Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 7

Munthu Olimba Mtima

Munthu Olimba Mtima

PAMENE anthu anayamba kuchuluka pa dziko, ambiri anachita zoipa ngati Kaini. Koma mmodzi anali wosiyana. Ndiye munthu’yu Enoke. Enoke anali munthu wolimba mtima. Anthu onse om’zungungulira anali kuchita zoipa kwambiri, koma iye anatumikirabe Mulungu.

Kodi mukudziwa chifukwa chake anthu kale’lo anachita zinthu zoipa zambiri? Taganiziranitu, kodi anachititsa Adamu ndi Hava kusamvera Mulungu ndi kudya chipatso choletsedwa ndi Mulungu ndani? Inde, anali mngelo woipa. Baibulo limam’cha Satana. Iye akuyesa kuipitsa ali yense.

Tsiku lina Yehova anauza Enoke kuuza anthu kanthu kena kamene sanafune kukamva. Ndiko: ‘Tsiku lina Mulungu adzaononga anthu onse oipa.’ Anthu’wo anaipidwa kumva izi. Iwo anayesa’di kum’pha. Chotero iye anafunikira kulimba mtima kwambiri kuti auze anthu’wo zodzachitidwa ndi Mulungu.

Mulungu sanalole kuti Enoke akhalitse pakati pa anthu oipa’wo. Iye anakhala ndi moyo zaka 365 zokha. Bwanji tikuti “zaka 365 zokha”? Chifukwa anthu m’nthawi’yo anali amphamvu kwambiri koposa tsopano ndipo anakhala ndi moyo kotalikirapo. Eya, mwana wa Enoke Metusela anakhala ndi moyo zaka 969!

Atafa Enoke, anthu’wo anaipira-ipira. Baibulo limati ‘chiri chonse chimene analingalira chinali choipa nthawi zonse,’ n’kuti ‘dziko lapansi linadzala chiwawa.’

Kodi mukudziwa chifukwa chake panali bvuto lalikulu pa dziko m’masiku’wo? N’chifukwa chakuti Satana anali ndi njira yatsopano yochititsira anthu kuchita zoipa. Tidzaphunzira za izi kenako.