhala ndi zolinga zowonjezera zomwe mumachita pomutumikira. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

  • Muvidiyoyi, kodi kukhala ndi zolinga zochita zambiri mu utumiki kunamuthandiza bwanji Cameron?

Si atumiki a Yehova onse amene angapite kudziko lina kukalalikira. Komabe, tonsefe tingathe kukhala ndi zolinga zochita zambiri mu utumiki. Werengani Miyambo 21:5, kenako muganizire zolinga zimene mungakonde kuzikwaniritsa . . .

  • mumpingo.

  • pantchito yolalikira.

Kodi mfundo yamulembali ingakuthandizeni bwanji kuti mukwaniritse zolinga zanuzo?

Zolinga zomwe mungakhale nazo

  • Kupereka mapemphero abwino kwambiri.

  • Kuwerenga Baibulo lonse.

  • Kudziwana ndi abale ndi alongo onse mumpingo wanu.

  • Kuyambitsa komanso kuchititsa phunziro la Baibulo.

  • Kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika.

  • Ngati ndinu m’bale, kuyesetsa kuti mukhale mtumiki wothandiza.

6. Mungakhale ndi moyo mpaka kalekale

Werengani Salimo 22:26, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungachite chiyani kuti mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Pitirizani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova ndiponso kukhala ndi zolinga zoti muchite zambiri potumikira Yehova. Mukatero, mukhoza kudzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

Kubwereza

  • N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti Yehova akuthandizani kupitiriza kumutumikira mokhulupirika?

  • Kodi mungalimbitse bwanji ubwenzi wanu ndi Yehova?

  • Kodi kukhala ndi zolinga zoti muchite zambiri potumikira Yehova kungakuthandizeni bwanji kuti mupitirize kukhala naye pa ubwenzi wolimba?

Cholinga Chimene Mukufuna Kudzakwaniritsa Chaka Chikubwerachi

ONANI ZINANSO

Kodi Yehova amaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani pakati pa kuchita zinthu mokhulupirika kamodzi kokha ndi kukhala wokhulupirika kwa moyo wonse?

Khalani Okhulupirika Ngati Abulahamu (9:20)

Ngakhale mtumiki wa Yehova wokhulupirika akhoza kusiya kukhala wosangalala potumikira Yehova. Onani zomwe mungachite kuti muyambirenso kusangalala.

Kusinkhasinkha Kungatithandize Kukhala Wosangalala (5:25)

Kodi mungatani kuti mukhale ndi zolinga zauzimu n’kumazikwaniritsa?

“Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu” (Nsanja ya Olonda, July 15, 2004)

N’chifukwa chiyani Mkhristu amafunika kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova, nanga angachite bwanji zimenezi?

“Yesetsani Kukula Mwauzimu Chifukwa ‘Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi’” (Nsanja ya Olonda, May 15, 2009)