Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 37

Chihema Cholambirira

Chihema Cholambirira

KODI mukudziwa chimene nyumba’yi iri? Ndiyo chihema chapadera cholambiriramo Yehova. Chimachedwa’nso chihema chokomana’ko. Anthu anamaliza kuchimanga patapita chaka chimodzi atatuluka m’Igupto. Kodi mukudziwa kuti linali lingaliro la yani kuti chimangidwe?

Linali lingaliro la Yehova. Mose ali pa Phiri la Sinai, Yehova anamuuza kuchimanga kwake. Iye anati chipangidwe kotero kuti chingathe kumasulidwa mosabvuta. Motere mbali zake zikanatha kunyamulidwa kumka nazo ku malo ena, ndi kukasonkhanitsidwa kumene’ko. Chotero pamene Aisrayeli anasamuka-samuka m’chipululumo, anamka ndi chihema chomwe.

Mukayang’ana m’kachipinda ka kumapeto kwa chihema’cho, mungaone bokosi. Limene’li limachedwa likasa la chipangano. Linali ndi angelo awiri a golidi, kapena akerubi, wina uku wina kwinako. Mulungu analemba’nso Malamulo Khumi pa miyala iwiri yaphanthi-phanthi, chifukwa Mose anaswa yoyamba ija. Ndipo miyala imene’yi inasungidwa m’likasa la chipangano’lo. Ndipo’nso, mbale ya mana inasungidwamo. Kodi mukukumbukira chimene mana ali?

Mkulu wa Mose Aroni ndiye amene Yehova anam’sankha kukhala mkulu wa ansembe. Iye anatsogolera anthu m’kulambira Yehova. Ndipo nawo’nso ana ake amuna ndi ansembe.

Tsopano yang’anani m’chipinda chokulira cha chihema’cho. N’chachikulu mowirikiza chaching’ono’cho. Kodi mukuona kabokosi’ko, kamene kakutulutsa utsi? Iri ndiro guwa lansembe pa limene ansembe anaocherapo zonunkhira zochedwa lubani. Ndiyeno pali choikapo nyali chimene chiri ndi nyali zisanu ndi ziwiri. Chinthu chachitatu m’chipinda’cho ndicho thebulo. Pa iro pamasungidwa mitanda 12 ya mkate.

M’bwalo la chihema chokomanako’cho munali beseni lalikuli, lodzazidwa madzi. Ansembe amaligwiritsira ntchito kusambamo. Muli’nso guwa lansembe lalikulu. Panopa nyama zophedwa zimaperekedwa nsembe kwa Yehova. Chihema’cho chiri pakati-kati pa msasa, ndipo Aisrayeli akukhala m’mahema ao mochizungulira.