Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 110

Timoteo—Wothandiza Paulo

Timoteo—Wothandiza Paulo

MNYAMATA mukumuona pano’yu ali ndi mtumwi Paulo ndiye Timoteo. Iye amakhala ndi a banja lake mu Lustra. Mai wake amachedwa Yunike ndi gogo wake Loisi.

Kano n’kachitatu kwa Paulo kufika m’Lustra. Pafupi-fupi chaka chimodzi chapita’cho, Paulo ndi Barnaba anadza koyamba kuno kudzalalikira. Ndipo tsopano Paulo wabwera’nso ndi bwenzi lake Sila.

Kodi mukudziwa zimene Paulo akulankhula ndi Timoteo? Iye akufunsa kuti, ‘Kodi ungakonde kutsagana ndi Sila ndi ine? Tingakugwiritsire ntchito kutithandiza m’kulalikira anthu a ku malo akutali.’

Timoteo akuyankha kuti, ‘Inde, ndikakonda kupita.’ Chotero mwamsanga pambuyo pake Timoteo akusiya banja lake natsagana ndi Paulo ndi Sila. Koma tisanaphunzire za ulendo wao, tiyeni tione zimene zikuchitikira Paulo. Papita zaka 17 chiyambire pamene Yesu anamuonekera pa njira ya ku Damasiko.

Pajatu, iye anadza ku Damasiko kudzabvutitsa ophunzira a Yesu, koma tsopano iye mwini’yo ndi wophunzira! Kenako adani ena akulinganiza kum’pha chifukwa chakuti sakukonda kuphunzitsa kwake za Yesu. Koma ophunzira akum’thandiza kupulumuka. Iwo akumuika mu mtanga ndi kum’tsitsira kunja kwa malinga a mzinda.

Pambuyo pake iye akumka ku Antiokeya kukalalikira. N’kunoko kumene atsatiri a Yesu choyamba akuchedwa Akristu. Ndiyeno Paulo ndi Barnaba akutumizidwa ku Antiokeya pa ulendo wokalalikira ku maiko akutali kwambiri. Umodzi wa mizinda imene iwo akufika’ko ndiwo Lustra, kwao kwa Timoteo.

Tsopano, chaka chimodzi pambuyo pake, Paulo wafika’nso ku Lustra pa ulendo wachiwiri. Pamene Timoteo akutsagana ndi Paulo ndi Sila, kodi mukudziwa kumene iwo akupita? Yang’anani pa mapu’po, ndipo tiyeni tiphunzire ena a malo’wa.

Choyamba, iwo akumka ku Ikoniya wapafupi’yo, kenako ku mzinda wachiwiri wochedwa Antiokeya. Pambuyo pake akumka ku Trowa, ndiyeno n’kupita ku Tesalonika ndi Bereya. Kodi mukuona Atene pa mapu’po? Paulo akulalikira kumene’ko. Pambuyo pake akutha chaka ndi theka akulalikira m’Korinto. Potsirizira pake akuima kaye pang’ono mu Efeso. Ndiyeno akubwerera’nso pa bwato ku Kaisareya, nayenda kumka ku Antiokeya, kumene Paulo akukhala.

Chotero Timoteo akuyenda mamailo mazana-mazana kumka nathandiza Paulo kulalikira “mbiri yabwino” ndi kuyambitsa mipingo yambiri Yachikristu. Mukadzakula, kodi mudzakhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu monga Timoteo?