Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 37

Kukumbukira Yehova ndi Mwana Wake

Kukumbukira Yehova ndi Mwana Wake

TAYEREKEZA kuti winawake wakupatsa mphatso yabwino kwambiri. Kodi ungachite chiyani?— Kodi unganene kuti zikomo, basi kenako ndi kuiwalako za munthuyo? Kapena kodi ungamakumbukire munthuyo limodzi ndi zimene anakuchitirazo?—

Yehova Mulungu anatipatsa mphatso yabwino kwambiri. Anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti atifere. Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yesu anafunika kutifera?— Imeneyi ndi nkhani yofunika kuidziŵa bwino kwambiri.

Ungakumbukire kuti mu Mutu 23 tinaphunzira kuti Adamu anachimwa ataswa lamulo labwino kwambiri la Mulungu. Ife tonse tinatengera uchimo kwa Adamuyo, atate wathu. Ndiye ukaganiza, kodi tikufunika chiyani?— Tinganene kuti tikufunika atate wina watsopano, amene anali ndi moyo wangwiro padziko lapansi. Kodi ungati ndani amene angakhale atate ameneyo?— Ndi Yesu.

Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti iye adzakhale atate wathu m’malo mwa Adamu. Baibulo limanena kuti: “‘Munthu woyamba uja, Adamu, anasanduka munthu wamoyo.’ Koma Adamu wotsiriza, anasanduka mzimu wopatsa moyo.” Kodi Adamu woyamba anali ndani?— Anali munthu uja amene Mulungu analenga kuchokera ku dothi. Nanga Adamu wachiŵiri ndani?— Ndi Yesu. Baibulo limaonetsa mfundo imeneyi pamene limati: ‘Adamu woyamba uja anali wochokera pansi pano, ndipo anali dothi. Koma Kristu, Adamu wachiŵiri uja, anali wochokera kumwamba.’1 Akorinto 15:45, 47, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono; Genesis 2:7.

Popeza kuti Mulungu anatenga moyo wa Yesu kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa mkazi uja Mariya, Yesu sanatengere uchimo uliwonse kuchokera kwa Adamu. Ndi chifukwa chake Yesu anali munthu wangwiro. (Luka 1:30-35) Ndi chifukwa chakenso Yesu atabadwa mngelo anauza abusa kuti: ‘Wakubadwirani inu lero Mpulumutsi.’ (Luka 2:11) Koma kuti akhale Mpulumutsi wathu, kodi Yesu wakhandayo anafunika kuti ayambe watani?— Anafunika kuti akule ndi kukhala munthu wamkulu, monga mmene Adamu analili. Pokhapo ndi pamene Yesu akanakhala “Adamu wachiŵiri.”

Yesu, Mpulumutsi wathu, adzakhalanso ‘Atate wathu Wosatha.’ Baibulo limamutchula tero. (Yesaya 9:6, 7) Inde, Yesu wangwiroyo angakhale atate wathu m’malo mwa Adamu, yemwe atachimwa anakhala wopanda ungwiro. Motero ife tingasankhe kuti “Adamu wachiŵiri” akhale atate wathu. Ndi zoona kuti Yesuyo ndi Mwana wa Yehova Mulungu.

Kodi Adamu ndi Yesu anali ofanana motani, nanga ndi chifukwa chiyani anafunika kufanana?

Mwa kudziŵa bwino Yesu, tingamulandire kukhala Mpulumutsi wathu. Kodi ukukumbukira kuti tifunika kupulumutsidwa ku chiyani?— Eya, tifunika kupulumutsidwa ku uchimo ndi imfa zimene tinatengera kwa Adamu. Moyo wangwiro umene Yesu ali munthu wamkulu anapereka nsembe chifukwa cha ife umatchedwa dipo. Yehova anatipatsa dipo kuti machimo athu athe kuchotsedwa.—Mateyu 20:28; Aroma 5:8; 6:23.

Ndithudi sitifuna kuiwala zimene Mulungu ndi Mwana wake atichitira, si choncho?— Yesu anasonyeza otsatira ake njira yapadera yomwe ingatithandize kukumbukira zimene anachita. Tiye tikambirane zimenezi.

Ganizira kuti uli m’chipinda chosanja cha nyumba ina ku Yerusalemu. Ndi nthaŵi yausiku. Yesu ndi atumwi ake ali pathebulo. Pathebulopo pali nyama yowotcha ya nkhosa, mkate, ndi vinyo wofiira. Iwo akudya chakudya chapadera. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?—

Chakudya chimenechi chinali kuwakumbutsa zimene Yehova anachita zaka mahandiredi ambiri kalelo pamene anthu ake Aisrayeli anali akapolo ku Igupto. Panthaŵi imeneyo Yehova anauza anthu ake kuti: ‘Muphe mwana wa nkhosa pabanja lililonse, ndipo magazi ake mupake pa maferemu a zitseko za nyumba zanu.’ Kenako anati: ‘Loŵani m’nyumba zanu mukadye nyama ya nkhosayo.’

Kodi magazi a mwana wa nkhosa anateteza Aisrayeli motani?

Aisrayeli anachita zimenezi. Ndipo usiku womwewo, mngelo wa Mulungu anadutsa m’dziko la Igupto. Mngeloyu anapha ana oyamba kubadwa m’nyumba zambiri. Koma mngeloyu amati akaona magazi a nkhosa aja pakhomo, nyumba imeneyo anali kuipitirira. Palibe mwana aliyense amene anaphedwa m’nyumba zoterozo. Farao, yemwe anali mfumu ya ku Igupto, anachita mantha kwambiri ndi zimene mngelo wa Yehova anachita. Choncho Farao anauza Aisrayeli kuti: ‘Muli aufulu kupita. Chokani mu Igupto!’ Atawauza zimenezi iwo anatenga katundu wawo ndi kumangirira pa ngamila zawo ndi abulu awo ndi kumapita.

Yehova sanafune kuti anthu ake aiwale mmene anawalanditsira. Ndiye ananena kuti: ‘Kamodzi pachaka muzidya chakudya chonga chimene mwadya usiku uno.’ Chakudya chapadera chimenechi anachitcha Paskha. Usiku umenewo mngelo wa Mulungu “anapitirira” nyumba zomwe zinali ndi magazi.—Eksodo 12:1-13, 24-27, 31.

Yesu ndi atumwi ake anali kuganizira zimenezi pakudya Paskha uja. Atatha Paskhayo, Yesu anachita chinachake chofunika kwambiri. Komabe asanachite zimenezo anayamba watulutsa mtumwi wosakhulupirika uja Yudasi. Ndiyeno Yesu anatenga mkate umodzi pa mikate imene inatsala. Atapemphera, anaunyema ndi kupatsa ophunzira ake, nati: “Tengani, idyani.” Ndiye anawauza kuti: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene ndidzapereka pokuferani inu.’

Kenako Yesu anatenga kapu momwe munali vinyo wofiira. Ataperekanso pemphero lothokoza, anawapatsa kuti amwe ndipo anati: ‘Imwani nonsenu.’ Anawauzanso kuti: ‘Vinyo ameneyu akuimira magazi anga. Posachedwapa ndikhetsa magazi anga kuti ndikumasuleni ku machimo anu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.’—Mateyu 26:26-28; 1 Akorinto 11:23-26.

Kodi magazi a Yesu, omwe Yesuyo anawayerekeza ndi vinyo, angatichitire chiyani?

Waona kuti Yesu ananena kuti ophunzira ake ayenera kumachita zimenezi kuti azimukumbukira?— Kuyambira pamenepo iwo sanafunike kudyanso Paskha. M’malo mwake, kamodzi chaka chilichonse iwo anayenera kudya chakudya chapadera chimenechi pokumbukira Yesu ndi imfa yake. Chakudya chimenechi chimatchedwa Mgonero wa Ambuye. Masiku ano nthaŵi zambiri timachitchula kuti Chikumbutso. Ukudziŵa chifukwa chake?— Ndi chifukwa chakuti chimatikumbutsa zimene Yesu ndi Atate ake, Yehova Mulungu, anatichitira.

Tikaona mkate tiyenera kuganiza za thupi la Yesu. Iye anali wofunitsitsa kupereka thupi limenelo kuti ife tidzakhale ndi moyo wosatha. Nanga bwanji vinyo wofiira?— Uyenera kutikumbutsa kufunika kwa magazi a Yesu. Ndi ofunika kwambiri kuposa magazi a nkhosa ya pa Paskha ku Igupto. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Baibulo limanena kuti machimo athu akhoza kukhululukidwa chifukwa cha magazi a Yesu. Ndipo pamene machimo athu onse adzachotsedwa, sitidzadwalanso, kaya kukalamba, ngakhale kufa. Tikafika pa Chikumbutso tiziganizira zimenezi.

Ukuganiza bwanji, kodi aliyense ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso?— Eya, Yesu anauza amene amadya ndi kumwa pa Chikumbutso kuti: ‘Mudzachita nawo ufumu mu ufumu wanga ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu kumwamba pamodzi ndi ine.’ (Luka 22:19, 20, 29, 30) Izi zinatanthauza kuti iwo akapita kumwamba kukakhala mafumu limodzi ndi Yesu. Ndiye ndi okhawo amene akuyembekeza kukalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo.

Komabe ngakhale amene sadya mkate kapena kumwa vinyo ayenera kufika pa Chikumbutso. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Ndi chifukwa chakuti Yesu anaferanso ifeyo. Tikapita ku Chikumbutso timasonyeza kuti sitinaiwale zimenezo. Timakumbukira mphatso yabwino kwambiri imene Mulungu anatipatsa.

Malemba ena ndi aŵa amene amasonyeza kuti dipo la Yesu ndi lofunika: 1 Akorinto 5:7; Aefeso 1:7; 1 Timoteo 2:5, 6; ndi 1 Petro 1:18, 19.