Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 112

Chombo Chinasweka pa Chisi

Chombo Chinasweka pa Chisi

TAONANI! bwato’lo likubvutika! Likusweka! Kodi mukuona anthu amene alumphira m’madzi’wo? Ena akusambira kuolokera pa mtunda. Kodi uyo ali apo’yo ndi Paulo? Tiyeni tione chimene chikum’chitikira?

Pajatu, kwa zaka ziwiri Paulo akusungidwa m’ndende m’Kaisareya. Ndiyeno iye ndi akaidi ena akuikidwa m’bwato, ndipo akuyamba ulendo wa ku Roma. Akudutsa pafupi ndi chisi cha Krete, pfunde loopsya likuwamenya. Mphepo ikuomba mwamphamvu kwambiri kwakuti amuna’wo sakutha kupalasa bwato’lo. Ndipo sakutha kuona dzuwa usana kapena nyenyezi usiku. Potsirizira pake, pambuyo pa masiku ambiri, onse okweramo akutaya mtima ponena za kupulumuka.

Ndiyeno Paulo akuimirira nati: ‘Palibe ali yense wa inu adzataya moyo wake; bwato lokha lidzatayika. Pakuti usiku watha’wu mngelo wa Mulungu anandidzera nati: “Usaope, Paulo! Uyenera kuima pamaso pa wolamulira Wachiroma Kaisara. Ndipo Mulungu adzapulumutsa onse amene ukuyenda nawo m’bwato’wo.”’

Pofika pakati pa usiku tsiku la 14 chiyambire pamene namondwe’yo anayamba, amalinyero’wo akuona kuti madzi’wo akukhala osaya kwambiri! Chifukwa cha kuopera kugunda miyala usiku, akuponya anagula ao. M’mawa mwake iwo akuona mtunda. Iwo akulingalira za kuyesa kupalasa bwato’lo kumka ku gombe’ko.

Ndiyeno, pofika pafupi ndi gombe’lo, bwato’lo likugunda pa mchenga osayenda’nso. Ndiyeno mapfunde anayamba kulimenya, ndipo linayamba kusweka. Mkulu wa nkhondo woyang’anira’yo akuti: ‘Inu nonse amene mungathe kusambira lumphirani m’madzi choyamba nimusambire kumka ku gombe. Enanu muwatsatire ndi kugwira zidutswa za bwato’lo.’ Ndipo ndizo zimene iwo akuchita. Motere anthu onse 276 amene analimo akufika bwino lomwe ku gombe, monga momwe’di mngelo’yo analonjezera.

Chisi’cho chikuchedwa Melita. Anthu’wo ngokoma mtima kwambiri, ndipo akusamalira onse ochokera m’bwato’lo. Pamene pakugwa bata, Paulo akuikidwa m’bwato lina namka naye ku Roma.