Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 25

Banja Lisamukira ku Igupto

Banja Lisamukira ku Igupto

YOSEFE sakutha’nso kudziletsa. Akuuza atumiki ake onse kutuluka m’chipinda’cho. Ali yekha ndi abale ake’wo, akuyamba kulira. Tingayerekezere m’mene abale ake akudabwira, chifukwa sakudziwa chifukwa chake akulira. Potsiriza akuti: ‘Ndine Yosefe. Kodi atate ali moyo?’

Abale ake angofa chikakasi. Akuopa. Koma Yosefe akuti: ‘Idzani pafupi chonde.’ Atafika, akuti: ‘Ndine mbale wanu Yosefe amene munam’gulitsa kudza kuno ku Igupto.’

Yosefe akupitirizabe kulankhula mokoma mtima kuti: ‘Musadzikwiyira nokha kuti munandigulitsa kuno. Ndiye’di Mulungu ananditumiza ku Igupto kuno kudzapulumutsa miyoyo ya anthu. Farao wandipanga kukhala wolamulira wa dziko lonse. Tsono bwererani msanga kwa atate ndi kukawauza izi. Ndipo kawauzeni adze kudzakhala kuno.’

Ndiyeno Yosefe akukupatira abale ake, akufungatira ndi kuwapsyompsyona onse. Pomva Farao kuti abale a Yosefe abwera, akuuza Yosefe kuti: ‘Alole atenge magaleta napite kukatenga atate wao ndi mabanja ao nabwerere kuno. Ndidzawapatsa malo abwino kopambana m’Igupto monse.’

Ndizo zimene iwo anachita. Pano mukuona Yosefe akukumana ndi atate wake pamene afika ku Igupto ndi banja lao lonse.

Banja la Yakobo linali litakhala lalikulu kwambiri. Iwo onse anali 70 pamene anasamukira ku Igupto, kuwerengera iye ndi ana ake ndi zidzukulu. Koma panali’nso akazi, ndipo’nso mosakaikira atumiki ambiri. Onsewa anakhala mu Igupto. Iwo anachedwa Aisrayeli, chifukwa Mulungu anasintha dzina la Yakobo kukhala Israyeli. Israyeli anakhala anthu apadera kwa Mulungu, monga momwe tidzaonera kenako.