Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 40

Mose Amenya Thanthwe

Mose Amenya Thanthwe

ZAKA zikupita—zaka 10, zaka 20, zaka 30, zaka 39! Ndipo Aisrayeli akali m’chipululu. Koma m’zaka zonse’zi Yehova akusamalira anthu ake. Akuwadyetsa mana. Akuwatsogolera usana ndi mtambo woti njo, usiku ndi moto woti njo. Ndipo m’zaka zonse’zi zobvala zao sizikutha ndipo mapazi ao sakupweteka.

Tsopano ndi mwezi woyamba wa chaka cha 40 chichokere ku Igupto. Kachiwiri’nso iwo akumanga misasa pa Kadesi. Apa ndipo pamene iwo anali pamene azondi 12 anatumizidwa kukazonda Kanani pafupi-fupi zaka 40 zapita’zo. Mlongo wa Mose Miriamu akufera pa Kadesi. Ndipo monga kale, pali bvuto pano.

Anthu sakupeza madzi. Chotero akudandaulira Mose: ‘Kukanankhala bwino kwambiri tikanafa. Kodi unatitulutsiranji mu Igupto kudzatilowetsa m’malo oopsya ano amene sangabale kanthu? Palibe dzinthu, nkhuyu, mphesa, makangaza. Palibe ngakhale madzi akumwa.’

Pamene Mose ndi Aroni akumka ku chihema chokomana’ko kukapemphera, Yehova akuuza Mose kuti: ‘Sonkhanitsa anthu. Ndiyeno pamaso pao onse akulankhula ndi thanthwe iro. Madzi okwanira adzatulukamo kaamba ka anthu’wo ndi zifuyo zonse.’

Tsono Mose akusonkhanitsa anthu, nati: Imvani, osadalira Mulungu inu! Kodi ine ndi Aroni tikutulutsireni madzi m’thanthwe’mu?’ Ndiyeno Mose akumenya thanthwe’lo kawiri ndi ndodo, ndipo madzi ochuluka anatulukamo. Pali madzi okwanira kumwa anthu onse ndi zifuyo.

Koma Yehova wakwiyira Mose ndi Aroni. Kodi mukudziwa chifukwa chake? N’chifukwa chakuti Mose ndi Aroni anati iwo akawatulutsira madzi m’thanthwe’lo. Koma analitu Yehova amene anatulutsa. Ndipo chifukwa chakuti Mose ndi Aroni sananene choonadi chonena za izi, Yehova akuti akawalanga. Iye akuti, ‘simudzalowetsa anthu anga m’Kanani.’

Posakhalitsa Aisrayeli akuchoka pa Kadesi. Kanthawi pang’ono iwo akufika pa Phiri la Hori. Pamwamba pa phiri lino, Aroni akufa. Iye ali ndi zaka 123 pa nthawi ya imfa yake. Aisrayeli ali achisoni kwambiri, chotero kwa masiku 30 anthu onse akulirira Aroni. Mwana wake Eliezara akukhala mkulu wansembe wotsatirapo wa mtundu wa Israyeli.