Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 10

Kodi Anthu Omvera Mulungu Adzalandira Madalitso Otani?

Kodi Anthu Omvera Mulungu Adzalandira Madalitso Otani?

Ambiri mwa anthu amene anamwalira adzaukitsidwa padziko lapansi. Machitidwe 24:15

Pali madalitso ambiri amene mudzalandire m’tsogolo muno ngati mukumvera Yehova. Mudzakhala ndi thanzi labwino ndipo palibe amene adzadwale, kulumala kapena kukalamba. Mudzatha kukhulupirira munthu aliyense chifukwa sikudzakhala anthu oipa.

Sikudzakhala zinthu zilizonse zopweteka, chisoni kapenanso kulira. Palibe amene adzakalambe ndi kufa.

Mudzasangalala kukhala pamodzi ndi anzanu komanso achibale anu ndipo moyo udzakhala wosangalatsa kwambiri m’Paradaiso.

Anthu adzakhala mopanda mantha ndipo adzakhaladi osangalala.

Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onse. Chivumbulutso 21:3, 4