Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 36

Mwana wa Ng’ombe wa Golidi

Mwana wa Ng’ombe wa Golidi

O, O! KODI anthu’wo akuchitanji tsopano? Iwo akupemphera kwa mwana wa ng’ombe! Kodi akuchitiranji izi?

Pamene Mose akukhala kwa nthawi yaitali pa phiripo anthu’wo akuti: ‘Sitidziwa chimene chachitikira Mose. Chotero tiyeni tipange mulungu atitulutse m’dziko lino.’

Mkulu wa Mose Aroni akuti, ‘Chabwino. Bvulani ndolo zanu zagolidi’zo, mudze nazo kwa ine.’ Atatero anthu’wo, Aroni akuzisungunula nazipanga mwana wa ng’ombe wa golidi. Ndipo anthu’wo akuti: ‘Uyu ndiye Mulungu wathu, amene anatitulutsa mu Igupto!’ Ndiyeno Aisrayeli akuchita phwando lalikulu, nalambira mwana wa ng’ombe wa golidi’yo.

Poona izi Yehova, akupsya mtima kwambiri. Chotero akuti kwa Mose: ‘Fulumira tsika. Anthu akuchita moipa kwambiri. Iwo aiwala malamulo anga ndipo akugwadira mwana wa ng’ombe wa golidi.’

Mose akutsika mofulumira m’phirimo. Ndipo pamene akufika pafupi, izi ndizo zimene akuona. Anthu’wo akuyimba ndi kubvina mozungulira mwana wa ng’ombe’yo! Mose akupsya mtima kwambiri kwakuti akuponya pansi miyala iwiri ija yokhala ndi malamulo, ndipo ikuphwanyika-phwanyika. Pamenepo iye akutenga mwana wa ng’ombe wa golidi’yo nam’sungunula. Kenako akum’pera-pera.

Anthu’wo achita chinthu choipa kwambiri. Chotero Mose akuuza ena a anthu’wo kutenga malupanga ao. ‘Anthu oipa amene analambira mwana wa ng’ombe wa golidi’yo ayenera kufa,’ akutero Mose. Chotero amuna’wo akupha anthu 3,000! Kodi izi sizikusonyeza kuti tiyenera kukhala osamala kuti tizilambira Yehova yekha osati milungu iri yonse yonyenga?