Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 95

Kaphunzitsidwe ka Yesu

Kaphunzitsidwe ka Yesu

TSIKU lina Yesu akuuza munthu wina kuti ayenera kukonda mnansi wake. Munthu’yo akufunsa Yesu kuti: ‘Ndani amene ali mnansi wanga?’ Eya, Yesu akudziwa zimene iye akuganiza. Munthu’yo akuganiza kuti anthu a pfuko lake okha ndi chipembedzo ndiwo anansi ake. Chotero tiyeni tione zimene Yesu akunena naye.

Nthawi zina Yesu amaphunzitsa mwa kunena nthano. Ndizo zimene iye akuchita tsopano. Akusimba za nkhani yonena za Myuda ndi Msamariya. Taphunzira kale kuti Ayuda ochuluka samakonda Asamariya. Chabwinotu, nayi nthano ya Yesu:

Tsiku lina Myuda wina anali kuyenda mu mseu wa m’mapiri kumka ku Yeriko. Koma achifwamba anam’lumphira. Iwo anatenga ndalama zake nam’menya mpaka kukomoka.

Pambuyo pake wansembe Wachiyuda anadza mu mseu’wo. Iye anaona munthu womenyedwa’yo. Kodi muganiza anachitanji? Eya, iye anangopambukira ku njira ina napita. Ndiyeno munthu wina wokonda chipembedzo kwambiri anadza. Iye anali Mlevi. Kodi iye anaima? Ai, iye sanaime kuti athandize munthu womenyedwa’yo. Mungaone wansembe ndi Mlevi awo akumka chauko’wo.

Koma onani uyu ali pano ndi munthu womenyedwa’yu. Iye ndi Msamariya. Ndipo iye akuthandiza Myuda. Iye akuika mankhwala pa mabala ake. Kenako, iye akutengera Myuda’yo ku malo amene iye angapume ndi kupeza bwino.

Atatha kukamba nthano yake’yo, Yesu akuti kwa munthu’yo: ‘Kodi ndi uti wa atatu’wa uganiza kuti anachita monga mnansi kwa munthu womenyedwa’yo? Kodi anali wansembe’yo, Mlevi kapena Msamariya’yo?’

Munthu’yo akuyankha kuti: ‘Msamariya’yo. Anakomera mtima womenyedwa’yo.’

Yesu akuti: ‘Walondola. Chotero pita ukachitire anthu monga momwe iye anachitira.’

Kodi simukukonda m’mene Yesu akuphunzitsira? Tingaphunzire zinthu zochuluka ngati timvetsera zimene Yesu akunena m’Baibulo, kodi si choncho?