Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 4

Kodi Makolo Athu Ali Kuti?

Kodi Makolo Athu Ali Kuti?

1, 2. Kodi ambiri amakhulupirira chiyani za akufa?

ANTHU ambiri mu Africa muno amakhulupirira kuti imfa si mapeto a moyo koma kuti munthu akafa amangosamuka kukakhala ndi moyo kwina. Ambiri amaganiza kuti makolo awo amene anamwalira anasamuka kuchoka m’dzikoli kupita kudziko losaoneka, kusiya dziko la anthu kupita kudziko la mizimu.

2 Amakhulupirira kuti makolo ameneŵa, kapena kuti mizimu ya makolo, imateteza achibale awo padziko lapansi ndi kuwadalitsa kuti azikhala ndi moyo wamtendere. Malinga ndi zimene amakhulupirirazi, mizimu ya makolo ndi mabwenzi amphamvu amene akhoza kuwapatsa chakudya chochuluka, thanzi, ndi kuwateteza ku ngozi. Amati ngati saisamala kapena akaiputa, imadzetsa masoka monga matenda, umphaŵi, ndi mavuto.

3. Kodi anthu ena amalambira bwanji makolo?

3 Amoyo amachita miyambo yosiyanasiyana kulemekeza mizimu ya makolo kuti ubale wawo ndi mizimuyo ukhale wabwino. Zimenezi zimaonekera makamaka m’miyambo ya maliro, monga kuchezera pamaliro ndi mwambo umene ena amati kuika maliro kachiŵiri. Kulambira makolo kumaonekeranso mwanjira zina. Mwachitsanzo, ena pofuna kumwa moŵa amayamba athirako wina pansi kupatsako mizimu ya makolo. Ndiponso, akaphika chakudya, amasiyako china mu mphika kuti mizimu ya makolo ikafika ipeze chakudyacho.

4. Kodi anthu ambiri amakhulupirira zoti chiyani pa nkhani ya mzimu?

4 Anthu ena amakhulupirira kuti amoyo ali ndi mzimu wosafa umene umapulumuka thupi likafa. Amakhulupirira kuti ngati munthu ali wabwino, mzimu wake umapita kumwamba, kapena ku paradaiso, koma ngati ali woipa, mzimu wake umapita ku helo. Anthu amaphatikiza mfundo imeneyi ndi zikhulupiriro za makolo awo. Mwachitsanzo, padanga la maliro m’nyuzipepala pamene amalengeza za mwambo woika maliro wochitikira m’tchalitchi, nthaŵi zina amanenanso kuti wakufayo “wasamukira kudziko lina” kapena kuti “wapita ku mizimu ya makolo.” Maziko a zimene amakhulupirirazi ndiyo mfundo yakuti mzimu umapulumuka thupi likafa. Nanga Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

Kodi Mzimu N’Chiyani?

5. Malinga ndi Baibulo, kodi mzimu ndi chiyani?

5 Kuphunzira Baibulo mosamalitsa kumasonyeza kuti mawu oyambirira a Chihebri ndi Chigiriki amene nthaŵi zambiri amawamasulira kuti “mzimu” ali ndi matanthauzo ambiri. Mawu onsewo amatanthauza chinthu chimene anthu satha kuchiona koma umboni wake ulipo wakuti ndi mphamvu yogwira ntchito. Mawu ameneŵa amagwira ntchito potchula (1) mphepo; (2) mphamvu ya moyo yogwira ntchito mwa anthu ndi nyama; (3) mphamvu imene ili mumtima wophiphiritsa wa munthu ndipo imam’limbikitsa kulankhula ndi kuchita zinthu mwanjira inayake; (4) mizimu; ndi (5) mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito, kapena kuti mzimu woyera. Ameneŵa ndi ena a matanthauzo a liwu lakuti “mzimu” lopezeka m’Baibulo.

6. Kodi mzimu umene uli mwa anthu n’chiyani?

6 Choncho tikuona kuti Baibulo likamatchula mzimu umene uli mwa anthu, limatanthauza mphamvu ya moyo yosaoneka imene imatheketsa anthu kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene amoyo amachita. Mzimu umenewo uli ngati magetsi. Magetsi amayendetsa fani kapena kuliza wailesi koma satha mwa iwo okha kukankha mpweya kapena kutulutsa mawu. N’chimodzimodzinso ndi mzimu wathu. Umatithandiza kuona, kumva, ndi kuganiza. Koma paokha mzimuwo sutha kuchita zimenezi popanda maso, makutu, kapena ubongo.

7. Kodi chimachitika n’chiyani mzimu ukaleka kugwira ntchito m’thupi?

7 Ndiye, munthu aliyense ali ndi mphamvu ya moyo, kapena kuti mzimu, umene umachirikiza moyo wake. Kuti mphamvu ya moyo imeneyi igwire ntchito, imathandizidwa ndi kupuma koma sindiyo kupumako. M’malo mwake, ndiyo nyonga ya moyo yopezeka m’selo iliyonse m’thupi la munthu. Mphamvu ya moyo imeneyi ikaleka kugwira ntchito m’thupi, thupilo limafa. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Thupi lopanda mzimu lili lakufa.”​—Yakobo 2:26.

8. Kodi chimachitikira zotsimikiza mtima za munthu n’chiyani mphamvu ya moyo wake ikaleka kugwira ntchito m’thupi lake?

8 Ndiponso Baibulo limafotokoza kuti munthu akamwalira, si thupi lokhalo limene limafa ayi. Poyamba kuŵerenga Salmo 146:4, timapeza kuti pamene ‘mpweya [“mzimu,” NW] wa munthu uchoka’​—kutanthauza kuti waleka kugwira ntchito​—iye “abwerera kumka ku nthaka yake,” ndiko kuti, thupi limabwerera kufumbi. Koma onani kuti lembalo likupitiriza kuti: “Tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”

9. Kodi mzimu suutha kuchita chiyani?

9 Choncho malinga ndi Baibulo, munthu akamwalira, mzimu kapena kuti mphamvu ya moyo, suuchoka m’thupi ndi kukakhalabe ndi moyo kudziko la mizimu. Motero munthu akamwalira, mzimu suutha kuchita kalikonse monga kutidalitsa, kutiopsa, kapena kutipweteka.

Mmene Akufa Alili

10. Kodi Baibulo limati chiyani za mmene akufa alili?

10 Nangano ndi motani mmene akufa alili? Popeza Yehova ndiye analenga anthu, amadziŵanso zimene zimatichitikira tikamwalira. Mawu ake amaphunzitsa kuti akufa alibe moyo, satha kumva, kuona, kulankhula, kapena kuganiza kanthu. Baibulo limati:

  • “Akufa sadziŵa kanthu bi.”​—Mlaliki 9:5.

  • “Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano.”​—Mlaliki 9:6.

  • ‘Kulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.’​—Mlaliki 9:10.

11. Adamu atachimwa, kodi Yehova anati chiyani kwa iye?

11 Taganizani zimene Baibulo limatiuza za Adamu, kholo lathu loyamba. Yehova anamuumba “ndi dothi lapansi.” (Genesis 2:7) Adamu akanamvera lamulo la Yehova, akanakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi mosangalala. Koma iye anaswa lamulo la Yehova, ndipo analandira chilango cha imfa. Nanga kodi Adamu anapita kuti atamwalira? Mulungu anamuuza kuti: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”​—Genesis 3:19.

12. Kodi chinamuchitikira Adamu n’chiyani atamwalira?

12 Kodi Adamu anali kuti Yehova asanamulenge ndi dothi? Sanali kwina kulikonse. Inde, kunalibe. Ndiye, mmene Yehova anati Adamu ‘adzabwerera kunthaka,’ anatanthauza kuti Adamuyo adzakhala wopanda moyo, ngati fumbi. Adamu sanapitirize kukhala ndi moyo kudziko la mizimu. ‘Sanasamukire’ kudziko la mizimu ya makolo ayi. Sanapite kumwamba kapena ku helo. M’malo mwake, anakhalanso wopanda moyo muja zinalili poyamba; anasiya kukhalako.

13. Kodi chimachitikira anthu ndi nyama pa imfa n’chiyani?

13 Kodi zimenezi n’zimenenso zimachitikira anthu onse? Inde. Baibulo limati: “Onse [anthu ndi nyama] apita kumalo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”​—Mlaliki 3:19, 20.

14. Kodi akufa akuyembekeza chiyani?

14 Baibulo limalonjeza kuti Mulungu adzautsa akufa kukhalanso ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi pano. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Koma zimenezi zidzachitika m’tsogolo. Panopo, iwo ali m’tulo ta imfa. (Yohane 11:11-14) Choncho sitiyenera kuwaopa kapena kuwapembedza, popeza sangatithandize kapena kutipweteka.

15, 16. Kodi Satana amatani pofuna kuti anthu akhulupirire kuti akufa ali moyo?

15 Ganizo lakuti sitifa ayi ndi bodza limene Satana Mdyerekezi akufalitsa. Pofuna kuwatsimikiza anthu kuti akhulupirire bodza limeneli, iye ndi ziwanda zake amayesa kulimbikitsa anthu kuganiza kuti mizimu ya akufa ndi imene imadzetsa matenda ndi mavuto ena. N’zoona kuti mavuto ena amayamba ndi ziwanda. Ndiponso ena sayamba ndi ziwanda. Koma zakuti amene akugona mu imfa angatipweteke si zoona.

16 Palinso njira ina imene ziwanda zimayesetsera kulimbikitsa anthu kuganiza kuti zimene Baibulo limanena pa imfa n’zolakwika. Zimanyenga anthu kuti aganize kuti akuona munthu amene anafa uja kapena kulankhula naye. Ziwandazo zimatero kudzera m’masomphenya, maloto, obwebweta, kapena njira zina. Komabe, zimenezi zikamachitika anthuwo amakhala akulankhula ndi ziwanda zimene zimayerekeza kukhala ngati akufa aja; salankhula ndi anthu akufa ayi. Ndiye chifukwa chake Yehova amatsutsiratu obwebweta ndi aja ofunsira akufa.​—Deuteronomo 18:10-12; Zekariya 10:2.