Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 113

Paulo m’Roma

Paulo m’Roma

MUKUONA maunyolo’wo pa Paulo, ndipo onani msilikali wom’londera’yo. Paulo ndi mkaidi m’Roma. Iye akuyembekezera kuti Kaisara asankhe chom’chitira. Ali mkaidi, anthu akuloledwa kum’zonda.

Atakhala masiku atatu m’Roma iye akutumiza mau kwa atsogoleri Achiyuda kudzamuona. Chifukwa cha ichi, Ayuda ambiri m’Roma akudza. Iye akuwalalikira za Yesu ndi ufumu wa Mulungu. Ena akukhulupirira nakhala Akristu, koma ena sakukhulupirira.

Iye akulalikira’nso kwa asilikali osiyana-siyana om’londera. Zaka ziwiri zimene iye akusungidwa muno monga wandende akulalikira kwa ali yense wothekera. Chotero, ngakhale a m’nyumba ya Kaisara akumva za mbiri yabwino yonena za Ufumu, ndipo ena a iwo akukhala Akristu.

Kodi mlendo akulemba pa thebulo’yu ndani? Kodi mungamuyerekezere? Inde, ndiye Timoteo. Naye’nso anali m’ndende kaamba ka kulalikira za Ufumu, koma wamasulidwa. Ndipo wadza kuno kudzathandiza Paulo. Kodi mukudziwa zimene iye akulemba? Tiyeni tione.

Kodi mukukumbukira mizinda’yo Filipo ndi Efeso m’Nkhani 110? Paulo anathandiza kuyambitsa mipingo Yachikristu m’mizinda’yo. Tsopano, ali m’ndende, akulembera makalata kwa Akristu’wa. Makalata’wo ali m’Baibulo, ndipo iwo onse akuchedwa Aefeso ndi Afilipi. Paulo tsopano akuuza Timoteo zoti alembere mabwenzi ao Achikristu m’Filipi.

Afilipi akhala om’komera mtima kwambiri. Iwo anam’tumizira mphatso m’ndende muno, ndipo chotero iye akuwathokoza. Epafrodito ndiye amene anadza nayo. Koma anadwala kwambiri kutsala pang’ono kufa. Tsopano iye ali bwino ndi wokonzekera kumka kwao. Iye adzatenga kalata ya Paulo ndi Timoteo pobwerera ku Filipi.

Akali m’ndende Paulo akulemba makalata ena awiri amene tiri nao m’Baibulo. Imodzi iri ya kwa Akristu a m’Kolose. Kodi mukudziwa chimene iyo ikuchedwa? Akolose. Ina ya kwa bwenzi lake lokondedwa Filemoni amene’nso amakhala m’Kolose. Iyo ndi yonena za Onesimo mtumiki wa Filemoni.

Onesimo anathawa kwa Filemoni namka ku Roma. Mwa njira ina iye anamva za kukhala m’ndende kwa Paulo munomo. Iye anadza kudzam’zonda, ndipo Paulo anam’lalikira. Posakhalitsa naye’nso anakhala Mkristu. Tsopano Onesimo ali ndi chisoni kuti anathawa. Chotero kodi mukudziwa zimene Paulo akulembera Filemoni m’kalata’yi?

Paulo akupempha Filemoni kukhululukira Onesimo. ‘Ndikum’bwezera kwa iwe,’ akutero Paulo. ‘Koma tsopano sali mtumiki wako chabe. Iye ali’nso mbale Wachikristu wabwino kwambiri.’ Pamene Onesimo akubwerera ku Kolose akumka ndi makalata awiri’wa, imodzi ya kwa Akolose ndi ina ya kwa Filemoni. Tingayerekezere m’mene Filemoni analiri wachimwemwe kumva kuti mtumiki wake anakhala Mkristu.

Pamene Paulo akulembera Afilipi ndi Filemoni, ali ndi mbiri yabwino kweni-kweni. ‘Ndikutumiza Timoteo kwa inu,’ akuuza motero Afilipi. ‘Koma’nso ine ndidzakuonani posachedwa.’ Ndipo Filemoni akum’lembera kuti, ‘Undikonzere malo odzakhalamo kumene’ko.’

Atamasulidwa Paulo akuzonda abale ndi alongo ake Achikristu m’malo ambiri. Koma pambuyo pake iye akumangidwa’nso m’Roma. Pa nthawi ino iye akudziwa kuti adzaphedwa. Chotero iye akulembera kalata Timoteo ndi kum’pempha kudza msanga. ‘Ndakhala wokhulupirika kwa Mulungu,’ akulemba motero Paulo, ‘ndipo Mulungu adzandipfupa.’ Zaka zowerengeka pambuyo pa kuphedwa kwa Paulo, Yerusalemu akuonongedwa kachiwiri, pa nthawi ino ndi Aroma.

Koma m’Baibulo muli zochuluka. Yehova Mulungu akuchititsa mtumi Yohane kulemba bukhu lotsirizira, kuphatikizapo bukhu la Chibvumbulutso. Bukhu la Baibulo limene’li limanena za m’tsogolo. Tiyeni tsopano tiphunzire zimene ziri m’tsogolo.