Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 25

Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe?

Kodi Amene Amachita Zinthu Zoipa Angasinthe?

KODI sizingakhale zosangalatsa ngati aliyense atamachita zinthu zabwino?— Komatu palibe munthu amene amachita zinthu zabwino nthaŵi zonse. Kodi ukudziŵa chifukwa chake tonse timachita zinthu zoipa nthaŵi zina, ngakhale pamene tikufuna kuchita zabwino?— Ndi chifukwa chakuti tonsefe tinabadwa ndi uchimo. Koma anthu ena amachita zinthu zambiri zoipa kwabasi. Amada anthu ena ndi kuwapweteka mwadala. Kodi ukuganiza kuti iwo angasinthe ndi kuphunzira kukhala anthu abwino?—

Taona munthu uyo amene wasunga zovala za anthu awo akuponya miyala Stefano. Dzina lake la Chihebri ndi Saulo, koma la Chiroma ndi Paulo. Iye akusangalala kuti Stefano, yemwe ndi wophunzira wa Mphunzitsi Waluso, akuphedwa. Tiye tione chifukwa chake Saulo akuchita zinthu zoipa zoterezi.

Saulo anali m’gulu lachipembedzo la Ayuda lotchedwa Afarisi. Afarisi anali ndi Mawu a Mulungu, koma iwo anali kugwiritsa ntchito kwambiri zimene atsogoleri awo ena achipembedzo anali kuphunzitsa. Saulo anali kuchita zinthu zoipa chifukwa cha zimenezi.

Pamene Stefano anagwidwa ku Yerusalemu, Saulo anali pomwepo. Stefano anapita naye ku khoti kumene oweruza ake ena anali Afarisi. Ngakhale kuti anthu anali kunena zinthu zoipa zokhudza Stefano, iye sanaope. Analankhula molimba mtima ndipo anachitira bwino umboni za Yehova Mulungu ndi Yesu kwa oweruzawo.

Koma oweruzawo sanasangalale nazo. Anali kale kudziŵa zambiri zokhudza Yesu. Ndipo si kale kwambiri pamene iwo anakonza za kupha Yesu! Koma pambuyo pake Yehova anatenga Yesu ndi kupita nayenso kumwamba. Tsopano m’malo mosintha zochita zawo, oweruzawo akulimbana ndi ophunzira a Yesu.

Oweruzawo anagwira Stefano ndi kupita naye kunja kwa mudzi. Anamumenya ndi kumugwetsa pansi ndi kuyamba kumuponya miyala. Ndipo monga ukuonera pachithunzichi, Saulo anali pomwepo, anali kuonerera. Anali kuganiza kuti ndi chinthu chabwino kupha Stefano.

Ndi chifukwa chiyani Saulo akuganiza kuti kupha Stefano ndi chinthu chabwino?

Kodi ukudziŵa chifukwa chake Saulo anali kuganiza motero?— Pamoyo wake wonse Saulo anali Mfarisi, ndipo anali kukhulupirira kuti zimene Afarisi anali kuphunzitsa zinali zolondola. Iye anali kuona anthu amenewo kukhala zitsanzo zabwino, choncho anali kuwatengera.—Machitidwe 7:54-60.

Kodi Saulo anachita chiyani Stefano ataphedwa?— Eti anaganiza za kutha ophunzira onse a Yesu! Anachita kupita kunyumba zawo ndi kumawakoka, amuna ndi akazi omwe. Akatero anali kuwaika m’ndende. Ophunzira ambiri anachokako ku Yerusalemu, komabe iwo sanaleke kulalikira za Yesu.—Machitidwe 8:1-4.

Izi zinachititsa Saulo kudana kwambiri ndi ophunzira a Yesu. Choncho anapita kwa Mkulu wa Ansembe Kayafa ndi kukatenga chilolezo chakuti akagwire Akristu amene anali ku mudzi wa Damasiko. Saulo anafuna kukawatenga ndi kubwera nawo ku Yerusalemu monga akaidi kuti akawalange. Koma ali m’njira kupita ku Damasiko, panachitika zodabwitsa.

Kodi ndani akulankhula ndi Saulo, ndipo kodi Iye akutuma Saulo kukachita chiyani?

Kunawala kwambiri kuchokera kumwamba, ndipo panamveka mawu akuti: ‘Saulo, Saulo, kodi ukundizunziranji?’ Yesu anali kulankhula kuchokera kumwamba! Kuwalako kunali konyezimira kwambiri moti Saulo anachita khungu, ndipo anthu amene anali naye limodzi ndiwo anamutsogolera ku Damasiko.

Patatha masiku atatu Yesu anaoneka m’masomphenya kwa wophunzira wake wina ku Damasiko dzina lake Hananiya. Yesu anauza Hananiya kupita kwa Saulo kuti akamuchotse khungu m’maso ndi kukalankhula naye. Hananiya atalankhula naye, Saulo anakhulupirira choonadi chonena za Yesu. Maso ake anayambiranso kuona. Moyo wake wonse unasintha, ndipo anakhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu.—Machitidwe 9:1-22.

Kodi tsopano ukuona chifukwa chake Saulo anali kuchita zinthu zoipa?— Chinali chifukwa chakuti anamuphunzitsa zinthu zolakwika. Iye anali kutsatira anthu amene sanali okhulupirika kwa Mulungu. Ndipo anali m’gulu la anthu amene anali kuona maganizo a anthu kukhala ofunika kwambiri kuposa Mawu a Mulungu. Koma kodi ndi chifukwa chiyani Saulo anasintha moyo wake ndi kuyamba kuchita zinthu zabwino, ngakhale kuti Afarisi ena anapitiriza kulimbana ndi Mulungu?— Ndi chifukwa chakuti Saulo sanali kudana ndi choonadi. Ndiye pamene anamusonyeza zolondola, anali wokonzeka kutsatira zimenezo.

Kodi ukudziŵa kuti kenako Saulo anali kudziŵika kuti ndani?— Eya, anali kudziŵika kuti mtumwi Paulo, mtumwi wa Yesu. Ndipo mwina ungakumbukire kuti Paulo analemba mabuku a m’Baibulo ambiri kuposa wina aliyense.

Pali anthu ambiri okhala ngati Saulo amene angasinthe. Komatu si zapafupi chifukwa pali winawake amene akuyesetsa kukakamiza anthu kuchita zinthu zoipa. Kodi ukumudziŵa?— Yesu ananena za iye pamene anaonekera kwa Saulo panjira yopita ku Damasiko. Panjirapo Yesu analankhula ndi Saulo kuchokera kumwamba ndipo ananena kuti: ‘Ine ndikukutuma iwe kwa anthu kuti ukawatsegule maso awo, kuti atembenuke kuchoka mu mdima ndi kuloŵa mu kuunika, ndiponso kuchoka mu ulamuliro wa Satana ndi kupita kwa Mulungu.’—Machitidwe 26:17, 18.

Inde, ndi Satana Mdyerekezi amene akuyesa kukakamiza aliyense kuchita zinthu zoipa. Kodi iwe nthaŵi zina zimakuvuta kuchita zinthu zabwino?— Tonsefe zimativuta nthaŵi zina. Satana amachititsa kuti tizivutika. Koma palinso chifukwa china chimene zimativutira nthaŵi zambiri kuchita zabwino. Kodi ukuchidziŵa?— Ndi chifukwa chakuti tinabadwa ndi uchimo.

Nthaŵi zambiri timachita zinthu zoipa mosavuta kusiyana ndi kuchita zinthu zabwino chifukwa cha uchimo umenewu. Ndiyeno, kodi tifunika kuchita chiyani?— Eya, tiyenera kulimbikira kuti tichite zabwino. Tikamatero tingakhale otsimikiza kuti Yesu, yemwe amatikonda, adzatithandiza.

Pamene Yesu anali padziko lapansi pano, anali kukonda anthu amene kale anali kuchita zinthu zoipa koma ndi kusintha. Iye anali kudziŵa kuti sikunali kwapafupi kuti iwo asinthe. Mwachitsanzo, panali akazi amene anali kugonana ndi amuna ambirimbiri. Zimenezi zinali zoipa kwambiri. Akazi ameneŵa Baibulo limawatchula kuti akazi achiwerewere, kapena kuti mahule.

Ndi chifukwa chiyani Yesu anakhululukira mkazi uyu amene anachita zinthu zoipa?

Tsiku lina, mkazi woteroyo anamva za Yesu, ndipo iye anapita kumene kunali Yesu kunyumba ya Mfarisi. Mkaziyu anathira mafuta mapazi a Yesu ndipo anagwiritsa ntchito tsitsi lake kupukuta misozi yake pa mapazi a Yesuwo. Anali wachisoni kwambiri ndi machimo ake, choncho Yesu anamukhululukira. Koma Mfarisiyo anaganiza kuti mkaziyo sanayenera kukhululukidwa.—Luka 7:36-50.

Kodi ukudziŵa zimene Yesu anauza Afarisi enanso?— Anawauza kuti: ‘Akazi achiwerewere akutsogola kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu kukusiyani inu.’ (Mateyu 21:31) Yesu ananena zimenezi chifukwa chakuti akazi achiwerewere anamukhulupirira ndipo anasintha njira zawo zoipa. Koma Afarisi anapitiriza kuchitira ophunzira a Yesu zinthu zoipa.

Ndiye Baibulo likaonetsa kuti zimene timachita ndi zoipa, tizikhala ofunitsitsa kusintha. Ndipo tikadziŵa zimene Yehova amafuna kuti tizichita, tizikhala okonzeka kuchita zimenezo. Tikatero Yehova adzakondwera nafe ndipo adzatipatsa moyo wosatha.

Tiye tiŵerengere limodzi malemba aŵa kuti atithandize kupewa kuchita zinthu zoipa: Salmo 119:9-11; Miyambo 3:5-7; ndi Miyambo 12:15.