Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHIGAWO 1

Kodi Zipembedzo Zonse Zimaphunzitsa Zoona?

Kodi Zipembedzo Zonse Zimaphunzitsa Zoona?

1. Kodi zina mwa zipembedzo zimene zili mu Africa muno n’ziti?

MU Africa muno, pafupifupi aliyense amavomereza kuti kulambira Mulungu n’kofunika. Koma tikafika pankhani ya kalambiridwe kake, anthu amasiyana maganizo kwambiri. Ena amakalambira kumsikiti, ndipo ena kukachisi wa makolo. Enanso amapita ku tchalitchi. Komano ngati munthu aganiza kuti mu Africa muno muli zipembedzo zitatu zokha basi, ameneyo waphonyetsa. Asilamu ena ali ndi malamulo ndi zikhulupiriro zosiyana ndi Asilamu anzawo. Zipembedzo za makolo zimasiyana malinga ndi malo. Matchalitchi amene amati ndi achikristu sagwirizana kwambiri. Kulikonse mu Africa muno kulinso timatchalitchi ting’onoting’ono tambirimbiri timene timayamba mwa kuchoka m’matchalitchi aakulu.

Chipembedzo Chathu Chifunika Kukhala Choona

2. (a) N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri anthu amasankha kukhala m’chipembedzo chawocho? (b) Ndi zifukwa ziti zimene si umboni wakuti Mulungu amakondwera ndi chipembedzo chathu?

2 N’chifukwa chiyani anthu amalambira mmene amachitiramu? Chifukwa chakuti ambiri amakonda zipembedzo za makolo awo. Ndiponso anthu masiku ano ali m’zipembedzo zawozo chifukwa cha zimene zinachitika kalekale. Buku lakuti The Africans​—A Triple Heritage limati: “Kumpoto kwa chipululu cha Sahara, Chisilamu chinafala mwa kugonjetsa adani ake, . . . ndipo kumwera kwa Sahara, Chikristu chinafala ndi njira yomweyonso. Pamene kumpoto kwa Sahara Chisilamu chinafala mwa kugwiritsa ntchito lupanga, kumwera kwa Sahara Chikristu chinafala mwa kugwiritsa ntchito mfuti.” Mulimonsemo, ambiri timaganiza kuti Mulungu amakondwera ndi chipembedzo chathu. Timatero chabe chifukwa chakuti mayi ndi bambo ali mmenemo kapena chifukwa chakuti boma lina kunja kwa dziko lathu linakakamiza makolo athu kalelo kuloŵa chipembedzo chimenecho. Koma zifukwazi sizipanga chipembedzo chathu kukhala choona ayi.

3-5. Ndi fanizo lotani limene likutithandiza kuona kuti si zipembedzo zonse zimene zikuphunzitsa zoona?

3 Ngakhale kuti zipembedzo zonse zimanena kuti n’zodalirika potsogolera anthu kupembedza Mulungu, zimasiyana zikhulupiriro zawo. Pankhani yakuti Mulungu ndani ndipo amafuna chiyani kwa ife, zimaphunzitsa zosiyana. Taganizani izi: Tinene kuti mwapeza ntchito pakampani inayake yaikulu. Mutapita kuntchito tsiku loyamba, mwapeza kuti bwana wanu kulibe ali patchuthi. Ndiye mukufunsa antchito atatu amene mwawapeza pamenepo kuti nanga mutani tsopano. Woyamba akukuuzani kuti bwana wanu akufuna kuti musese. Wachiŵiri akuti mupake penti nyumbayo. Ndipo wachitatu akuti mukhale wamtengatenga.

4 Inuyo mutamva zimenezo, mukuwafunsa za bwana wanu. Woyamba akuti bwana wanu ndi mnyamata wamtali, wovuta. Wachiŵiri akuti ndi wamfupi, wokalamba, wokoma mtima. Ndiye wachitatu uja akukuuzani kuti bwanayo si mwamuna ayi koma ndi mkazi. Mosakayika, mudzazindikira kuti antchito atatuwo sakukuuzani zoona onse. Ngati mukufuna kukhala pantchito yanu yatsopanoyo, simudzalephera kufufuza kuti mum’dziŵe bwana wanuyo ndi zimene akufuna kuti inuyo muchite.

5 Ndi mmenenso chipembedzo chakhalira. Popeza ambiri amakhulupirira zosiyanasiyana pankhani yakuti Mulungu ndani ndipo amafuna chiyani kwa ife, tifunika kuonetsetsa kuti kulambira kwathu ndi koona. Koma kodi tingatani kuti tidziŵe zoona zake za Mulungu?