Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 46

Malinga a Yeriko

Malinga a Yeriko

KODI n’chiani chimene chikugwetsa malinga a Yeriko’wa? Kukuonekera ngati kuti pagwera bomba lalikulu. Koma m’masiku’wo kunalibe mabomba; iwo analibe ngakhale mfuti. N’chozizwitsa china cha Yehova! Tiyeni tiphunzire m’mene zinachitikira.

Imvani zimene Yehova akuuza Yoswa: ‘Iwe ndi ankhondo ako muzizungulira mzinda’wo. Muuzungulire kamodzi pa tsiku kwa masiku asanu ndi limodzi. Mumke ndi likasa la chipangano lomwe. Ansembe asanu ndi awiri ayenera kulitsogolera ndi kuomba mphalasa zao.

‘Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzungulira mzinda nthawi zisanu ndi ziwiri. Ndiyeno n’kuliza chilizire mphalasa’zo, n’kuuza ali yense kufuulitsa. Ndipo malinga’wo adzagwa pansi phwata!’

Yoswa ndi anthu’wo akuchita zonena za Yehova. Pozungulira, ali yense ali chete. Palibe wolankhula liu. Zokha zimene zikumveka ndizo mphalasa ndi mlikiti wa mapazi. Adani a anthu a Mulungu m’Yerikomo ayenera kukhala akuchita mantha. Kodi mukuona chingwe chofiira chikulendewera pa zenera’cho? Kodi n’zenera la yani iro? Inde, Rahabi wachita zimene azondi aja anamuuza. A m’banja mwake onse ali m’katimo akuonera naye.

Kenako, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, atazungulira kasanu ndi kawiri, mphalasa zikulizidwa, ankhondo’wo akupfuula, ndipo malinga akugwa. Yoswa akulamulano kuti: ‘Iphani ali yense mu mzinda’wo. Tenthani chiri chonse. Sungani kokha siliva, golidi, mkuwa ndi chitsulo, n’kuzipereka zilowe mosungira mwa chihema cha Yehova.’

Yoswa akuuza azondi awiri’wo, kuti: ‘Lowani m’nyumba ya Rahabi, nimum’tulutse iye ndi a m’banja lake onse.’ Rahabi ndi a m’banja lake apulumitsidwa, monga momwe analonjezera azondi’wo.