Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 19

Kodi Ndi Bwino Kuchita Ndewu?

Kodi Ndi Bwino Kuchita Ndewu?

KODI ukudziŵapo mnyamata aliyense kapena mtsikana aliyense amene amadzitukumula ndi kuopseza anzake?— Kodi umasangalala ukakhala nawo pamodzi? Kapena kodi ungakonde kukhala limodzi ndi munthu wokoma mtima ndi wokonda zamtendere?— Mphunzitsi Waluso ananena kuti: ‘Osangalala ndi anthu amtendere chifukwa adzatchedwa kuti ana a Mulungu.’—Mateyu 5:9.

Komabe nthaŵi zina anthu ena amachita zinthu zimene zimatikwiyitsa. Izi ndi zoona, si choncho kodi?— Ndiyeno ife tingaganize kuti ndi bwino kuwabwezera. Tsiku lina, zoterezi zinachitikira ophunzira a Yesu pamene anali paulendo wopita ku Yerusalemu ndi Yesu. Taleka ndikuuze mmene zinalili.

Ali panjira m’kati mwa ulendowo, Yesu anatuma ophunzira ake angapo kupita ku mudzi wa Asamariya kukapeza malo ogona. Koma anthu akumeneko sanafune kuti iwo agone m’mudzi mwawo, chifukwa chakuti Asamariyawo anali a chipembedzo china. Ndipo iwo sanali kusangalala ndi munthu aliyense amene anali kupita kukalambira ku mudzi wa Yerusalemu.

Kodi Yakobo ndi Yohane anafuna kuchita chiyani kuti abwezere Asamariya?

Kodi ukanakhala iweyo ukanachita chiyani? Kodi ukanakwiya? Kodi ukanaganiza zowabwezera?— Yakobo ndi Yohane, ophunzira a Yesu, anafuna kuchita zimenezo. Anauza Yesu kuti: ‘Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba kuti uwatenthe?’ Ndi pake kuti Yesu anawatcha kuti Ana a Bingu! Koma Yesu anawauza kuti si bwino kuchitira anthu ena zoterozo.—Luka 9:51-56; Marko 3:17.

Anthu ena akhozadi kutichitira nkhanza nthaŵi zina. Ana ena sangafune kuti tiziseŵera nawo limodzi. Mwina mpaka akhoza kukuuza kuti: “Zipita, sitikukufuna.” Zoterezi zikhoza kutikwiyitsa kwambiri, si choncho? Tingafune kungochita zinazake kuti tiwabwezere. Koma kodi tiyenera kubwezera?—

Tatenga Baibulo lako. Tiye tipeze Miyambo chaputala 24, vesi 29. Pamenepa pamanena kuti: ‘Usanene, Ndidzamuchitira zomwezo anandichitira ine; ndidzabwezera munthuyo monga mwa machitidwe ake.’

Kodi ukuganiza kuti mawu ameneŵa akutanthauza chiyani?— Akutanthauza kuti sitiyenera kubwezera. Sitiyenera kuchitira munthu nkhanza chifukwa chakuti iyeyo anatichitira nkhanza. Nanga bwanji ngati winawake akukuyamba dala kuti mumenyane? Angakuitane mayina amene susangalala nawo pofuna kuti ukwiye. Mwina angakuseke ndi kunena kuti ndiwe wamantha. Bwanji atanena kuti ndiwe wopanda mphamvu. Kodi uyenera kuchita chiyani? Kodi uyenera kukalipa mpaka kuchita ndewu?—

Tiye tionenso zimene Baibulo limanena. Tsegula Mateyu chaputala 5, vesi 39. Yesu pa vesili ananena kuti: “Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umutembenuzire linanso.” Kodi ukuganiza kuti Yesu anali kutanthauza chiyani? Kodi anali kutanthauza kuti munthu wina akakumenya nkhonya mbali imodzi ya mutu wako, umuuze kuti akumenyenso mbali inayi?—

Ayi, si zimene Yesu anali kutanthauza. Kukupanda mbama patsaya ndi kosiyana ndi kukumenya nkhonya. Mbama imangokhala ngati wakukankha. Munthu angatiwombe mbama pofuna kuyambitsa ndewu. Amafuna kuti ifeyo tikalipe. Ndiyeno ife tikakalipa ndi kumukankhanso iyeyo, kodi chimachitika ndi chiyani?— Basitu ndewu imayambika.

Koma Yesu sanafune kuti ophunzira ake azichita ndewu. Ndiye ndi chifukwa chake ananena kuti ngati munthu watiwomba mbama, sitiyenera kumubwezera. Sitiyenera kukalipa ndi kuchita ndewu. Tikakalipa timaonetsa kuti sitikusiyana ndi amene anayambitsa ndewuyo.

Ngati wina ayamba kukuvutitsa, kodi ukuganiza kuti chinthu chanzeru kuchita ndi chiyani?— Chinthu chanzeru ndi kuchokapo. Iye angakukankhebe kangapo. Koma zikhoza kuthera pomwepo. Ukachokapo sindiye kuti ndiwe wopanda mphamvu. Zimangosonyeza kuti ndiwe wolimba pa kuchita chabwino.

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu wina akutiyamba dala kuti timenyane?

Koma bwanji utachita ndewu ndiyeno iweyo ndi kuwina? Ukuganiza kuti chingachitike ndi chiyani?— Amene unamumenya uja akhoza kukatenga anzake ndi kubwera nawo. Akhoza kukupweteka ndi ndodo kapena mpeni. Kodi ukuona pamenepa chifukwa chake Yesu sanafune kuti tizichita ndewu?—

Kodi tikaona anthu ena akuchita ndewu tizichita chiyani? Kodi tizithandiza mmodzi wa anthuwo?— Baibulo limatiuza chinthu chabwino kuchita. Tsegula Miyambo chaputala 26, vesi 17. Vesili likuti: “Wakungopita ndi kuvutika ndi ndewu yosakhala yake akunga wogwira makutu a galu.”

Kodi kuloŵerera ndewu ya ena ndi kofanana motani ndi kugwira makutu a galu? Akhoza kukuluma, ndiye osayesera dala kumugwira!

Kodi chingachitike ndi chiyani ngati utagwira makutu a galu? Galuyo akhoza kumva kuŵaŵa, ndipo angafune kukuluma, si choncho? Ndiye galuyo angayambe kulimbalimba kuti umusiye. Pamene akulimbalimba kwambiri iwenso ungafunike kumugwira makutuwo kwambiri, ndipo galuyo angaluse kwambiri. Ngati utamusiya, mwina akhoza kukuluma kwambiri. Koma kodi ungangokhala pomwepo ndi kumugwira makutu mpaka kalekale?—

Eya, tikhoza kukhala m’mavuto otereŵa ngati titaloŵerera ndewu ya anthu ena. Sitingadziŵe kuti anayambitsa ndewuyo ndani kapenanso kuti akumenyana chifukwa chiyani. Zingatheke kuti wina akumenyedwa mwina chifukwa chakuti anabera mnzakeyo. Ngati ife timuthandiza ndiye kuti tikuthandiza mbala. Ndiye zingakhale bwino kutero?

Tsono, kodi uyenera kuchita chiyani ukaona ena akuchita ndewu?— Ngati ndi kusukulu, ukhoza kuthamanga ndi kukauza aphunzitsi. Ndipo ngati si kusukulu, ukhoza kuitana makolo ako kapena munthu wina wamkulu. Inde, tizikhala amtendere ngakhale pamene anthu ena akufuna kuchita ndewu.

Kodi uyenera kuchita chiyani ukaona ena akuchita ndewu?

Ophunzira enieni a Yesu amayesetsa kupewa ndewu. Mwa kuchita zimenezi timasonyeza kuti ndife olimba pa zabwino. Baibulo limanena kuti wophunzira wa Yesu ‘sayenera kuchita ndewu, komatu akhale wodekha kwa onse.’—2 Timoteo 2:24.

Tsopano tiye tione malangizo enanso abwino amene adzatithandiza kupewa ndewu: Aroma 12:17-21 ndi 1 Petro 3:10, 11.