Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 33

Kuoloka Nyanja Yofiira

Kuoloka Nyanja Yofiira

TAONANI zimene zikuchitika! Ndi Mose uyo ndi ndodo yake yotansiridwa pa Nyanja Yofiira. Awo ali naye bwino lomwe’wo ku tsidya iro ndiwo Aisrayeli. Koma Farao ndi gulu lake lonse lankhondo akumizidwa m’nyanjamo. Tiyeni tione m’mene zinachitikira.

Monga momwe tinaphunzirira, Farao anauza Aisrayeli kuchoka ku Igupto Mulungu atadzetsa mliri wa 10 pa Aigupto. Amuna Achiisrayeli 600,000 ndi ana ndi akazi omwe anatuluka. Ndipo’nso chiwerengero chachikulu cha anthu ena, amene anakhulupirira Yehova, anatsagana ndi Aisrayeli. Onse anatenga nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zao popita.

Asananyamuke, iwo anapempha Aigupto zobvala ndi zinthu zopangidwa ndi golidi ndi siliva. Aigupto anali oopa kwambiri, chifukwa cha mliri womaliza’wo pa iwo. Chotero anawapatsa chiri chonse chimene iwo anapempha.

Patapita masiku owerengeka iwo anafika pa Nyanja Yofiira. Napuma pamenepo. Pa nthawi ino, Farao ndi anthu ake anayamba kumva chisoni kuti anawalola kupita. ‘Talola akapolo athu kupita!’ anatero.

Chotero Farao anaganiza’nso zina. Mwamsanga anakonza magaleta ake ankhondo ndi gulu la nkhondo. Nayambano kutsatira Aisrayeli ndi magaleta apadera 600, ndi magaleta ena onse a Igupto.

Aisrayeli poona Farao ndi magulu ake ankhondo akudza, anaopa kwambiri. Panalibe njira yothawira. Ku mbali ina kunali Nyanja Yofiira, ndipo kuno Aigupto analinkudza. Koma Yehova anaika mtambo pakati pa anthu ake ndi Aigupto. Chotero Aigupto sanali kuona Aisrayeli kuti awaukire.

Yehova anauzano Mose kutambasulira ndodo yake pa Nyanja Yofiira. Atatero, Yehova anachititsa chimphepo chochokera kum’mawa kuomba. Madzi a nyanja’yo anagawanitsidwa, nachita khoma mbali ndi mbali.

Aisrayeli anayamba kuyenda pouma kuoloka nyanja’yo. Kunatenga maola ambiri kuti anthu mamiliyoni’wo ndi zifuyo zao zonse afike ku tsidya lina’lo bwino lomwe. Kenako Aigupto anali okhoza kuwaona’nso. Akapolo ao anali kupita! Chotero analowa m’nyanjamo kuwathamangira.

Atatero, Mulungu anachititsa magudumu a magaleta ao kuguluka. Aigupto anaopa kwambiri nayamba kupfuula kuti: ‘Yehova kachiwiri’nso akumenyera nkhondo Aisrayeli. Tiyeni titulukemo!’ Koma kunali kochedwa kwambiri.

Ndipo pamene Yehova anauza Mose kutambasulira ndodo yake pa Nyanja Yofiira, monga munaonera m’chithunzi chija. Mose atatero, makoma a madzi anayamba kukumana namiza Aigupto ndi magaleta ao. Gulu lonse lankondo linali litatsatira Aisrayeli m’nyanjamo. Ndipo palibe mmodzi wa Aigupto’wo anatulukamo. wamoyo!

Ndi okondwa chotani nanga m’mene analiri anthu onse a Mulungu kukhala atapulumutsidwa! Iwo anayimba nyimbo yothokoza Yehova, nati: ‘Yehova wapeza chipambano chaulemerero. Wamiza m’nyanja akavalo ndi okwerapo.’ Mlongo wa Mose Miriamu anatenga lingaka lake, akazi onse nam’tsatira ndi malingaka ao. Pamene anayimba mosangalala, iwo anayimba nyimbo yofanana’yo imene amuna anayimba kuti: ‘Yehova wapambanatu. Waponya akavalo ndi owakwera ao m’nyanja.’