Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 78

Zolembedwa ndi Manja pa Khoma

Zolembedwa ndi Manja pa Khoma

KODI chikuchitika pano n’chiani? Anthu’wa ali pa madyerero. Mfumu ya Babulo yaitana anthu ochuka zikwi-zikwi. Akugwiritsira ntchito zikho zagolidi ndi zasiliva ndi mbale zotengedwa m’kachisi wa Yehova. Komano. modzidzimutsa, zala za dzanja la munthu zikuoneka m’malere naziyamba kulemba pa khoma. Ali yense akuopsyedwa.

Belisazara, mdzukulu wa Nebukadinezara, pa nthawi ino ndiye mfumu. Akuitana anzeru onse mopfuula. ‘Ali yense amene angadiwerengere zolembedwa’zi n’kundiuza kutanthauza kwake,’ ikutero mfumu’yo, ‘adzapatsidwa mphatso zambiri ndi kupangidwa kukhala wolamulira wachitatu mu ufumu.’ Koma palibe wanzeru wokhoza kuwerenga zolembedwa’zo, kapena kuzitanthauzira.

Mai wa mfumu pomva phokoso akudza modyeramo. ‘Chonde musaopsyedwe kwambiri,’ akutero mai’yo. ‘Muli munthu mu ufumu wanu wodziwa milungu yoyera. Muja gogo wanu Nebukadinezara anali mfumu anam’panga kukhala mkulu wa anzeru onse. Munthu’yo ndiye Danieli. Kamuitaneni, adzakuuzani tanthauzo lake.’

Pomwepo Danieli akulowetsedwa. Atakana kulandira mphatso iri yonse, Danieli akuyamba kufotokoza chifukwa chake Yehova pa nthawi ina anachotsa gogo wa Belisazara, Nebukadinezara pa ufumu. ‘Iye anali wodzitukumula kwambiri,’ Danieli akutero. ‘Yehova anam’langa.’

‘Koma inu,’ Danueli akuuza Belisazara, ‘munadziwa zonse zimene zinam’chitikira, ndipo komabe muli wonyada monga momwe analiri iye. Mwadza ndi zikho ndi mbale za m’kachisi wa Yehova ndi kumweramo. Mwatamanda milungu yopangidwa ndi mtengo, ndi mwala, ndipo simunalemekeza Mlengi wathu Wamkulu. Ndicho chifukwa chake Mulungu watumiza dzanja kudzalemba mau’wa.

‘Zolembedwa ndi izi,’ akutero Danieli: ‘MEʹNE, MEʹNE, TEʹKEL ndi PARʹSIN.’

‘MEʹNE amatanthauza kuti Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu n’kuwatha. TEʹKEL amatanthauza kuti waikidwa pa muyeso nupezeka woperewera. PARʹSIN amatanthauza kuti ufumu wanu waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.’

Danieli akali chilankhulire, Amedi ndi Aperisi aukira kale Babulo. Akulanda mzinda’wo napha Belisazara. Mau olembedwa ndi manja pa khoma’wo akukwaniritsidwa usiku womwewo! Kodi n’chiani chimene chidzachitikira Aisrayeli tsopano? Tidzaona posachedwa, koma tiyeni tiyambe taona chimene chukuchitikira Danieli.