ULENDO WOYAMBA
PHUNZIRO 5
Kulankhula Mwaluso
Mfundo yaikulu: “Mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima.”—Akol. 4:6.
Zomwe Paulo Anachita
1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 17:22, 23. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:
-
Kodi Paulo anamva bwanji ataona miyambo ya chipembedzo chonyenga ku Atene?—Onani Machitidwe 17:16.
-
M’malo mowadzudzula, kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji zomwe anthuwa ankakhulupirira kuti akwanitse kuwalalikira?
Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo
2. Tikamasankha bwino zoti tilankhule, mmene tingazilankhulire komanso nthawi yoti tizilankhule, tidzathandiza anthu kufunitsitsa kumvetsera uthenga wathu.
Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo
3. Muzisankha mawu mosamala. Mwachitsanzo, polankhula ndi munthu amene si Mkhristu, muyenera kusankha mawu abwino mukamanena za Baibulo kapena zokhudza Yesu.
4. Musamamudule mawu. M’patseni mpata wolankhula za kumtima kwake. Ngati atalankhula zina zake zomwe sizikugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, musamutsutse. (Yak. 1:19) Mukamamumvetsera pomwe akulankhula, ndi pamene mumamvetsa bwino maganizo ake.—Miy. 20:5.
5. Muzivomerezana naye komanso kumuyamikira pa mfundo zina. Akhoza kukhala wotsimikiza kuti zomwe chipembedzo chake chimakhulupirira ndi zolondola. Yambani ndi kukambirana zinthu zomwe mungagwirizane. Pomwe nthawi ikupita mungamuthandize kumvetsa mfundo zina za m’Baibulo.