CHIGAWO 5
Ukapolo M’babulo Mpaka pa Kumangidwa’nso kwa Malinga a Yerusalemu
Akali mu ukapolo m’Babulo, Aisrayeli anali ndi ziyeso zambiri za chikhulupiriro chao. Sadrake, Mesake ndi Abedinego anaponyedwa m’ng’anjo ya moto wa koli-koli, koma Mulungu anawatulutsamo amoyo. Kenako, Babulo atagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperesi, Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango, koma Mulungu amam’tetezera’nso mwa kutseka pakamwa pa mikango.
Potsirizira pake, mfumu ya Peresi Koresi anamasula Aisrayeli. Iwo anabwerera ku dziko lakwao patapita zaka 70 chiyambire pamene iwo anatengedwa kumka ku Babulo monga akapolo. Chinthu chimodzi chimene iwo anachita atabwerera ku Yerusalemu chinali kuyamba kumanga kachisi wa Yehova. Komabe, adani posapita nthawi anaimitsa ntchito yao. Chotero panali pafupi-fupi pambuyo pa zaka 22 atabwerera ku Yerusalemu kuti iwo potsirizira pake anamaliza kachisi’yo.
Kenako, timaphunzira za ulendo wa Ezara wobwerera ku Yerusalemu kukakongoletsa kachisi. Izi zinali pambuyo pa zaka 47 kuyambira pamene kachisi anamalizidwa. Ndiyeno, zaka 13 pambuyo pa ulendo wa Ezara’wo, Nehemiya anathandiza kumanga’nso malinga ogamuka’wo a Yerusalemu. Chigawo CHACHISANU chikulowetsamo zaka 152 za mbiri kudzafika ku nthawi ino.