Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ULENDO WOYAMBA

PHUNZIRO 1

Kuchita Chidwi ndi Anthu

Kuchita Chidwi ndi Anthu

Mfundo yaikulu: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.

Zomwe Yesu Anachita

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 4:6-9. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1.    Kodi Yesu anadziwa zotani zokhudza mayiyo asanayambe kucheza naye?

  2.   Yesu anati: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.” N’chifukwa chiyani imeneyi inali njira yabwino yoyamba kukambirana naye?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Zikhoza kutiyendera bwino kwambiri tikamakambirana ndi anthu nkhani yomwe angachite nayo chidwi.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzikhala okonzeka kusintha. Musamakakamire kuti muyambe kukambirana ndi munthu nkhani yokhayo yomwe mwakonzekera. Mungayambe ndi kukambirana nkhani ina yomwe ili m’kamwam’kamwa. Dzifunseni kuti:

  1.    ‘Kodi munyuzi mwalembedwa nkhani yanji?’

  2.   ‘Kodi maneba anga, anzanga a kuntchito kapena anzanga a kusukulu akulankhula zotani?’

4. Muzichita chidwi. Dzifunseni kuti:

  1.    ‘Kodi munthuyu akutani? Kodi angakhale kuti akuganiza chiyani?’

  2.   ‘Kodi zomwe wavala, mmene akuonekera kapena mmene pakhomo pake palili zikundiuza chiyani zokhudza chikhalidwe chake komanso zomwe amakhulupirira?’

  3.   ‘Kodi ino ndi nthawi yabwino yoti ndicheze naye?’

5. Muzimvetsera.

  1.    Musamalankhule kwambiri.

  2.   Muzimupatsa mpata wofotokoza maganizo ake. Ngati ndi zotheka, mukhoza kumufunsa mafunso.