Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 2

Munda Wokongola

Munda Wokongola

ONANI pa dziko’pa! N’chokongola chotani nanga m’mene chiri chonse chiriri! Onani udzu ndi mitengo, maluwa n’zinyama zonse. Kodi njobvu ndi mikango ziripo?

Kodi munda wokongola’wu unakhalapo motani? Tiyeni tione.

Mulungu, anayamba wapanga nsipu wokuta dziko. Napanga’nso mitundu yonse ya tomera. Zomera’zi zimakongoletsa dziko. Zimatipatsa’nso zakudya zokoma.

Anapanga’nso nsomba zisambire m’madzi ndi mbalame ziuluke m’mwamba. Anapanga agalu, amphaka ndi akavalo, zinyama zazikulu n’zazing’ono. Kodi n’ziti zimene ziri pafupi ndi nyumba yanu? Kodi sitimakondwera kuti Mulungu anatipangira zonse’zi?

Potsiriza, anapanga mbali ina ikhale malo apadera kwambiri. Anawacha munda wa Edene. Anali abwino’di kotheratu. Chiri chonse chowazungulira chinali chokongola. Mulungu anafuna kuti dziko lonse likhale ngati munda wakongola’wu.

Koma onani’nso chithunzi cha munda’wu. Kodi mukudziwa chimene Mulungu anaona kukhala chikusowamo? Tiyeni tione.