Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 82

Mordekai ndi Estere

Mordekai ndi Estere

TIYENI tibwerere m’mbuyo ku zaka zowerengeka Ezara asanapite ku Yerusalemu. Mordekai ndi Estere ndiwo Aisrayeli ofunika kopambana mu ufumu wa Perisiya. Estere ndi mkazi wa mfumu, ndipo mwana wa mn’gono wa atate wake Mordekai ngwachiwiri kwa mfumu mu ulamuliro. Tiyeni tione m’mene zimene’zi zinachitikira.

Makolo a Estere anafa akali wamng’ono kwambiri, ndipo analeredwa ndi Mordekai. Ahaswero, mfumu ya Perisiya, anali ndi mphala mu mzinda wa Susani, ndipo Mordekai ndi mmodzi wa atumiki ake. Ndiyeno, tsiku lina mkazi wa mfumu Vasiti sakumumvera, chotero iyo ikusankha mkazi watsopano kukhala mkazi wake. Kodi mukudziwa mkazi amene iyo ikusankha? Inde, mtsikana wokongola’yo Estere.

Kodi mukumuona munthu wonyada’yu amene anthu akum’weramira? Ndiye Hamani. Iye ndi munthu wofunika kwambiri m’Perisiya. Iye akufuna’nso kuti Mordekai, amene mukumuona atakhala pansi’yu, am’gwadire. Koma iye sakukuchita. Sakuganiza kuti n’koyenera kuweramira munthu woipa wotere’yu. Izi zikupangitsa Hamani kukwiya kwambiri. Ndipo chotero nazi zimene iye akuchita.

Hamani akuuza mfumu mabodza ponena za Aisrayeli. ‘Iwo ndi anthu oipa amene sakumvera malamulo anu,’ akutero. ‘Iwo ayenera kuphedwa.’ Ahaswero sakudziwa kuti mkazi wake Estere ndi Muisrayeli. Chotero akumvetsera Hamani, nachititsa lamulo kupangidwa lakuti pa tsiku lina Aisrayeli onse ayenera kuphedwa.

Mordekai atamva za lamulo’lo, iye akubvutika maganizo kwambiri. Iye akutumiza mthenga kwa Estere kuti: ‘Uuze mfumu, ndi kuipempha itipulumutse.’ N’kotsutsana ndi lamulo m’Perisiya kukaonana ndi mfumu ngati sunaitanidwe. Koma Estere akumka wosaitanidwa. Mfumu’yo ikutukulira ndodo yake ya golidi kwa iye, kutanthauza kuti sayenera kuphedwa. Estere akuitanira mfumu ndi Hamani ku phwando. Kumene’ko mfumu ikufunsa Estere bwino umene iye angam’chitire. Estere akuti adaiuza ngati iyo ndi Hamani adzadza ku chakudya china m’mawa mwake.

Pa chakudya’cho Estere akuuza mfumu kuti: ‘Ine ndi anthu a mtundu wanga tiyenera kuphedwa.’ Mfumu yakwiya. ‘Ndani amene akufuna kuchita chinthu chotero’cho?’ ikufunsa motero.

‘Mdani’yo, ndiye munthu woipa’yu Hamani! akutero Estere.

Tsopano mfumu yakwiya kwambiri’di. Ikulamula kuti Hamani aphedwe. Kenako, mfumu ikupanga Mordekai kukhala wachiwiri m’mphamvu kwa iye mwini. Mordekai akutsimikizirano kuti lamulo latsopano likupangidwa lolola Aisrayeli kumenyera nkhondo miyoyo yao pa tsiku limene iwo ayenera kuphedwa. Chifukwa chakuti Mordekai ali wofunika kwambiri tsopano, anthu ambiri akuthandiza Aisrayeli, ndipo akupulumutsidwa kwa adani ao.

Bukhu la Baibulo la Estere.