Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mateyu Chaputala 5-7

Mateyu Chaputala 5-7

5 Ataona khamu la anthu, anakwera m’phiri. Atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye. 2 Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:

3 “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

4 “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.

5 “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.

6 “Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhuta.

7 “Odala ndi anthu achifundo, chifukwa adzachitiridwa chifundo.

8 “Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.

9 “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’

10 “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.

11 “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. 12 Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.

13 “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja kumene anthu akaupondaponda.

14 “Inu ndinu kuwala kwa dziko. Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15 Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse m’nyumbamo. 16 Momwemonso, onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.

17 “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa. 18 Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta, kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi ka lemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike. 19 Chotero aliyense wophwanya lililonse la malamulo aang’ono awa ndi kuphunzitsa anthu kuphwanya malamulowo, adzakhala ‘wosayenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba. Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa, ameneyo adzakhala ‘woyenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba. 20 Pakuti ndikukuuzani inu kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha alembi ndi Afarisi, ndithudi simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

21 “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu. Aliyense amene wapha mnzake wapalamula mlandu wa kukhoti.’ 22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima m’bale wake wapalamula mlandu wa kukhoti. Komano aliyense wonenera m’bale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe!’ adzapita ku Gehena a wamoto.

23 “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, 24 siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.

25 “Thetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26 Kunena zoona, sudzatulukamo kufikira utalipira kakhobidi kotsirizira.

27 “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’ 28 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. 29 Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa, b ulikolowole ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehena. 30 Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehena.

31 “Pajanso anati, ‘Aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, apatse mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’ 32 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama, c amamuchititsa chigololo akakwatiwanso, ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.

33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’ 34 Koma ine ndikukuuzani kuti: Usamalumbire n’komwe, kutchula kumwamba, chifukwa ndi kumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu; 35 kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake, kapena kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda wa Mfumu yaikulu. 36 Kapena usalumbire kutchula mutu wako, chifukwa sungathe kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyera kapena lakuda. 37 Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.

38 “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’ 39 Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja, umutembenuzirenso linalo. 40 Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, m’patsenso akunja. 41 Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri. 42 Munthu akakupempha kanthu m’patse, ndipo munthu wofuna kukongola kanthu kwa iwe popanda chiwongoladzanja usamukanize.

43 “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako ndi kudana ndi mdani wako.’ 44 Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, 45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba. Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe. 46 Pakuti mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani? Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? 47 Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48 Choncho khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.

6 “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni, chifukwa mukatero simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba. 2 Chotero pamene ukupereka mphatso zachifundo, usalize lipenga muja amachitira onyenga m’masunagoge ndi m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 3 Koma iwe, pamene ukupereka mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita, 4 kuti mphatso zako zachifundo zikhale zamseri. Ukatero Atate wako amene akuyang’ana kuseriko adzakubwezera.

5 “Komanso pamene mukupemphera, musamachite ngati anthu onyenga. Pakuti iwo amakonda kuimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera. 7 Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza ngati mmene amachitira anthu a mitundu ina, chifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu awamvera akanena mawu ambirimbiri. 8 Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.

9 “Koma inu muzipemphera motere:

“‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. 10 Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. 11 Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. 12 Mutikhululukire zolakwa d zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. e 13 Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’

14 “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani. 15 Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.

16 “Pamene mukusala kudya, lekani kumaonetsa nkhope yachisoni ngati mmene onyenga aja amachitira. Iwo amaipitsa nkhope zawo kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 17 Koma iwe, pamene ukusala kudya, dzola mafuta m’mutu mwako ndi kusamba nkhope yako, 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatero Atate wako amene akukuona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.

19 “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete f ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. 20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba. 21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.

22 “Nyale ya thupi ndi diso. Chotero ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala. 23 Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndiko mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!

24 “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.

25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala? 26 Onetsetsani mbalame zam’mlengalenga, pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola, kapenanso kusunga chakudya m’nkhokwe. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi? 27 Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha g mwa kuda nkhawa? 28 Komanso pa nkhani ya zovala, n’chifukwa chiyani mukuda nkhawa? Phunzirani pa mmene maluwa akutchire amakulira. Sagwira ntchito, ndiponso sawomba nsalu. 29 Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 30 Tsopano ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha, mawa n’kuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu? 31 Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ 32 Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.

33 “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu. 34 Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.

7 “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe, 2 pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho. Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo. 3 Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga h la nyumba umene uli m’diso lako? 4 Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba? 5 Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.

6 “Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.

7 “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. 8 Pakuti aliyense wopempha amalandira, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira. 9 Inde, ndani pakati panu amene mwana wake atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? 10 Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11 Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!

12 “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.

13 “Lowani pachipata chopapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. 14 Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.

15 “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi? 17 Momwemonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake. 18 Mtengo wabwino sungabale zipatso zopanda pake, ndiponso mtengo wovunda sungabale zipatso zabwino. 19 Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto. 20 Chotero anthu amenewo mudzawazindikira ndi zipatso zawo.

21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” 22 Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’ 23 Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.

24 “Chotero aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe. 25 Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. 26 Aliyense wakumva mawu angawa koma osawachita adzafanizidwa ndi munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pamchenga. 27 Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo moti inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”

28 Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, 29 chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro, osati monga alembi awo.

[Mawu a M’munsi]

a Malo omwe ankawotcherako zinyalala kunja kwa Yerusalemu. Mawu Achigiriki a Chigwa cha Hinomu chomwe chinali kum’mwera chakum’mawa kwa Yerusalemu wakale. Palibe umboni wosonyeza kuti Gehena anali malo oponyako nyama zamoyo kapena anthu amoyo kuti apse kapena kuzunzidwa. N’chifukwa chake mawuwa sangatanthauze malo enaake osaoneka kumene mizimu ya anthu imazunzidwa kwamuyaya m’moto weniweni. Choncho, mawu akuti Gehena anagwiritsidwa ntchito ndi Yesu ndiponso ophunzira ake pophiphiritsira kuwonongedweratu, kufafanizidwa m’chilengedwe chonse cha Mulungu.

b Mawu ake enieni, “limakupunthwitsa.”

c Mawu achigiriki akuti por·neiʹa (poneya), amagwiritsidwa ntchito m’Malemba potanthauza mitundu ya kugonana komwe Mulungu amaletsa. Zimenezi zikuphatikizapo chigololo, uhule, kugonana kwa anthu omwe sanakwatirane, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha komanso kugonana ndi nyama.

d Mawu ake enieni, “ngongole.”

e Mawu ake enieni, “ali nafe ngongole.”

f Mawu amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.

g Mawu ake enieni, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.”

h Kapena kuti “tsindwi.