Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 9

Nowa Akhoma Chingalawa

Nowa Akhoma Chingalawa

NOWA anali ndi mkazi ndi ana amuna atatu. Maina a ana’wo anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Ali yense wa iwo anali ndi mkazi. Chotero munali anthu asanu ndi atatu m’banja la Nowa.

Mulungu tsopano anafuna kuti Nowa achite kanthu kachilendo. Anamuuza kukhoma chingalawa. Chingalawa’chi chinali ngati sitima, koma chinaoneka ngati chibokosi chachitali. ‘Uchipange cha zipinda zosanja zitatu,’ anatero Mulungu, ‘nupangemo zipinda.’ Zipinda zinali za Nowa ndi banja lake, zinyama ndi zakudya zao zofunika.

Mulungu anauza’nso Nowa kuchipanga kuti chisalowe madzi. Iye anati: ‘Ndidzadzetsa chigumula chachikulu ndi kuononga dziko lonse. Ali yense wosakhala m’chingalawa adzafa.’

Nowa ndi ana ake anamvera Yehova nayamba kukhoma’ko. Koma anthu ena ankangoseka. Anaipabe chiipire. Palibe aliyense anakhulupirira Nowa pamene anawauza zimene Mulungu adzachita.

Kunatenga nthawi yaitali kukhoma chingalawa’cho chifukwa chinali chachikulu kwambiri. Pambuyo pa zaka zambiri chinatha. Tsopano Mulungu anauza Nowa kulowetsamo zinyama. Anati alowetsemo ziwiri-ziwiri za mitundu ina, zazimuna ndi zazikazi zomwe. Koma mitundu ina, Mulungu anauza Nowa kulowetsamo zisanu ndi ziwiri. Mulungu anamuuza’nso kulowetsamo mitundu yonse ya mbalame. Nowa anachita’di zonenedwa ndi Mulungu’zo.

Kenako, Nowa ndi banja lake nawo’nso analowa m’chingalawa. Mulungu natseka chitseko. Alimo, Nowa ndi banja lake anayembekeza. Tayerekezerani muli m’chingalawa’cho, mukuyembekezera nawo. Kodi kudzakhala’di chigumula monga momwe ananenera Mulungu?