NKHANI 63
Mfumu yanzeru Solomo
SOLOMO n’kamnyamata pamene iye akukhala mfumu. Iye amakonda Yehova, ndipo amatsatira chilangizo chabwino chimene atate wake Davide anam’patsa. Yehova akukondwera ndi Solomo, tsono usiku wina akunena naye m’loto kuti: ‘Solomo, kodi ungafune kuti ndikupatsenji?’
Solomo anayankha kuti: ‘Yehova Mulungu wanga, ndiri wamng’ono ndipo sindidziwa kulamulira. Chotero ndipatseni nzeru kuti ndilamulire anthu anu moyenera.’
Yehova kukondwera ndi zimene Solomo akupempha. Iye akuti: ‘Chifukwa chakuti wapempha nzeru ndipo osati moyo wautali kapena chuma, ndidzakupatsa nzeru zambiri koposa wina ali yense amene anakhakapo ndi moyo. Koma ndidzakupatsa’nso zimene sunapemphe, chuma ndi ulemerero womwe.’
Posapita nthawi pambuyo pake akazi awiri anadza kwa Solomo ndi chothetsa nzeru. ‘Mkazi’yu ndi ine timakhala m’nyumba imodzi,’ mmodzi wa iwo akutero. ‘Ndinabala mwana wamwamuna, ndipo masiku awiri pambuyo pake naye’nso anabala mwana wamwamuna. Ndiyeno usiku wina khanda lake linafa. Koma ndiri mtulo, anadzagoneka mwana wake wakufa’yo pa ine natenga mwana wanga. Nditadzuka ndi kuona mwana wakufa’yo, ndinaona kuti sanali wanga.’
Pamenepo mkazi wina’yo anati: ‘Ai! Mwana wamoyo’yo ngwanga, ndipo wakufa’yo ngwake!’ Mkazi woyamba’yo akuyankha kuti: ‘Ai! Mwana wakufa’yo ngwako, ndipo wamoyo’yo ngwanga!’ Ndimo m’mene akazi’wo anatsutsanira. Kodi Solomo adzachitanji?
Akuitanitsa lupanga, ndipo, atadza nalo, akuti: ‘Dulani pakati mwana wamoyo’yo, n’kuwaninkha wina theka wina theka.’
‘Ai!’ akutero molira mai wake weni-weni. ‘Chonde musaphe khanda’lo. Mpatseni!’ Koma mkazi wina’yo akuti: ‘Musam’pereke kwa ali yense wa ife; ingom’dulani pawiri.’
Potsiriza Solomo akuti: ‘Musaphe mwana’yo! Mperekeni kwa mkazi woyamba’yo. Ndiye mai wake weni-weni. Solomo akudziwa izi chifukwa chakuti mai weni-weni amakonda khanda kwambiri kwakuti iye ali wofunitsitsa kum’pereka kwa mkazi wina’yo kuti asaphedwe. Anthu pomva m’mene Solomo anathetsera chothetsa nzeru’cho, iwo akukonda kukhala ndi mfumu yanzeru yotero’yo.
M’kukamulira kwa Solomo, Mulungu akudalitsa anthu’wo mwa kupangitsa nthaka kukhala yobala tirigu wochuluka ndi barele, mphesa ndi nkhuyu ndi zakudya zina. Anthu akubvala zobvala zabwino ndipo akukhala m’nyumba zabwino. Pali zabwino zokwanira munthu ali yense.