Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 60

Abigayeli ndi Davide

Abigayeli ndi Davide

KODI mukudziwa mkazi wokongola amene akuchingamira Davide’yo? Ndiye Abigayeli. Ngwa maganizo abwino, ndipo akuletsa Davide kuchita choipa. Tisanaphunzire za izi, tiyeni tione chimene chachitikita Davide.

Davide atathawa Sauli, akubisala m’phanga. Abale ake ndi ena onse a m’banja lake ali naye kumeneko’ko. Onse pamodzi anthu 400 akudza kwa iye, ndipo Davide akukhala m’tsogoleri wao. Pamenepo iye akumka kwa mfumu ya Moabu nati: ‘Chonde lolani kuti atate ndi amai wanga akhale nanu mpaka nditaona chimene chidzandichitikira.’ Kenako iye ndi anthu ake akuyamba kubisala m’mapiri.

Zitachitika izi ndi pamene iye akukumana ndi Abigayeli. Mwamunake Nabala ndi wolemera wokhala ndi kadziko. Ali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Nabala ndi munthu wachipongwe. Mkazi wake ndi wokongola kwambiri. Ndipo’nso, ngwodziwa kuchita zoyenera. Pa nthawi ina anapulumutsa banja lake. Tiyeni tione.

Davide ndu anthu ake akhala okoma mtima kwa Nabala. Iwo athandiza kutetezera nkhosa zake. Tsiku lina Davide akutuma amuna ake kukapempha chithandizo kwa Nabala. Iwo akufika kwa Nabala iye ndi othandiza ake kusenga ubweya wa nkhosa. N’tsiku la phwando, ndipo iye ali ndi zakudya zambiri zabwino. Chotero nazi zimene anthu a Davide akunena: ‘Takhala okoma mtima kwa inu. Sitinabe iri yonse ya nkhosa zanu, koma tathandiza kuziyang’anira. Tsono, chonde, tipatseniko chakudya.’

‘Sindidzapatsa chakudya changa kwa anthu onga inu,’ akutero Nabala. Akulankhula monyoza Davide kwambiri. Amuna’wo atabwerera nauza Davide za izi, Davide’yo akupsya mtima kwambiri. Ndiyeno akuuza amuna ake kuti, ‘Tengani malupanga anu!’ Ndipo ananyamuka kumka kukapha Nabala ndi amuna ake.

Mmodzi wa anthu a Nabala, amene anamva mau oipa a Nabala, akuuza Abigayeli zochitika’zo. Pompo iye akukonza zakudya. Akuziika pa abulu namka nazo. Pokumana ndi Davide, akutsika pa bulu wake, nagwada pansi nati: ‘Chonde, mbuyanga, musamvere mwamunanga Nabala. Iye ngwopusa, ndipo amachita zopusa. Nawu mtulo. Ulandireni chonde, nimutikhululukire chifukwa cha zimene zinachitika’zi.’

‘Iwe ndiwe mkazi wanzeru,’ akuyankha tero Davide. ‘Wandiletsa kupha Nabala kum’bwezera kuipa kwake. Pita kwanu mu mtendere.’ Kenako, atafa Nabala, Abigayeli akukhala mmodzi wa akazi a Davide.