Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 1

Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?

Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?

Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo. 2 Timoteyo 3:16

Mulungu woona anathandiza anthu kuti alembe maganizo ake m’buku limodzi lopatulika. Buku limeneli ndi Baibulo. M’Baibulo muli zinthu zofunika kwambiri zimene Mulungu amafuna kuti muzidziwe.

Mulungu amadziwa zinthu zimene zingatithandize, ndipo iye ndi amene angatipatse nzeru. Choncho ife tingakhale anzeru tikamamvetsera zimene akunena.​—Miyambo 1:5.

Mulungu amafuna kuti munthu aliyense padziko lapansi aziwerenga Baibulo. Ndipo masiku ano Baibulo likupezeka m’zinenero zambirimbiri.

Ngati mukufuna kumvera Mulungu, muyenera kuwerenga Baibulo ndi kulimvetsa bwino.

Padziko lonse, anthu akumvetsera zimene Mulungu akunena. Mateyu 28:19

Anthu a Mboni za Yehova angakuthandizeni kuti mulimvetse bwino Baibulo.

Padziko lonse lapansi, iwo amaphunzitsa choonadi chonena za Mulungu.

Maphunziro amenewa ndi aulere. Mungathe kuphunziranso za Mulungu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova imene ikupezeka kwanuko.