NKHANI 23
Maloto a Farao
ZAKA ziwiri zikupitapo, ndipo Yosefe akali m’ndende. Woperekera zakumwa uja sakum’kumbukira. Ndiyeno usiku wina Farao analota maloto awiri apadera kwambiri, ndipo sakudziwa matanthauzo ao. Mukumuona uyo ali mtulo? M’mawa mwake Farao akuitana anzeru ake nawauza zinthu zimene iye walota. Koma sakukhoza kumasulira maloto ake.
Wopereka zakumwa uja potsiriza akukumbukira Yosefe. Akuti kwa Farao: ‘Ndiri m’ndende munali munthu wokhoza kumasulira maloto.’ Yosefe akutulutsidwa m’ndende ndi Farao pa nthawi yomweyo.
Farao akuuza Yosefe maloto ake: ‘Ndinaona ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa, zokongola. Kenako ndinaona ng’ombe zoonda kwambiri zisanu ndi ziwiri. Ndipo zoonda’zo zinadya zonenepa’zo.
‘M’lachiwiri ndinaona ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu wakucha zinamera pa mbuwa. Kenako ndinaona ngala za tirigu zisanu ndi ziwiri zoonda ndi zouma. Ndipo ngala zoonda’zo zinayamba kumeza ngala zabwino zisanu ndi ziwiri’zo.
Yosefe akuti kwa Farao: ‘Maloto awiri’wo kumasulira kwake n’kumodzi. Ngombe zonenepa zisanu ndi ziwiri ndi ngala zakucha’zo zikutanthauza zaka zisanu ndi ziwiri, ng’ombe zisanu ndi ziwiri ndi ngala zoonda zisanu ndi ziwiri’zo zitanthauza zaka zina’nso zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala zaka zisanu ndi ziwiri za zakudya zochuluka m’Igupto. Ndiyeno padzakhala zaka zisanu ndi ziwiri za zakudya zochepa.
Tsono Yasefe akuuza Farao kuti: ‘Sankhani munthu wanzeru mumuike kuyang’anira kusonkhanitsa zakudya m’zaka zisanu ndi ziwiri zabwino’zo. Zikatero anthu sadzabvutika ndi njala m’zaka zoipa zosowa zakudya’zo.’
Farao akukonda lingaliro’lo. Akusankha Yosefe kusonkhanitsa zakudya, ndi kuzisunga. Pokhala wachiwiri, kwa Farao, Yosefe akukhala wofunika kopambana mu Igupto.
Zitapita zaka zisanu ndi zitatu, m’kati mwa njala, Yosefe akuona amuna ena akudza. Kodi mukuwadziwa? Eya, ndiwo akulu ake 10! Atate wao Yakobo wawatuma ku Igupto chifukwa analibe chakudya m’Kanani. Yosefe akudziwa abale ake, koma iwo sakum’dziwa. Kodi mukudziwa chifukwa chake? N’chifukwa chakuti Yosefe wakula kwambiri, ndipo wabvala zobvala za mtundu wina.
Yosefe akukumbukira kuti akali mnyamata analota abale akudza kudzam’gwadira. Kodi mukukumbukira kukhala mutawerenga za izo? Yosefe motero akuona kuti ndiye Mulungu anam’tumiza ku Igupto kaamba ka chifukwa chabwino. Kodi muganiza Yosefe akuchitanji? Tiyeni tione.