Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 28

Kudziwa Amene Uyenera Kumumvera

Kudziwa Amene Uyenera Kumumvera

NTHAŴI zina zimavuta kudziŵa amene tiyenera kumumvera. Amayi ako kapena atate ako angakuuze kuchita zinazake. Koma aphunzitsi kusukulu kapena wapolisi angakuuze kuchita zina zosiyana ndi zimenezo. Kodi zimenezi zikachitika, udzamvera ndani?—

Kumayambiriro kwa buku lino, m’Mutu 7, tinaŵerenga m’Baibulo pa Aefeso 6:1-3. Pamenepo pamanena kuti ana azimvera makolo awo. ‘Mverani akukubalani mwa Ambuye,’ limatero lembalo. Kodi ukudziŵa kuti mawuwo ‘mwa Ambuye’ akutanthauza chiyani?— Makolo amene ali mwa Ambuye amaphunzitsa ana awo kumvera malamulo a Mulungu.

Koma anthu ena achikulire sakhulupirira Yehova. Ndiye bwanji ngati wachikulire wina anena kuti ndi bwino kuonera polemba mayeso kapena kutenga chinachake mu sitolo popanda kulipira? Kodi ndiye kuti ndi bwino mwana kuonera kapena kuba?—

Ndiganiza ukukumbukira kuti Mfumu Nebukadinezara tsiku lina inalamula kuti munthu aliyense agwadire fano lagolidi limene iyo inapanga. Koma Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anakana kugwadira fanolo. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Chinali chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti anthu azilambira Yehova yekha.—Eksodo 20:3; Mateyu 4:10.

Kodi Petro akuti chiyani kwa Kayafa?

Yesu atamwalira, atumwi ake anatengedwa kupita nawo ku Sanihedirini, khoti lalikulu lachipembedzo la Ayuda. Mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa, anati: ‘Tinakulamulirani chilamulire, musaphunzitse kutchula dzina la Yesu; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu.’ Nanga ndi chifukwa chiyani atumwiwo sanamvere Sanihedirini?— Petro, polankhulira atumwi onse, anayankha Kayafa kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:27-29.

Panthaŵi imeneyo, atsogoleri achipembedzo cha Ayuda anali ndi mphamvu kwambiri. Komabe boma la Roma ndilo linali kulamulira dziko lawo. Mtsogoleri wa bomalo anali kutchedwa Kaisara. Ngakhale kuti Ayuda sanali kufuna kuti Kaisara aziwalamulira, boma la Roma linali kuwachitira zinthu zabwino zambiri. Ndiponso masiku ano maboma amachitira anthu awo zinthu zabwino. Kodi ukudziŵa zina za zimene maboma amachita?—

Boma limapanga misewu yoyendamo ndi kulipira apolisi ndi ozimitsa moto kuti atiteteze. Limamanganso sukulu za ana ndi kupereka chithandizo cha mankhwala kwa okalamba. Boma limawononga ndalama zambiri kuti lichite zinthu zimenezi. Kodi ukudziŵa kumene boma limapeza ndalamazo?— Ndi kwa anthu. Ndalama zimene anthu amalipira kuboma zimatchedwa msonkho.

Nthaŵi imene Mphunzitsi Waluso anali padziko lapansi, Ayuda ambiri sanafune kupereka msonkho ku boma la Roma. Ndiye tsiku lina ansembe anatuma anthu ena kuti akafunse Yesu za nkhaniyi. Chimene anali kufuna ndi kumupeza chifukwa. Funso lawo linali lakuti, ‘Kodi tizilipira msonkho kwa Kaisara kapena tisamalipire?’ Funsoli analifunsa mochenjera kwambiri. Yesu akanayankha kuti, ‘Inde, muzilipira misonkho,’ Ayuda ambiri sakanakondwera ndi zimenezo. Koma Yesu sakananenanso kuti, ‘Iyayi, musamalipire misonkho.’ Akanatero akanalakwa.

Ndiye mmene zinalilimu, kodi Yesu anachita chiyani? Eya, iye anati: ‘Tandionetsani ndalamayo.’ Atamupatsa, Yesu anawafunsa kuti: ‘Kodi chithunzi chili pa ndalamayi ndi dzinali, ndi za ndani?’ Anthuwo anati: ‘Ndi za Kaisara.’ Ndiye Yesu anati: “Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”—Luka 20:19-26.

Kodi Yesu anayankha bwanji funso limene anthu aŵa anamufunsa mochenjera?

Atatero, munthu wina aliyense sanaone cholakwa ndi yankho limenelo. Ngati Kaisara amachitira anthu zinthu zabwino, ndiye ndi bwino kugwiritsa ntchito ndalama zimene iye wapanga kumulipira chifukwa cha zinthu zabwino zimene amachitazo. Pamenepa, Yesu anasonyeza kuti ndi bwino kulipira misonkho ku boma chifukwa cha zimene limatichitira.

Tsono, mwina iwe sunafike msinkhu wolipira msonkho. Koma pali chinachake chimene uyenera kuchita ku boma. Kodi ukuchidziŵa?— Uyenera kumvera malamulo a boma. Baibulo limanena kuti: ‘Mverani maulamuliro aakulu.’ Maulamuliro ameneŵa ndi anthu aja amene ali ndi udindo m’boma. Choncho Mulungu ndiye amatiuza kuti tizimvera malamulo a boma.—Aroma 13:1, 2.

Mwina pangakhale lamulo loletsa kutaya zinyalala paliponse. Kodi uyenera kumvera lamulo limenelo?— Inde, Mulungu akufuna kuti uzimvera. Kodi uyeneranso kumvera apolisi?— Boma limalipira apolisi kuti iwo aziteteza anthu. Kumvera apolisiwo ndi chimodzimodzi kumvera boma.

Ndiye ngati pofuna kudumpha msewu, wapolisi anena kuti “Yembekezani!” kodi uyenera kuchita chiyani?— Ngati ena akungodumphabe msewuwo, kodi iwenso uyenera kudumpha?— Uyenera kuyembekeza, ngakhale ngati ndiwe wekha amene uyembekeze. Mulungu amatiuza kuti tizimvera.

Mwina kudera la kuno kwathu kungakhale mavuto, ndipo wapolisi anganene kuti: “Osayenda mumsewu. Musatuluke panja.” Koma mwina iwe ungamve anthu akukuwa ndipo ungafune kudziŵa chimene chikuchitika. Kodi ndi bwino kutuluka panja kuti ukaone chimene chikuchitika?— Kodi ukatero ndiye kuti ukumvera “maulamuliro aakulu”?—

M’madera ambiri, boma limamanganso sukulu, ndi kulipira aphunzitsi. Ndiye ukuganiza bwanji, kodi Mulungu amafuna kuti uzimveranso aphunzitsi?— Ukaganizira, uona kuti boma limalipira aphunzitsi kuti aziphunzitsa, ngati mmene limalipirira apolisi kuti aziteteza anthu. Choncho kumvera apolisi kapena aphunzitsi ndi kumvera boma.

Ndi chifukwa chiyani tiyenera kumvera wapolisi?

Koma bwanji ngati aphunzitsi akuuza kuti ulambire fano linalake? Kodi udzachita chiyani?— Ahebri atatu aja sanagwadire fano, ngakhale pamene Mfumu Nebukadinezara inawauza kutero. Kodi ukukumbukira chifukwa chake?— Iwo anafuna kumvera Mulungu.

Munthu wina wolemba mbiri, dzina lake Will Durant, analemba za Akristu oyambirira. Ananena kuti ‘kukhulupirika kwawo makamaka sikunali kwa Kaisara’ ayi. M’malo mwake, iwo anali okhulupirika kwa Yehova! Choncho uzikumbukira kuti Mulungu ndiye woyamba pamoyo wathu.

Timamvera boma chifukwa chakuti ndi zimene Mulungu amafuna. Koma ngati bomalo litiuza kuchita zimene Mulungu amaletsa, kodi tiyenera kunena chiyani?— Tiyenera kunena zimene atumwi anauza mkulu wa ansembe uja kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.

Baibulo limatiphunzitsa kulemekeza malamulo. Ŵerengani zimene zili pa Mateyu 5:41; Tito 3:1; ndi 1 Petro 2:12-14.