Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 53

Lonjezo la Yefita

Lonjezo la Yefita

KODI munayamba mwapanga lonjezo ndiye pambuyo pake n’kuliona kukhala lobvuta kulisunga? Mwanuna’yo m’chithunzi’chi anatero, ndicho chifukwa chake ali wachisoni kwambiri. Mwamuna’yo ndi woweruza wolimba mtima wa Israyeli wochedwa Yefita.

Iye akukhala ndi moyo pa nthawi imene Aisrayeli sakulambira’nso Yehova. Iwo akuchita’nso zoipa. Chotero Yehova akulola Aamoni kuwakatha. Izi zikuchititsa Aisrayeli kupfuulira kwa Yehova kuti: ‘Takuchimwirani. Chonde, tipulumutseni!’

Anthu’wo ali n’chisoni chifukwa cha zoipa zimene iwo achita. Akusonyeza kuti ali n’chisoni mwa kulambira’nso Yehova. Chotero kachiwiri’nso Yehova akuwathandiza.

Yefita akusankhidwa ndi anthu’wo kukamenyana ndi Aamoni oipa’wo. Yefita akufuna kwambiri kuti Yehova am’thandize m’nkhondo’yo. Chotero akulonjeza Yehova kuti: ‘Ngati mudzandipatsa chipambano pa Aamoni, munthu woyamba wotuluka m’nyumba mwanga kudzandichingamira pochokera ku chipambano’ko ndidzam’pereka kwa inu.’

Yehova akumvetsera lonjezo la Yefita, ndipo akum’thandiza kupambana. Pobwerera kwao, kodi mukudziwa amene anali woyambirira kum’chingamira? Ndiye mwana wake wamkazi, amene anali mmodzi yekha. ‘O, mwana wanga wamkazi!’ akutero Yefita. N’chisoni chotani nanga chimene ukundidzetsera. Koma ndalonjeza kwa Yehova, sindingasinthe.’

Atamva za lonjezo’lo mwana’yo, poyamba ali ndi chisoni naye’nso. Pakuti zikutanthauza kuti adzafunikira kusiya atate ndi mabwenzi ake. Koma adzaonongera moyo wake wonse akutumikira Yehova pa chihema m’Silo. Iye akuuza atate wake kuti: ‘Ngati mwapanga lonjezo kwa Yehova muyenera kulisunga.’

Chotero mwana’yo akumka ku Silo, naonongera moyo wake wonse m’kutumikira Yehova pa chihema. Masiku anai pa chaka akazi a Isryeli akukam’zonda kumene’ko, ndipo onse amasangalalira pamodzi. Anthu amakonda mwana’yo chifukwa ndi mtumiki wabwino wa Yehova.