Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 6

Mwana Wabwino, ndi Woipa

Mwana Wabwino, ndi Woipa

YANG’ANANI Kaini ndi Abele tsopano. Onse akula. Kaini wakhala mlimi. Iye amalima dzinthu ndi zipatso ndi ndiwo zamasamba.

Abele wakhala woweta nkhosa. Iye amakonda kusamalira ana a nkhosa. Iwo amakula kukhala nkhosa zazikulu, ndipo chotero Abele posapita nthawi akukhala ndi gulu la nkhosa loliyang’anira.

Tsiku lina Kaini ndi Abele akudza ndi mphatso kwa Mulungu. Kaini akudza ndi zakudya zimene walima. Abele akudza ndi nkhosa yake yabwino kopambana. Yehova akukondwera ndi Abele ndi mphatso yake. Koma sakukondwera ndi Kaini ndi mphatso yake. Kodi mukudziwa chifukwa chake?

Si ubwino wokha wa mphatso ya Abele koposa ya Kaini. N’chifukwa cha ubwino wa Abele. Amakonda Yehova ndi mbale wake. Koma ngwoipa; samakonda mbale wake.

Mulungu akuuza Kaini kusintha. Koma Kaini sakumvetsera. Iye wakwiya kwambiri chifukwa chakuti Mulungu anakonda kwambiri Abele. Chotero Kaini akuti ‘Tiye tipite kumunda.’ Kumene’ko ali okha, Kaini akumenya Abele. Akum’menya zolimba mpaka kumupha. Kodi izi sizinali zoopsya?

Ngakhale Abele anafa, Mulungu akum’kumbukirabe. Iye anali wabwino, ndipo Yehova samaiwala munthu wabwino wonga iye. Tsiku lina Yehova adzaukitsa Abele. Pa nthawi’yo sadzafa’nso. Adzakhala pa dziko pano kosatha. Kodi sikudzakhala kwabwino kudziwa anthu onga iyeyo?

Koma Mulungu samakondwera ndi anthu onga Kaini. Chotero Kaini atapha mbale wake, Mulungu anam’langa mwakum’thamangitsa kwa abale ake. Atachoka kukakhala kwina, anatenga mmodzi wa alongo ake, nam’kwatira.

Kenako Kaini ndi mkazi wake anabala ana. Ana ena amuna ndi akazi a Adamu anakwatirana, nawo’nso anabala ana. Posakhalitsa panali anthu ambiri pa dziko. Tiyeni tiphunzire za ena a iwo.