Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO B

Kusiya Kukambirana ndi Munthu

Kusiya Kukambirana ndi Munthu

Ngati munthu sakuvomereza mfundo inayake kapena akufunsa kuti adziwe bwino zina zake, timakhala okonzeka kumuthandiza. Timafuna tizikambirana ndi anthu omwe ali ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.”​—Mac. 13:48.

Koma bwanji ngati ndi waukali, akungofuna zokangana kapenanso sakufuna kuti ticheze naye? Tingasiye kukambirana naye, modekha komanso mwaulemu. (Miy. 17:14) Ngati titasiyana naye bwino, zingakhale zosavuta kudzachezanso naye m’tsogolo.​—1 Pet. 2:12.