Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 44

Rahabi Abisa Azondi

Rahabi Abisa Azondi

AMUNA’WA ali m’bvuto. Iwo ayenera kuchoka, akapanda kutero adzaphedwa. Iwo ndi azondi Achiisrayeli, ndipo mkazi amene akuwathandiza’yo ndiye Rahabi. Rahabi amakhala muno m’nyumba ya m’linga la mzinda wa Yeriko. Tiyeni tione chifukwa chake amuna’wa ali m’bvuto.

Aisrayeli akonzeka kuoloka Yordano kulowa m’Kanani. Koma asanatero, Yoswa akutumiza azondi awiri. Iye akuwauza kuti: ‘Kazondeni mzinda wa Yeriko.’

Pamene Azondi’wo akulowa m’Yeriko, akulowa m’nyumba ya Rahabi. Koma wina wake akuuza mfumu ya Yeriko kuti: ‘Aisrayeli awiri analowa muno usiku kudzazonda dziko’li.’ Pomva zimene’zi, mfumu’yo ikutumiza anthu kwa Rahabi, nam’lamula kuti: ‘Tulutsa amuna amene uli nao m’nyumba mwako!’ Koma Rahabi anabisa amuna’wo pa tsindwi lake. Chotero akuti: ‘Anadza’di amuna ena pa nyumba panga, koma sindidziwa kumene anachokera. Iwo ananyamuka pamene kumayamba kuda, chipata cha mzinda chisanatsekedwe. Ngati mutafulumira, mungawapeze!’ Ndipo chotero amuna’wo akuwathamangira.

Atachoka, Rahabi akufulumira kumka pa tsindwipo. ‘Ndidziwa kuti Yehova adzakupatsani dziko’li,’ iye akuuza motero azondi’wo. Tinamva m’mene anaphwetsera Nyanja Yofiira pamene munalinkuchoka ku Igupto, ndi m’mene munaphera mafumu’wo Sihoni ndi Ogi. Ndakukomerani mtima, chotero ndilonjezeni, chonde, kuti mudzandikomera mtima. Pulumutsani atate ndi mai wanga, ndi abale ndi alongo anga.’

Azondi’wo akulonjeza kuti adzatero, koma Rahabi ayenera kuchita kanthu kena. ‘Tenga chingwe chofiira’chi ndi kuchimangirira pa zenera lako,’ akutero azondi’wo, ‘nusonkhanitse achibale ako onse m’nyumba mwako. Ndipo pakubwerera ife ku Yeriko, tidzaona chingwe’chi pa zenera lako ndipo sitidzapha ali yense m’nyumba mwako.’ Pobwerera kwa Yoswa azondi’wo, akumuuza zonse zimene zinachitika.