Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 86

Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi

Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi

KODI mukuona nyenyezi yowala’yo imene amuna’wa akuiloza? Pamene ananyamuka m’Yerusalemu, nyenyezi’yo inaoneka. Amuna’wa ngochokera Kum’mawa, ndipo iwo amaphunzira nyenyezi. Iwo amakhulupirira kuti nyenyezi yatsopano’yi ikuwatsogolera kwa wina wake wofunika.

Pamene amuna’wo akufika ku Yerusalemu, iwo anafunsa kuti: ‘Kodi ali kuti mwana amene adzakhala mfumu ya Ayuda?’ “Ayuda” ndi dzina lina la Aisrayeli. ‘Tinayamba kuona nyenyezi ya mwana’yo tikali Kum’mawa,’ anatero amuna’wo, ndipo tadza kudzam’lambira.’

Herode, amene ali mfumu pa Yerusalemu, pomva izi, anabvutika maganizo. Iye sanafune kuti mfumu ina itenge malo ake. Chotero iye anaitana akulu ansembe nawafunse kuti: ‘Kodi mfumu yolonjezedwa’yo idzabadwira kuti’ Iwo akuyankha kuti: ‘Baibulo limati m’Betelehemu.’

Chotero Herode anaitana amuna Akum’mawa’wo, nati nawo: ‘Mukani mukafune-fune kamwana’ko. Mutakapeza, zandidziwitseni. Nane’nso ndikufuna kumka kukakalambira.’ Koma, kweni-kweni, Herode anafuna kupeza mwana’yo ndi kum’pha!

Ndiyeno nyenyezi’yo ikuyenda patsogolo pa amuna’wo kumka ku Betelehemu, ndipo ikuima pa malo pamene pali mwana’yo. Atalowa m’nyumbamo amuna’wo, akupezamo Mariya ndi mwana’yo Yesu. Iwo akutulutsa mphatso nazipereka kwa Yesu. Koma kenako Yehova akuwachenjeza m’kulota kusabwerera kwa Herode. Chotero akubwerera kwao pa njira ina.

Herode atamva kuti amuna a Kum’mawa aja abwerera kwao, akupsya mtima kwambiri. Chotero akulamula kuti ana amuna onse m’Betelehemu a zaka ziwiri ndi zocheperapo aphedwe. Koma Yehova akuchenjeza Yosefe pasadakhale m’kulota, ndipo Yosefe ndi banja lake akuchoka kumka ku Betelehemu. Kenako, Yosefe atamva kuti Herode wafa, akutenga Mariya ndi Yesu nabwerera ku Nazarete kwao. Kuno ndiko kumene Yesu anakulira.

Kodi muganiza kuti ndani amene anapangitsa nyenyezi yatsopano’yo kuwala? Pajatu, choyamba amuna’wo anamka ku Yerusalemu ataona nyenyezi’yo. Satana Mdierekezi anafuna kupha Mwana wa Mulungu, ndipo anadziwa kuti Mfumu Herode ya Yerusalemu ikayesa kum’pha. Chotero Satana ndiye amene ayenera kukhala atapangitsa nyenyezi’yo kuwala.